‘Perekani Umboni Mokwanira’
1. Kodi mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino chiti pa nkhani ya utumiki?
1 Mtumwi Paulo analangiza Timoteyo kuti: “Ukwaniritse mbali zonse za utumiki wako.” (2 Tim. 4:5) Mtumwi Paulo anali ndi ufulu wopereka malangizo amenewa kwa Timoteyo chifukwa nayenso mtumwiyu ankalalikira mwakhama. Ndipotu Paulo anayenda maulendo atatu aumishonale kuyambira mu 47 C.E. mpaka mu 56 C.E. Komanso buku la Machitidwe limanena mobwerezabwereza kuti Paulo anachitira “umboni mokwanira.” (Mac. 23:11; 28:23) Kodi masiku ano tingatani kuti nafenso tizilalikira mwakhama?
2. Kodi tingapereke bwanji umboni mokwanira tikamalalikira kunyumba ndi nyumba?
2 Kunyumba ndi Nyumba: Kuti tikwanitse kulalikira anthu amene sanamvepo uthenga wabwino, mwina tingachite bwino kusintha nthawi imene timapitira kunyumba ndi nyumba. Mwachitsanzo, tingapeze abambo pakhomo ngati tikulalikira madzulo kapena Loweruka ndi Lamlungu. Tiyenera kuchita khama kuti tizilankhula ndi munthu panyumba iliyonse ndipo zimenezi zingatheke ngati titamapita mobwerezabwereza kunyumba zomwe sitinapezeko anthu. Koma kodi mungatani ngati simukupeza anthu nthawi iliyonse imene mwapita panyumba inayake? Mwina mungathe kuwalalikira powalembera kalata kapena kuwaimbira foni.
3. Kodi inuyo panokha mumakhala ndi mwayi wotani wolalikira m’misewu ndiponso mwamwayi?
3 Kulalikira M’misewu Ndiponso Mwamwayi: Atumiki a Yehova masiku ano amalalikira “nzeru yeniyeni” kwa aliyense amene angamvetsere. Nthawi zina zimenezi zimachitika “mumsewu” kapena “m’mabwalo a mzinda.” (Miy. 1:20, 21) Choncho, tikamachita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku, tiyenera kudzifunsa kuti, Kodi ndimakhala wokonzeka kupereka umboni? Kodi ndimakhala ‘wotanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu?’ (Mac. 18:5) Ngati timatero ndiye kuti tikukwaniritsa udindo wathu ‘wopereka umboni mokwanira.’—Mac. 10:42; 17:17; 20:20, 21, 24.
4. Kodi kupemphera komanso kusinkhasinkha kungatithandize bwanji kuti tizipereka umboni mokwanira?
4 Komabe nthawi zina tingalephere kupereka umboni chifukwa cha mphwayi kapena manyazi. Tisakayikire kuti Yehova amatimvetsa ndipo amadziwa zimene tingakwanitse. (Sal. 103:14) Komabe tikhoza kupemphera kwa Yehova kuti atipatse mphamvu zoti tikwanitse kulalikira. (Mac. 4:29, 31) Komanso kuphunzira Mawu a Mulungu patokha ndiponso kusinkhasinkha kungatithandize kuti tiziyamikira kwambiri uthenga wabwino womwe ndi wamtengo wapatali. (Afil. 3:8) Zimenezi zingatithandize kuti tizilalikira mwakhama.
5. Kodi tingathandizire bwanji kukwaniritsa ulosi wa Yoweli?
5 Ulosi wa Yoweli unaneneratu kuti tsiku lalikulu la Yehova lomwe ndi loopsa komanso lochititsa mantha lisanafike, anthu a Mulungu adzapitiriza ‘kuyenda’ ndipo sadzalola chilichonse kuti chiwalepheretse kulalikira. (Yow. 2:2, 7-9) Choncho tiyeni tipitirize kugwira nawo mwakhama ntchito yochitira umboniyi, yomwe sidzabwerezedwenso.