Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/13 tsamba 2
  • Kodi Ndi Ndani Amene Angakonde Magazini Awa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndi Ndani Amene Angakonde Magazini Awa?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Sankhani Nkhani Zokopa Chidwi cha Anthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 5/13 tsamba 2

Kodi Ndi Ndani Amene Angakonde Magazini Awa?

1. Tikamawerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! tiyenera kuganizira ndani, ndipo n’chifukwa chiyani?

1 Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amalembedwa pofuna kuthandiza anthu osiyanasiyana padziko lonse. Choncho, magaziniwa amakhala ndi nkhani zosiyanasiyana. Tikamawerenga nkhani iliyonse m’magaziniwa, tiyenera kumaganizira anthu amene angapindule ndi nkhani imeneyo. Tikatero, tizikagawira anthuwo magaziniyo.

2. Kodi ndi nkhani ziti zimene zili m’magazini zimene anthu ena angachite nazo chidwi?

2 Kodi Nsanja ya Olonda imene mwangolandira kumene ikufotokoza nkhani ya m’Baibulo imene munakambiranapo ndi mnzanu wa kuntchito? Kodi m’magaziniyo muli nkhani ina yokhudza banja imene ingathandize wachibale wanu? Kodi pali mnzanu amene akukonzekera ulendo wopita kudziko lina limene lafotokozedwa m’magazini ya Galamukani!? Kodi pali anthu ogwira ntchito zina kapena am’boma amene angakonde magaziniwa? Mwachitsanzo, magazini imene ikufotokoza za mavuto amene anthu okalamba amakumana nawo ingasangalatse anthu amene akusamalira anthu okalamba. Anthu ogwira ntchito zachitetezo angasangalale kuwagawira magazini onena za chiwawa.

3. Fotokozani chitsanzo chosonyeza kufunika kogawira magazini kwa anthu amene tikuganiza kuti angakonde nkhani zake?

3 Zotsatira Zake: Banja lina la Mboni ku South Africa litawerenga magazini ya mutu wakuti, “Kodi Mungalere Bwanji Ana Anu Kuti Akule Bwino?,” linaimbira foni masukulu okwana 25 a m’gawo la mpingo wawo. Masukulu okwana 22 analandira magaziniyo ndipo anagawira ana awo asukulu. Banja lina m’dziko lomwelo linachitanso chimodzimodzi ndipo linagawira magazini ambiri m’masukulu amene anali m’gawo lawo. Aphunzitsi a sukulu ina anaika magaziniwa m’gulu la mabuku amene ankaphunzitsira. Banja limeneli linafotokozera woyang’anira dera zimenezi ndipo iye analimbikitsa mipingo ya m’dera lake kuti agawire magaziniwo m’masukulu a m’gawo lawo. Chifukwa cha zimenezi, ofesi ya nthambi inalandira maoda owonjezereka a magaziniwa ndipo zinachititsa kuti magaziniwa asindikizidwenso.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kugawira anthu ambiri magazini athu?

4 Magazini athu amathandiza anthu kumvetsa zinthu zimene zikuchitika masiku ano. Amafotokozanso zimene Baibulo limanena komanso za Ufumu wa Mulungu. Magaziniwa ndi okhawo padziko lapansi omwe ‘amalengeza za chipulumutso.’ (Yes. 52:7) Choncho, tiyenera kugawira anthu ambiri magaziniwa. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kumadzifunsa kuti, ‘Kodi ndi ndani amene angakonde magazini awa?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena