Zimene Ena Anachitapo
◼ Australia: John, yemwe ndi wophunzira kwambiri, ankapita kutchalitchi ali mwana koma kenako anasiya ndipo anayamba kukhulupirira kuti kulibe Mulungu. Mpainiya wina anamupatsa kabuku kakuti Was Life Created? ndipo pa ulendo wotsatira anam’patsanso kabuku kakuti Origin of Life. Mpainiyayo anapitirizabe kum’patsa John magazini atsopano ndipo ankakambirana naye nkhani za m’magaziniwo zomwe zimanena za chilengedwe komanso maulosi a m’Baibulo. Ataona kuti John wayamba kumvetsa bwino mfundo zina, anamupatsa buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Atawerenga bukuli, John anayamba kunena kuti Mulungu aliko koma kungoti ndi wosadziwika bwinobwino. Kenako mpainiyayo anamupatsa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo anamusonyeza ndime 8 patsamba 20, ndime 13 mpaka 16 patsamba 23 ndi 24. John anachita chidwi kwambiri ndi malemba amene ali m’ndime zimenezi, moti anati: “Mwina zingakhale bwinodi nditaphunzira Baibulo. N’kutheka kuti limanena zoona.”
◼ Mexico: Munthu wina anauza m’bale wina kuti iye sakhulupirira kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu. M’baleyo anamuuza kuti angathe kumusonyeza umboni woti Baibulo ndi louziridwa. Atakambirana kwa kanthawi, munthuyo anakhudzidwa mtima ndi zimene anaphunzira m’Baibulo. Anakhudzidwa kwambiri makamaka ataphunzira zokhudza mfundo za makhalidwe abwino zimene zili m’Baibulo. Anauza m’baleyo kuti: “Poyamba tikamawerenga Baibulo ndinkangoona ngati malangizo ake ndi ochokera kwa munthu, ngati mmene zimakhalira ndi mabuku ena onse, ndipo malangizowo ndinalibe nawo ntchito kwenikweni. Koma panopa, tikamaphunzira Baibulo, zimandikhudza kwambiri, makamaka zimene limanena pa nkhani yokhudza makhalidwe.”
◼ United States: Pamene banja lina linkalalikira pogwiritsa ntchito dongosolo lapadera lolalikira m’malo opezeka anthu ambiri, anakumana ndi mayi wina wa ku Taiwan amene ankakhulupirira Mulungu koma ankaona kuti Baibulo ndi buku la azungu. Ngakhale kuti mayiyo anali wolemera, ankaona kuti alibe moyo wosangalala, ndipo anafika patebulo limene banjali linaikapo mabuku. Anaona kuti mwina Baibulo lingamuthandize kukhala ndi moyo wosangalala. Banjalo linayamba kuphunzira naye pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso kabuku kakuti Lasting Peace and Happiness—How to Find Them. M’malo mophunzira naye mutu 2 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, anaphunzira naye mutu wa m’kabukuka, womwe umanena za mmene Baibulo lingathandizire anthu pa nkhani zosiyanasiyana. Ataphunzira naye ndime 6 pa mutu umenewu, mayiyo anachita chidwi kwambiri ndi zimene anaphunzirazo moti ananena kuti Baibulo ndi lapadera kwambiri kuposa mabuku onse achipembedzo. Komanso ataphunzira maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa, mayiyo anati: “Ndikuona kuti palibenso buku lina lolondola ngati Baibulo.”
◼ Japan: M’bale wina anapitirizabe kumapita kwa munthu wina n’kumacheza naye mwachidule, ngakhale kuti munthuyo ananena kuti sakhulupirira Mulungu. M’baleyo ankakambirana naye nkhani za mu Galamukani! za mutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” Patapita nthawi, munthuyo anasintha maganizo ndipo anayamba kuvomereza kuti n’kuthekadi kuti Mulungu alipo. Panopa munthuyu amakhulupirira zoti kuli Mulungu ndipo m’baleyo akuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu.
◼ Canada: Mayi wina analandira magazini atsopano amene mlongo wina anamupatsa pamene ankatuluka m’nyumba kupita m’galimoto yake. Pamene mlongoyo anapitanso kwa mayiyu, anakana kwamtuwagalu kuti sakufuna kukambirana naye chifukwa sakhulupirira Mulungu. Komabe mlongoyo sanagwe mphwayi ndipo anaganiza zomupititsiranso kabuku kakuti, Moyo Wokhutiritsa Mmene Mungaupezere. Atafika kunyumba kwa mayiyu, anamuuza kuti akudziwa kuti sakhulupirira kuti kuli Mulungu komabe anaganiza zobweranso chifukwa anazindikira kuti mayiyo akulera yekha ana ake. Ndiyeno anasonyeza mayiyo ndime 6, patsamba 4 m’kabukuka. Ndimeyi imanena kuti tiyenera kupeza malangizo abwino olerera ana. Kenako anamulimbikitsa kuti awerenge mutu 2 umene umanena za kulera ana. Mayiyo anasangalala kwambiri ndipo analandira kabukuko.