Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/13 tsamba 1
  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Hoseya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Hoseya
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Ulosi wa Hoseya Umatithandiza Kuyenda ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Hoseya
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Yendani ndi Mulungu, Kuti Mukolole Zabwino
    Nsanja ya Olonda—2005
  • “Njira za Yehova Zili Zoongoka”
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
km 11/13 tsamba 1

Tengerani Chitsanzo kwa Aneneri—Hoseya

1. Kodi mwina munadzifunsapo funso lotani?

1 ‘Kodi ndingatani kuti ndizikhala ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova?’ Mwina mumadzifunsa funso limeneli mukaganizira zabwino zimene Mulungu wakuchitirani. (Sal. 103:2-4; 116:12) Mneneri Hoseya anagwira modzipereka ntchito imene Yehova anamupatsa ngakhale kuti kuchita zimenezi kunkafuna kuti akhale wodzimana. Kodi tingatengere bwanji chitsanzo chake?

2. Kodi chitsanzo cha Hoseya chingatithandize bwanji kuti tizipirira tikamakumana ndi mavuto polalikira?

2 Ankalalikira M’nthawi Yovuta: Uthenga wa Hoseya makamaka unali wopita kwa anthu a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10, ndipo pa nthawiyi n’kuti kulambira koona kutangotsala pang’ono kutheratu. Mfumu Yerobowamu Yachiwiri inkachita zinthu zoipa kwambiri pamaso pa Yehova ndipo inkalimbikitsa kulambira mwana wa ng’ombe. Mfumu Yerobowamu Yoyamba ndi imene inayambitsa kulambira kumeneku. (2 Maf. 14:23, 24) Mafumu amene anabwera pambuyo pake anapitiriza kuchita zoipa mpaka pamene ufumuwo unawonongedwa mu 740 B.C.E. Ngakhale kuti kulambira konyenga kunali ponseponse, Hoseya anatumikira Yehova mokhulupirika ngati mneneri kwa zaka pafupifupi 59. Kodi ifenso timalalikirabe nthawi zonse ngakhale pamene anthu akutitsutsa komanso kudana nafe?—2 Tim. 4:2.

3. Kodi zimene zinachitika pa moyo wa Hoseya zinasonyeza bwanji kuti Yehova ndi Mulungu wachifundo?

3 Muziganizira Chifundo cha Yehova: Yehova anauza Hoseya kuti akwatire ‘mkazi wadama.’ (Hos. 1:2) Ngakhale kuti mkazi wake Gomeri anamuberekera mwana wamwamuna, iye anaberekanso ana ena awiri apathengo. Hoseya anakhalabe wokhulupirika kwa mkazi wakeyu komanso anam’khululukira, ndipo izi zinasonyeza chifundo chimene Yehova anasonyeza ku mtundu wa Isiraeli. (Hos. 3:1; Aroma 9:22-26) Kodi ifenso ndife okonzeka kusalola zimene timakonda kutilepheretsa kuthandiza anthu amitundu yonse kuti adziwe kuti Yehova ndi wachifundo?—1 Akor. 9:19-23.

4. Kodi anthu ena achita zotani kuti azikhala ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova?

4 Atumiki ena a Yehova asiya ntchito zapamwamba kuti azithera nthawi yambiri akuchita utumiki. Ena asankha kusakhala pabanja kapena kukhala opanda ana n’cholinga choti azikhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu za Ufumu. Tikaganizira zimene Hoseya anachita pa moyo wake, mwina tingaganize kuti, ‘Koma ine sindingachite zimenezo.’ Koma ngati timayamikira zabwino zimene Yehova amatichitira komanso kudalira mzimu wake woyera, tidzalola kuti Yehova atigwiritsire ntchito m’njira iliyonse, ngati mmene anachitira ndi Hoseya.—Mat. 19:26; Afil. 2:13.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena