Kodi Ndikuchita Zokwanira?
1. Kodi Mkhristu wokhulupirika angamadere nkhawa za chiyani?
1 Kodi munayamba mwadzifunsapo funso limeneli? Mwina mumakhumudwa kuti masiku ano, chifukwa cha ukalamba, matenda kapena kusamalira banja, simukuchita zambiri mu utumiki monga mmene munkachitira kale. Mlongo wina, yemwe ali ndi ana atatu, anafotokoza kuti nthawi zina amadziimba mlandu kuti sakuchita zokwanira mu utumiki chifukwa amathera nthawi yambiri komanso mphamvu yake pa kusamalira banja lake. N’chiyani chingatithandize kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhaniyi?
2. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?
2 Zimene Yehova Amafuna Kuti Tizichita: Mosakayikira, tonsefe timafuna kuchita zambiri mu utumiki. Koma kawirikawiri zimene timafuna kuchita zimasiyana kwambiri ndi zimene tingathe kuchita. Ngati timalakalaka kuchita zambiri, ndiye kuti tili ndi chidwi ndi utumiki. Tizikumbukira kuti Yehova amadziwa mavuto athu ndipo amadziwa zimene tingathe kuchita ndi zimene sitingathe. (Sal. 103:13, 14) Kodi amafuna kuti tizichita chiyani? Amafuna kuti tizimutumikira ndi moyo wathu wonse, kapena kuti tizichita zonse zimene tingathe.—Akol. 3:23.
3. Kodi tingadziwe bwanji ngati tikuchita zonse zimene tingathe mu utumiki?
3 Kodi tingadziwe bwanji kuti tikuchita zimene tingathe? Tingapemphe Yehova kutithandiza kuona zimene tingathedi kuchita. (Sal. 26:2) Komanso ngati tili ndi mnzathu wokhulupirika amene ndi Mkhristu wokhwima mwauzimu, amenenso amatidziwa bwino, ndipo sangaope kutiuza zenizeni, tingamupemphe kuti atithandize kuona ngati tikuchitadi zonse zimene tingathe. (Miy. 27:9) Kumbukirani kuti zinthu zimasintha pa moyo, choncho m’pofunika kuti nthawi ndi nthawi tiziona ngati pali zimene tingachite kuti tiwonjezere utumiki wathu.—Aef. 5:10.
4. Kodi tizimva bwanji tikamakumbutsidwa mfundo za m’Baibulo zokhudza utumiki?
4 Kodi Tizimva Bwanji Tikamakumbutsidwa za Utumiki?: Pa mpikisano wothamanga, nthawi zambiri anthu oonerera amachemerera othamangawo n’cholinga choti awalimbikitse kumaliza bwino mpikisanowo osati kuwafooketsa. Mofanana ndi zimenezi, pa misonkhano yathu kapena m’mabuku athu timalimbikitsidwa komanso kukumbutsidwa kudzera m’Baibulo kuti ‘tizilalikira mawu mwachangu.’ Mawu amenewa satanthauza kuti sitikuchita zokwanira ayi, koma amanenedwa kuti atipatse mphamvu. (2 Tim. 4:2) Tisamakayikire kuti tikapitiriza kuchita zonse zimene tingathe, Yehova adzakumbukira ‘chikondi chathu ndi ntchito zathu.’—Aheb. 6:10.