Gwiritsani Ntchito Webusaiti Yathu Yovomerezeka Pophunzira Panokha Komanso Pophunzira ndi Banja Lanu
Werengani Magazini Atsopano pa Intaneti: Werengani magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pa Intaneti. Magaziniwa amaikidwa pa Intaneti kutatsala milungu ingapo kuti tiwalandire kumpingo. Mukhozanso kumvetsera magaziniwa pa Intaneti.—Pitani pamutu wakuti “Mabuku Ndiponso Zinthu Zina/Magazini.”
Werengani Nkhani Zimene Zimapezeka pa Webusaiti Pokha: Nkhani zina monga zakuti “Za Achinyamata,” “Zimene Ndikuphunzira m’Baibulo,” “Zokhudza Banja Lonse” ndi “Zimene Achinyamata Amadzifunsa,” tsopano zikupezeka pa Webusaiti pokha. Mukamaphunzira Baibulo panokha kapena mukamaphunzira ndi banja lanu, muzipita pa Webusaitiyi ndi kuphunzira zina mwa nkhanizi.—Pitani pamutu wakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa/Zoti Ana Achite/Achinyamata.”
Werengani Nkhani Zongochitika Kumene: Werengani malipoti olimbikitsa komanso zimene atumiki a Mulungu akukumana nazo m’madera osiyanasiyana padziko lonse lapansi. Mungathenso kuonera timavidiyo tosonyeza mmene ntchito yathu ikuyendera padziko lonse. Palinso malipoti onena za masoka achilengedwe ndiponso onena za anthu a Mboni omwe akuzunzidwa. Nkhani zimenezi zingatithandize kuti tiziwatchula abalewa mwachindunji m’mapemphero athu. (Yak. 5:16)—Pitani pamutu wakuti “Nkhani.”
Fufuzani Nkhani pa Laibulale ya pa Intaneti: Ngati laibulaleyi ilipo m’chinenero chanu, igwiritseni ntchito ngati muli ndi kompyuta kapena chipangizo chamakono cha m’manja kuti muzitha kuwerenga lemba la tsiku pa Intaneti. Mungathenso kufufuza nkhani zosiyanasiyana m’mabuku ndi magazini atsopano.—Pitani pamutu wakuti “Mabuku Ndiponso Zinthu Zina/Laibulale ya pa Intaneti,” kapena lembani adiresi iyi pamalo olembapo adiresi: www.wol.jw.org.
[Chithunzi patsamba 4]
(Onani mu Utumiki wa Ufumu kuti mumvetse izi)
Iyeseni
1 Tsegulani chithunzi kapena mawu akuti “Koperani.” Chithunzi chizitseguka patsamba la PDF. Chisindikizeni kuti muchigwiritse ntchito pophunzitsa mwana wanu.
2 Kuti muonere vidiyo, sindikizani batani lotsegulira vidiyo.