Muzigwiritsira Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa
Pamene Yehova ankauza Abulahamu ndi Yeremiya zinthu zofunika, sankangowafotokozera zinthuzo koma ankagwiritsanso ntchito zinthu zooneka. (Gen. 15:5; Yer. 18:1-6) Tingathandize ophunzira Baibulo athu kumvetsa zimene Baibulo limanena tikamagwiritsira ntchito bwino zinthu monga mavidiyo. Mavidiyo otsatirawa mungaonetse ophunzira Baibulo anu pamene mukuphunzira nawo mitu ina ya m’mabuku athu. Koma sikuti ndi lamulo kuti muzichita zimenezi nthawi zonse popeza kuti anthu amene timaphunzira nawo amasiyanasiyana.
Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
◻ Mutu 1: Mukaphunzira ndime 17, muonetseni vidiyo yakuti, The Wonders of Creation Reveal God’s Glory
◻ Mutu 2: Pamapeto pa mutuwu, muonetseni vidiyo ya The Bible—Mankind’s Oldest Modern Book
◻ Mutu 9: Mukaphunzira ndime 14, muonetseni vidiyo ya Mboni za Yehova—Gulu Limene Likulalikira Uthenga Wabwino
◻ Mutu 14: Pamapeto pa mutuwu, muonetseni vidiyo yakuti, The Bible—Its Power in Your Life
◻ Mutu 15: Mukamaliza ndime 10, muonetseni vidiyo yakuti, Gulu Lonse la Abale
Buku la “Chikondi cha Mulungu”
◻ Mutu 3: Mukamaliza ndime 15, muonetseni vidiyo yakuti, Zimene Achinyamata amadzifunsa—Kodi Ndingapeze Bwanji Anzanga Abwino?
◻ Mutu 4: Pamapeto pa mutuwu, muonetseni vidiyo yakuti, Respect Jehovah’s Authority
◻ Mutu 7: Mukamaliza ndime 12, muonetseni vidiyo yakuti, No Blood—Medicine Meets the Challenge
◻ Mutu 9: Mukamaliza ndime 6, muonetseni vidiyo yakuti, Warning Examples for Our Day
◻ Mutu 17: Pamapeto pa mutuwu, muonetseni vidiyo yakuti, ‘Yendani mwa Chikhulupiliro Osati mwa Zooneka ndi Maso’
Kodi pali mavidiyo ena amene angathandize ophunzira anu ngati atawaonera? Mwachitsanzo, ophunzira Baibulo amene akutsutsidwa angalimbikitsidwe ataonera vidiyo yakuti, Faithful Under Trials—Jehovah’s Witnesses in the Soviet Union kapena Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault. Achinyamata angapindule ataonera vidiyo yakuti, Pursue Goals That Honor God ndi Young People Ask—What Will I Do With My Life? Mulembe zimenezi m’buku lanu la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso la “Chikondi cha Mulungu” kuti muzidziwa pamene mungaonetse wophunzira wanu vidiyo kapena kumubwereka kuti aionere. Mavidiyo atsopano akatuluka, ganizirani mmene mungawagwiritsire ntchito pothandiza anthu amene mukuphunzira nawo Baibulo.—Luka 24:32.