Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/13 tsamba 1
  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Yoweli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Yoweli
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Mavuto Amene Takumana Nawo Atithandiza Kudalira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Gulu Lankhondo Lochokera Kumpoto
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Kodi ‘Adzapulumuka Ndani’?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kumbukirani Tsiku la Yehova
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 7/13 tsamba 1

Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Yoweli

1. Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Yoweli tikamalikira?

1 Kodi mneneri Yoweli anali ndani? Iye anangonena kuti anali “mwana wa Petueli.” (Yow. 1:1) Mneneri wodzichepetsayu anatsindika za kufunika kwa uthenga wa Yehova, osati za udindo wake monga mneneri. Mofanana ndi zimenezi, ifenso tikakhala mu utumiki sitifuna kuti anthu azitama ifeyo, koma timafuna kuti azitamanda Yehova ndiponso azidalira Baibulo. (1 Akor. 9:16; 2 Akor. 3:5) Uthenga umene timalalikira umatilimbikitsa kwambiri. Kodi ndi mbali ziti za ulosi wa Yoweli zimene zingatilimbikitse kukhala ndi chiyembekezo komanso kugwira ntchito yathu mwakhama?

2. Kodi kudziwa kuti tsiku la Yehova layandikira, kuyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani?

2 “Tsiku la Yehova Lili Pafupi.” (Yow. 1:15): Ngakhale kuti mawu amenewa analembedwa zaka zambirimbiri zapitazo, akukwaniritsidwa m’masiku athu ano. Mmene zinthu zaipira padzikoli komanso kuchuluka kwa anthu osakonda uthenga wathu omwe amatinyoza, ndi umboni wakuti tili m’masiku otsiriza. (2 Tim. 3:1-5; 2 Pet. 3:3, 4) Tikamaganizira zoti mapeto ayandikira, timaona kuti ntchito yathu yolalikira ndi yofunika kwambiri pa moyo wathu.—2 Pet. 3:11, 12.

3. N’chifukwa chiyani ntchito yathu yolalikira ndi yofunika kwambiri makamaka panopa, pamene chisautso chachikulu chikuyandikira?

3 “Yehova Adzakhala Chitetezo kwa Anthu Ake.” (Yow. 3:16): Kugwedezeka kumene kwatchulidwa pavesili kukunena za zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu pa nthawi yomwe Yehova adzapereke chiweruzo. Koma kudziwa kuti pa nthawiyi Yehova adzapulumutsa atumiki ake okhulupirika, kumatilimbikitsa kwambiri. (Chiv. 7:9, 14) Tikamagwira ntchito yolalikira n’kumaona mmene Yehova amatithandizira, timakhala ndi chikhulupiriro ndiponso timaphunzira kupirira ndipo makhalidwe amenewa adzatithandiza pa chisautso chachikulu.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osangalala tikamayembekezera tsiku la Yehova?

4 Ngakhale anthu ena amaona kuti uthenga wa Yoweli ndi wosasangalatsa, uthengawu umapereka chiyembekezo chosangalatsa kwa atumiki a Mulungu. (Yow. 2:32) Choncho, tiziyembekezera tsiku la Yehova mwachidaliro kwinaku tikulalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu potsatira mawu a pa Yoweli 2:23 akuti: “Kondwerani ndi kusangalala chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena