Timakobidi Tiwiri Tochepa Mphamvu
Njira imodzi imene tingathandizire pa zinthu za Ufumu ndi kupereka nawo ndalama zothandizira pa ntchito yolalikira padziko lonse. Bwanji ngati timapeza ndalama movutikira?
Nthawi ina Yesu anaona mkazi wamasiye akuponya timakobidi tiwiri tochepa mphamvu moponyamo zopereka m’kachisi. Kukonda Yehova n’kumene kunachititsa mayiyu kupereka “mu umphawi wake, . . . zonse zimene anali nazo, inde zonse zochirikizira moyo wake.” (Maliko 12:41-44) Chifukwa chakuti Yesu anatchula nkhani imeneyi, zikusonyeza kuti zimene mayiyu anapereka zinali zamtengo wapatali kwa Mulungu. Nawonso Akhristu oyambirira sankaona kuti Akhristu olemera okha ndi amene anali ndi udindo wopereka. Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo cha anthu a ku Makedoniya. Ngakhale kuti anali pa ‘umphawi wadzaoneni, . . . anapitiriza kupempha mochonderera kwambiri, kuti awapatse mwayi wopereka nawo.’—2 Akor. 8:1-4.
Choncho, tizikumbukira kuti ngati nafenso tingamapereke “timakobidi tiwiri tochepa mphamvu,” pamapeto pake timakobidi tambiri tidzakhala ndalama zambiri. Ndipotu tikamapereka mochokera pansi pa mtima, Atate wathu wakumwamba amene ndi wopatsa, adzasangalala chifukwa “Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 Akor. 9:7.