‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
1. Kodi kuyambira mlungu wa January 23, tidzayamba kuphunzira buku liti pa Phunziro la Baibulo la Mpingo?
1 Kuyambira mlungu wa January 23, 2012, tidzayamba kuphunzira buku la ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’ pa Phunziro la Baibulo la Mpingo. Buku limeneli likufotokoza nkhani za m’buku la m’Baibulo la Machitidwe, zimene zinachitika mofulumira kwambiri, m’njira yosangalatsa kwambiri kwa wowerenga. Cholinga cha buku la Kuchitira Umboni si kufotokoza nkhani za m’buku la Machitidwe vesi ndi vesi, koma kuti tiphunzirepo kanthu pa nkhani za m’buku la m’Baibulo limeneli ndiponso kuti tione mmene ifeyo patokha tingagwiritsire ntchito zimene taphunzirazo.—Aroma 15:4.
2. Fotokozani zinthu zina zopezeka m’buku la Kuchitira Umboni.
2 Zinthu Zopezeka M’bukuli: Mawu oyamba omwe akupezeka patsamba 2 ndi kalata yochokera ku Bungwe Lolamulira. Kalatayi ikufotokoza zimene tingachite kuti tipindule ndi bukuli. Kumayambiriro kwa mutu uliwonse kuli mfundo imene ikufotokoza mwachidule mfundo yaikulu ya mutuwo ndiponso kuli mavesi a m’buku la Machitidwe amene akufotokozedwa m’mutu umenewo. Mitu yambiri ili ndi mabokosi amene ali ndi mfundo zothandiza zofotokoza mbiri za anthu, malo ndi zochitika. M’mbali mwa masamba a bukuli muli mipata ikuluikulu mmene tingalembemo mfundo zathu. M’bukuli mulinso zithunzi za zochitika m’nthawi ya Baibulo zotithandiza kuona m’maganizo mwathu zochitika zofunika kwambiri. Patsamba lomaliza pali mlozera wa zithunzi amene akufotokoza zimene zasonyezedwa pa zithunzi zosiyanasiyana. M’kati mwa chikuto choyamba ndi chomaliza muli mapu otithandiza kuona malo amene Akhristu anzathu analalikirako kuyambira pamene anayamba kulalikira uthenga wabwino mpaka kufika “kumalekezero a dziko lapansi.”—Mac. 1:8.
3. Kodi tikamaphunzira buku la Machitidwe tipeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri ati?
3 Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri: Kukambirana buku la Machitidwe kutithandiza kudziwa bwino mayankho a mafunso ofunika kwambiri okhudza ntchito yolalikira ya Akhristu. Mwachitsanzo, kodi ndi ntchito ndiponso uthenga uti umene umadziwikitsa otsatira enieni a Yesu Khristu? Kodi ndani akutsogolera ntchito yolalikira imeneyi padziko lonse lapansi ndipo akuchita bwanji zimenezi? Kodi chizunzo chimapereka mpata wotani kwa atumiki a Mulungu? Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji pa ntchito yathu yolalikira?
4. Fotokozani zimene tingachite kuti tipindule kwambiri pamene tikuphunzira buku la Kuchitira Umboni.
4 Kuti mupindule kwambiri pophunzira bukuli, muzikonzekera zimene mukaphunzire ndiponso kukayankha pamene mukukambirana ku mpingo. Muzipezeka pa msonkhano uliwonse ndiponso muzisinkhasinkha mmene mungagwiritsire ntchito zimene mwaphunzira pa utumiki wanu. Choncho, kuphunzira kwathu buku losangalatsali kutilimbikitse kuchitira umboni za Ufumu wa Mulungu mokwanira.—Mac. 28:23.