Bokosi la Mafunso
◼ Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwaletsedwa kulalikira?
Nthawi zina apolisi amauza ofalitsa amene awapeza akulalikira kuti akuphwanya malamulo ndipo amawaletsa kulalikira. Ngati mwauzidwa kuchita zimenezi, nthawi yomweyo siyani kulalikirako ndi kuchoka m’gawolo mwaulemu. (Mat. 5:41; Afil. 4:5) Simuyenera kuyesa kuthetsa nkhaniyo panokha mwa kuyamba kukambirana nawo za malamulo amene amatipatsa ufulu wolalikira. Ngati n’kotheka, yesani kukopera nambala ya baji ya wapolisiyo ndiponso nambala ya malo amene iye amayang’anira. Kenako, dziwitsani mwamsanga akulu, ndipo iwo adzadziwitsa ofesi ya nthambi zimene zachitikazo. Mofananamo, ngati woyang’anira nyumba zimene pamakhala anthu ambiri kapena womuimira akuuzani kuti musalalikire nyumba zimenezi, muyenera kuwamvera ndiponso kudziwitsa akulu. Kuchita zinthu mofatsa ndiponso modzichepetsa tikakumana ndi anthu amene ali ndi ulamuliro kungathandize kupewa mavuto ena.—Miy. 15:1; Aroma 12:18.