Kodi Mwagwiritsapo Ntchito Tsamba Lomaliza?
Anthu akatenga magazini nthawi zambiri amayang’ana tsamba loyamba ndipo kenako amaitembenuza n’kuyang’ana tsamba lomaliza. Patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda yogawira pamakhala mafunso ndiponso mfundo zosiyanasiyana zochititsa chidwi. Amasonyezaponso masamba amene nkhanizo zikupezeka m’magaziniyo.
Tikhoza kugwiritsa ntchito mafunso ndiponso mfundo zimenezi poyamba kukambirana ndi munthu. Ngati timapitapita m’gawo lathu, tikhoza kugwiritsa ntchito mafunso osiyanasiyana kuti tizikhala ndi ulaliki wosiyanasiyananso mwezi wonse. Ngati mwininyumba watanganidwa, tikhoza kufupikitsa ulaliki wathu pomusonyeza funso limodzi limene lili patsamba lomaliza la magazini. Kenako tingamuuze kuti, “Ngati mukufuna kudziwa yankho la funso limeneli, ndikhoza kukusiyirani magazini awa ndipo tidzakambirana zambiri mukadzakhala ndi mpata.” Ofalitsa ena amayamba kukambirana ndi mwininyumba pomusonyeza tsamba lomaliza n’kumupempha kuti asankhe funso limene wachita nalo chidwi. Kenako amamusonyeza pamene angapezepo yankho m’magaziniyo, n’kuwerenga lemba limene analikonzekera. Mwina inunso mungaganizire njira zina zimene mungagwiritsire ntchito tsamba lomaliza kuti muchititse anthu kukopeka ndi Nsanja ya Olonda.