Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda December 1
“Panyengo ino ya Khirisimasi, ambiri amajambula zinthuzi zosonyeza anzeru akum’mawa atatu akupereka mphatso kwa Yesu potengera nkhani ya m’Baibulo iyi. [Werengani Mateyo 2:1, 11.] Kodi mwaona kuti zimene anthuwa amajambula ndi zosiyana ndi zimene Baibulo limanena? [Yembekezani ayankhe.] Nkhaniyi ikufotokoza zimene zinachitikadi.” Aonetseni nkhani imene ili patsamba 31.
Galamukani! December
“Ndikufuna kumva maganizo anu pa zimene Yesu ananena palemba ili. [Werengani Mateyo 5:3.] Popeza kuti pali zipembedzo zambirimbiri, kodi mukuganiza kuti zipembedzo zonse zingatithandize kuthetsa njala yathu yauzimu? [Yembekezani ayankhe.] Nkhaniyi ili ndi mfundo za Baibulo zotithandiza kudziwa mmene tingathetsere njala yathu yauzimu. Aonetseni nkhani imene ili patsamba 12.
Nsanja ya Olonda January 1
“Zipembedzo zosiyanasiyana zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya kumwa mowa. Kodi inuyo mukuganiza kuti Mulungu amawaona bwanji anthu amene amamwa mowa? [Yembekezani ayankhe.] Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti nthawi ina Yesu anasintha madzi kukhala vinyo, limanenanso izi. [Werengani Miyambo 23:20a.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limanenadi pa nkhani ya mowa.”
Galamukani! January
“M’nthawi yovuta ino, anthu ambiri amapanikizika kwambiri ndi ntchito. Kodi inunso mumaona kuti mumapanikizika? [Yembekezani ayankhe.] Taonani malangizo othandiza awa. [Werengani Mlaliki 4:6.] Magazini iyi ikufotokoza zimene tingachite kuti tizikhala ndi nthawi yogwira ntchito, yocheza ndi banja lathu komanso yopuma. Ilinso ndi malangizo othandiza anthu amene akufunafuna ntchito.”