Mukhoza Kukwanitsa Kulalikira Mwamwayi
1. (a) Kodi munthu amachita motani ulaliki wamwamwayi? (b) Kodi ndi anthu angati pano amene tinamva koyamba za choonadi munthu wina atatilalikira mwamwayi?
1 Kodi ndi anthu angati mumpingo mwanu amene anamva koyamba za choonadi chifukwa cha ulaliki wamwamwayi? Mukhoza kudabwa kudziwa kuti ndi anthu ambiri. Pa ulaliki wamwamwayi, munthu amalalikira kwa anthu amene amakumana nawo pochita zinthu za tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo munthu akhoza kulalikira mwamwayi akakhala pa ulendo, akapita kukacheza ndi achibale kapena anthu oyandikana nawo nyumba, pogula zinthu kumsika, akakhala kusukulu, kuntchito, ndi malo ena. Pa gulu linalake la ofalitsa obatizidwa okwana 200, panapezeka kuti anthu 80 anamva koyamba za choonadi chifukwa cha ulaliki wamwamwayi. Choncho tingathe kuona kuti ulaliki wamwamwayi ndi wothandiza kwambiri.
2. Kodi m’Baibulo muli zitsanzo zotani za ulaliki wamwamwayi?
2 Yesu ndiponso Akhristu oyambirira nthawi zambiri ankalalikira mwamwayi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yesu akudutsa mumzinda wa Samariya, analalikira mwamwayi kwa mkazi amene ankatunga madzi pachitsime cha Yakobo. (Yoh. 4:6-26) Filipo analalikira mwamwayi kwa nduna ya ku Itopiya imene inkawerenga buku la Yesaya, poifunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” (Mac. 8:26-38) Paulo atamangidwa ku Filipi, analalikira kwa woyang’anira ndende. (Mac. 16:23-34) Patapita nthawi, Paulo anamangidwanso ndipo anauzidwa kuti asamachoke panyumba. Anthu “onse obwera kudzamuona anali kuwalandira ndi manja awiri. Anali kuwalalikira za ufumu wa Mulungu, ndi kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.” (Mac. 28:30, 31) Inunso mukhoza kukwanitsa kulalikira mwamwayi, ngakhale mutakhala munthu wamanyazi. Kodi mungachite bwanji zimenezi?
3. Kodi n’chiyani chingatithandize ngati timavutika kulankhula ndi anthu?
3 Kodi Mungayambire Pati? Ambirife timavutika kuyamba kulankhulana ndi anthu amene sitikuwadziwa. Timavutikanso kuyamba kukambirana nkhani yokhudza choonadi ngakhale kwa anthu amene tikudziwana nawo. Komabe kuti zisamativute, tizisinkhasinkha za ubwino wa Yehova ndi chuma chauzimu chimene watipatsa. Komanso tizimvera chisoni anthu a m’dzikoli chifukwa chakuti akukumana ndi mavuto aakulu ndipo alibe chiyembekezo chilichonse. (Yona 4:11; Sal. 40:5; Mat. 13:52) Tikhoza kupempheranso kwa Yehova kuti atithandize ‘kulimba mtima.’ (1 Ates. 2:2) Wophunzira wina wa sukulu ya Gileadi anati: “Nthawi zambiri ndimaona kuti kupemphera kumandithandiza ndikamavutika kulankhula ndi anthu.” Ngati mukuopa kulankhula, muzipemphera chamumtima mwachidule.—Neh. 2:4.
4. Kodi tingachite chiyani tisanayambe kulalikira, ndipo zimenezi zingatithandize bwanji?
4 Ulaliki wamwamwayi suchita kufuna kuti tikhale ndi mawu oyamba apadera kapena lemba loyambira kukambirana kwathu. Nthawi zina ndi bwino kuyamba kucheza kaye ndi munthuyo m’malo mongofikira kumulalikira. Ofalitsa ambiri aona kuti kuchita zimenezi kumawathandiza kuti alimbe mtima n’kuyamba kukambirana uthenga wabwino ndi munthu. Ngati munthuyo sakufuna kukambirana nanu, musamukakamize. Ingosiyani kuchezako.
5. N’chiyani chinathandiza mlongo wina wamanyazi kuti azikwanitsa kulalikira mwamwayi?
5 Mlongo wina yemwe ndi wamanyazi kwambiri, amati akapita kumsika amamumwetulira munthu amene akufuna kulankhula naye. Munthuyo akamwetuliranso, amamulankhula mawu ochepa. Munthuyo akayankha mwaulemu, mlongoyu amalimba mtima n’kupitiriza kucheza naye. Iye amamvetsera mwatcheru munthuyo akamalankhula uku akuganizira mfundo za m’Baibulo zimene munthuyo angachite nazo chidwi. Njira imeneyi yathandiza mlongoyu kugawira mabuku ambiri komanso kuyambitsa phunziro la Baibulo.
6. Kodi tingayambe bwanji kucheza ndi anthu popanda kuonetsa kuti tikuwalalikira?
6 Mmene Tingayambire Kukambirana: Kodi n’chiyani chimene tinganene kuti tiyambe kulalikira mwamwayi? Polankhula ndi mkazi uja pachitsime, Yesu anayamba ndi kupempha madzi akumwa. (Yoh. 4:7) Choncho mwina mukhoza kulankhulana ndi munthu pomupatsa moni mwansangala kapena pomufunsa funso. Pamene mukucheza mungapeze mpata wofotokoza lemba linalake, zimene zingachititse kuti mubzale mbewu za choonadi. (Mlal. 11:6) Anthu ena aona kuti zinthu zimawayendera bwino akayamba n’kunena mfundo inayake yochititsa chidwi imene imapangitsa anthu kuti afune kudziwa zambiri. Mwachitsanzo, podikirira kuonana ndi dokotala, mungayambe kucheza ndi anthu ponena mawu ngati awa: “Zidzakhala zosangalatsa kwambiri matenda akadzatha padzikoli.”
7. Kodi kuchita chidwi ndi zinthu kungatithandize bwanji kulalikira mwamwayi?
7 Kuchita chidwi ndi zinthu zimene tikuona kungatithandizenso kuti tisavutike kuyamba kulalikira. Mwachitsanzo, ngati kholo lili ndi ana akhalidwe labwino, tingaliyamikire. Kenako tingafunse kuti, “Mumatani kuti ana anu akhale ndi khalidwe labwino chonchi?” Mlongo wina amamvetsera anzake akuntchito akamakambirana nkhani zosiyanasiyana. Kenako amawasonyeza nkhani yomwe anzakewo angachite nayo chidwi yogwirizana ndi zimene akukambiranazo. Atamva kuti mtsikana wina kuntchitoko ali ndi ukwati posachedwa, iye anamupatsa Galamukani! yonena za mmene munthu angakonzekerere mwambo wa ukwati. Zimenezi zinachititsa kuti azikambirana mfundo za m’Baibulo nthawi ndi nthawi.
8. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mabuku athu kuti tiyambe kukambirana ndi anthu?
8 Njira inanso yoyambira kukambirana ndi anthu ndi kuwerenga mabuku kapena magazini athu pamalo amene anthu ena akhoza kutiona. M’bale wina amatenga Nsanja ya Olonda kapena Galamukani!, kutsegula tsamba limene lili ndi nkhani yochititsa chidwi n’kuyamba kuwerenga chamumtima. Akaona kuti munthu wina akuyang’ana magaziniyo, iye amamufunsa funso kapena kumufotokozera mwachidule zimene akuwerenga. Zimenezi zimachititsa kuti ayambe kucheza naye komanso kumulalikira. Kusiya mabuku kapena magazini athu pamalo oonekera n’kothandizanso kwambiri. Anthu amene timagwira nawo ntchito kapena anzathu akusukulu akhoza kuchita nawo chidwi n’kuyamba kutifunsa mafunso n’cholinga choti adziwe zambiri.
9, 10. (a) Kodi tingachite chiyani kuti tikhale ndi mipata yolalikira mwamwayi? (b) Kodi inuyo mipata yolalikira mwamwayi mumaipeza bwanji?
9 Muzifufuza Mipata Yolalikira Mwamwayi: Popeza kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuichita mwachangu, tisamadikire kuti mpata wolalikira upezeke wokha. M’malomwake, tiziyesetsa kufufuza mipata yolalikira tsiku lililonse. Muziganizira za anthu amene mungakumane nawo tsiku limenelo, ndi mmene mungayambire kucheza nawo. Muziyenda ndi Baibulo komanso muzikhala ndi magazini amene mungagawire anthu achidwi.—1 Pet. 3:15.
10 Chifukwa choganiza mwakuya, ofalitsa ambiri apeza mipata yolalikirira mwamwayi. Mwachitsanzo, mlongo wina amakhala m’nyumba yaikulu imene ili kumpanda kumene kumakhala anthu ambiri ndipo kuli chitetezo chokhwima. Iye amagwiritsira ntchito malo osewererako amene ali kumpandako pofuna kukambirana ndi anthu. Amachita masewera olumikiza tizidutswa ta zithunzi kuti apange chithunzi chimodzi chachikulu cha malo okongola. Anthu akaima n’kuyamikira chithunzicho, mlongoyo amagwiritsa ntchito mwayi umenewu n’kuyamba kukambirana nawo zimene Baibulo limalonjeza zokhudza “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” (Chiv. 21:1-4) Kodi mungaganizire njira zimene zingakuthandizeni kupeza mipata yolalikira mwamwayi?
11. Kodi anthu achidwi amene timawalalikira mwamwayi tingawathandize bwanji kuti chidwi chawo chisathe?
11 Muzibwerera kwa Anthu Achidwi: Mukapeza munthu amene wasonyeza chidwi muziyesetsa kukonza zoti mudzakambiranenso. Ngati n’zotheka, mungamuuze munthuyo kuti: “Ndasangalala kwambiri kucheza nanu. Kodi ndingadzakupezeni bwanji kuti tidzachezenso?” Ofalitsa ena amangopereka adiresi ndi nambala yawo ya foni kwa munthuyo n’kumuuza kuti: “Ndasangalala kwambiri kucheza nanu. Ngati mungafune kudziwa zambiri pa nkhani imene takambiranayi, mungagwiritse ntchito adiresi kapena nambala imeneyi.” Ngati inuyo simungathe kudzakumananso ndi munthuyo, mungapereke fomu yakuti Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) kwa mlembi wa mpingo wanu. Mlembiyo angaitumize ku mpingo wa pafupi ndi kumene munthuyo amakhala kuti wofalitsa wina akamuyendere.
12. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kulemba komanso kuchitira lipoti nthawi imene timalalikira mwamwayi? (b) Kodi kulalikira mwamwayi kwathandiza bwanji? (Onani bokosi lakuti “Ulaliki Wamwamwayi Umathandiza.”)
12 Nthawi imene timalalikira mwamwayi tiyenera kuichitira lipoti. Choncho, muziyesetsa kulemba nthawi iliyonse imene mwalalikira mwamwayi, ngakhale ngati ndi mphindi zochepa chabe. Taganizirani izi: Ngati wofalitsa aliyense atamalalikira mwamwayi kwa mphindi zisanu tsiku lililonse, pomatha mwezi tonse pamodzi tikhoza kukhala titalalikira maola oposa 17 miliyoni.
13. Kodi tili ndi zifukwa zomveka ziti zolalikirira mwamwayi?
13 Tili ndi zifukwa zomveka zolalikirira mwamwayi. Timalalikira mwamwayi chifukwa chakuti timakonda Mulungu komanso anthu anzathu. (Mat. 22:37-39) Timayamikira kwambiri makhalidwe a Yehova ndi zolinga zake ndipo zimenezi zimatichititsa kulankhula za “ulemerero waukulu wa ufumu wake” (Sal. 145:7, 10-12) Chifukwa chakuti timadera nkhawa anthu anzathu, timagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene wapezeka kuti tiwalalikire uthenga wabwino nthawi isanathe. (Aroma 10:13, 14) Ngati tonsefe titaganizira bwinobwino ndi kukonzekera pasadakhale, tikhoza kukwanitsa kulalikira mwamwayi. Mwinanso tikhoza kuthandiza anthu a mitima yabwino kuphunzira choonadi, ndipo zimenezi zingatibweretsere chimwemwe chachikulu.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Nthawi zina ndi bwino kuyamba kucheza kaye ndi munthuyo
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Chifukwa choganiza mwakuya, ofalitsa ambiri apeza mipata yolalikirira mwamwayi
[Bokosi patsamba 5]
Zimene Mungachite Kuti Muyambe Kulalikira
◼ Pempherani kuti Mulungu akuthandizeni kulimba mtima
◼ Sankhani anthu amene akuoneka kuti ndi ochezeka komanso amene sakufulumira kwambiri
◼ Mwetulirani ndipo tchulani mfundo imene iyenso angachite nayo chidwi
◼ Mvetserani mwatcheru
[Bokosi patsamba 6]
Ulaliki wa Mwamwayi Umathandiza
• M’bale wina akudikirira kuti galimoto yake ikonzedwe pagalaja, analalikira anthu amene anali pamalopo n’kuwapatsa timapepala towaitanira ku nkhani ya onse. Pamsonkhano wachigawo chaka chotsatira, m’baleyo anapatsidwa moni mwansangala ndi munthu wina amene sanamuzindikire. Munthuyo anali mmodzi wa anthu amene anawapatsa timapepala aja. Munthuyo atalandira kapepala kaja anapita kukamvetsera nkhani ya onse ndipo anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Pa nthawi ya msonkhanowu n’kuti munthuyo ndi mkazi wake atabatizidwa.
