Kodi Muli ndi “Chifukwa Chosangalalira”?
1. N’chiyani chimatichititsa kukhala osangalala kumapeto kwa mwezi uliwonse?
1 Kumapeto kwa mwezi uliwonse timapemphedwa kuti tipereke malipoti a utumiki wa kumunda. Kodi inuyo mumakhala ndi “chifukwa chosangalalira” ndi zimene mwachita mu utumiki? (Agal. 6:4) Kaya ndinu mpainiya wapadera yemwe amapereka maola 130 kapena ndinu wofalitsa amene anavomerezedwa kuti akhoza kumapereka mphindi 15, tonsefe tiyenera kusangalala chifukwa chotumikira Yehova ndi mtima wonse.—Sal. 100:2.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuchita zambiri potumikira Yehova?
2 Yehova ndi Ambuye Wamkulu Koposa wachilengedwe chonse ndipo tiyenera kumutumikira ndi mtima wonse. (Mal. 1:6) Chifukwa chakuti timamukonda, tinadzipereka kuti tichite chifuniro chake. Choncho, ngati pamapeto pa tsiku kapena mwezi uliwonse, timaona kuti tatumikira Yehova ndi nthawi yathu, luso lathu komanso mphamvu zathu zonse, zomwe zili ngati “zipatso zoyambirira,” timakhala ndi chifukwa chosangalalira. (Miy. 3:9) Komabe, ngati chikumbumtima chathu chikutiuza kuti tikanatha kuchita zambiri, tingachite bwino kuona zimene tingachite kuti tiwonjezere utumiki wathu.—Aroma 2:15.
3. N’chifukwa chiyani sibwino kudziyerekezera ndi anthu ena?
3 “Osati Modziyerekezera Ndi Munthu Wina”: Sibwino kuti tizidziyerekezera ndi anthu ena kapena kudziyerekezera mmene tinalili pamene tinali ndi mphamvu. Zinthu zimasintha pamoyo komanso anthu amakhala ndi luso losiyanasiyana. Kudziyerekezera ndi ena kumachititsa kuti tikhale ndi mtima wampikisano kapena kumadziona kuti ndife osafunika. (Agal. 5:26; 6:4) Yesu sankayerekezera munthu ndi munthu wina. M’malo mwake ankayamikira munthu mogwirizana ndi zimene wakwanitsa kuchita.—Maliko 14:6-9.
4. Kodi tingaphunzire chiyani pa fanizo la Yesu la matalente?
4 Mu fanizo la Yesu la matalente, wantchito aliyense analandira matalente “malinga ndi luso lake.” (Mat. 25:15) Mbuye wawo atabwera anawafunsa zimene achita ndi ndalama zimene anawapatsa. Amene anagwira ntchito mwakhama mogwirizana ndi luso lawo komanso mmene zinthu zinalili pamoyo wawo, anawayamikira ndipo anasangalala limodzi ndi mbuye wawo. (Mat. 25:21, 23) Ifenso tikamalalikira mwakhama za Ufumu, Mulungu adzasangalala nafe ndipo tidzakhala ndi chifukwa chosangalalira.