• Mlongo wina amene anaphunzira choonadi atalalikiridwa mwamwayi, amaona kuti gawo lake lolalikirira ndi anthu amene amakumana nawo kudzera mwa ana ake atatu. Iye amalalikira anthu oyandikana nawo nyumba komanso makolo a ana ena amene amakumana nawo kusukulu ndi pamisonkhano ya makolo. Poyamba kulankhula, amafotokoza kuti iye ndi ndani ndipo amanena kuti Baibulo lamuthandiza kwambiri kuti alere bwino ana ake. Kenako amapitiriza kulankhula nkhani zina. Akachita zimenezi, zimakhala zosavuta kutchula mfundo za m’Baibulo pamene akukambirana nkhani zinazo. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, mlongoyu wathandiza anthu 12 kubatizidwa.
• Munthu wina wogwira ntchito ku kampani ya inshuwalansi atabwera kunyumba ya mlongo wina, mlongoyo anapezerapo mwayi womulalikira. Mlongoyo anafunsa munthuyo ngati angafune kukhala ndi inshuwalansi ya thanzi labwino, moyo wachimwemwe, komanso moyo wosatha. Munthuyo anayankha kuti angakonde koma anafunsa kuti angaipeze kuti inshuwalansi yotere. Mlongoyo anamusonyeza zimene Baibulo limalonjeza ndipo anamupatsanso magazini athu. Munthuyo anawerenga magaziniyi n’kuimaliza tsiku limodzi. Kenako anayamba kuphunzira Baibulo. Ankapezeka pamisonkhano ndipo patapita nthawi anabatizidwa.
• Mlongo wina ali pa ulendo wa pa ndege, anayamba kucheza ndi mayi amene anakhala naye pafupi ndipo anamulalikira. Kumapeto kwa ulendo wawo, mlongoyo anapatsa mayiyo adiresi ndi nambala yake ya foni, ndipo anamulimbikitsa kuti akadzakumananso ndi a Mboni za Yehova adzawapemphe kuti ayambe kumuphunzitsa Baibulo. Tsiku lotsatira, anthu awiri a Mboni za Yehova anafika panyumba pake. Mayiyo anayamba kuphunzira Baibulo, anapita patsogolo mofulumira ndipo anabatizidwa. Pasanapite nthawi yaitali, anayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo atatu.
• M’bale wina wosaona wa zaka 100 yemwe amakhala kunyumba yosungira okalamba amakonda kunena kuti, “Tikufunikira Ufumu wa Mulungu.” Zimenezi zimachititsa kuti manesi ndi anthu ena okalamba azimufunsa mafunso. Akatero, iye amayamba kuwafotokozera zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu. Mayi wina amene amagwira ntchito pamalowa anamufunsa m’baleyo kuti afotokoze zimene adzachite m’Paradaiso. Iye anayankha kuti, “Ndidzayambanso kuona ndi kuyenda bwinobwino, komanso ndidzawotcha njinga imene ndimayenderayi.” Popeza m’baleyu saona, amapempha mayiyo kuti azimuwerengera magazini. Tsiku lina kutabwera mwana wamkazi wa m’baleyo, mayiyo anamupempha kuti atengeko magaziniwo kupita nawo kwawo. Nesi wina wa pamalopa anauza mwanayo kuti, “Panopa tikuyendera mfundo yakuti: ‘Tikufunikira Ufumu wa Mulungu.’”
• Mlongo wina akudikirira chakudya palesitilanti, anamva amuna angapo achikulire amene anakhala pafupi naye akukambirana nkhani za ndale. Mmodzi wa iwo ananena kuti boma silingathetse mavuto a anthu. Mlongoyo ananena chamumtima kuti, ‘Eya, mwayi uja ndi umenewu.’ Iye anapemphera chamumtima mwachidule, kenako anapita pamene panali anthuwo. Atafotokoza kuti iye ndi ndani, anawafotokozera kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu. Kenako anawapatsa kabuku kamene anali nako. Pasanapite nthawi, mkulu wa palesitilantipo anafika. Mlongoyo anaganiza kuti mwina mkuluyo akufuna kumuuza kuti achoke pamalopo. Koma mkuluyo anauza mlongoyo kuti amamva nawo zimene amakambirana ndi anthu aja ndipo nayenso akufuna kubuku kake. Mayi winanso wogwira ntchito pamalopo amene amamvetsera anabwera pomwepo, misozi ikuyenderera m’masaya. Iye ananena kuti kale ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo akufuna kuyambiranso kuphunzira.