Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Omwe Sadziwa Kuwerenga Komanso Amene Amavutika Kuwerenga?
1. Kodi timakumana ndi mavuto otani tikapeza anthu omwe sadziwa kwenikweni kuwerenga?
1 Nthawi zina tikakhala mu utumiki, timapeza anthu achidwi koma osadziwa kwenikweni kuwerenga. Anthuwa amachita manyazi tikawauza kuti awerenge Baibulo kapena mabuku athu. Kungofikira kupatsa anthu oterewa buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani sikungathandize kwenikweni. Ndiye kodi tingawathandize bwanji? Tinafunsa ofalitsa aluso ochokera m’mayiko 20 kuti atiuze zimene amachita. Anthuwa anafotokoza mfundo zotsatirazi.
2. Kodi tingagwiritse ntchito zinthu ziti pothandiza anthu amene amawerenga movutikira?
2 Ngati munthuyo satha kuwerenga kapena amawerenga movutikira, mungayambe ndi kabuku ka Mverani Mulungu kapena ka Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Mpainiya wina wa ku United States amaonetsa munthu timabuku tiwiri tonseti, n’kumuuza kuti asankhe kamene akufuna akambirane. Ofesi ya nthambi ya ku Kenya inanena kuti timabuku timeneti ndi tothandiza kwambiri kwa anthu a kumeneko. Ofesiyi inanena kuti izi zili choncho chifukwa anthu ambiri a ku Africa anazolowera kuphunzira zinthu pofotokozeredwa nkhani m’malo mokambirana pogwiritsa ntchito mafunso ndi mayankho. Zimakhala zosavuta kwa munthu amene anaphunzira tikamupempha kuti awerenge kenako n’kumufunsa funso. Koma anthu ena omwe sanaphunzire kwenikweni, samasuka tikamagwiritsa ntchito njira imeneyi. Choncho pofuna kuthandiza anthu oterewa, ofalitsa ena amakonda kuyamba ndi kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kapena kakuti, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu kapenanso Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.
3. Kodi tiyenera kudziwa zinthu ziti zomwe zingatithandize kuti tiziphunzitsa bwino anthu osadziwa kuwerenga?
3 Muziwayamikira: Anthu amene sadziwa kuwerenga amachita manyazi komanso amadzikayikira. Choncho chinthu choyamba chomwe tingachite n’kuwathandiza kukhala omasuka. Nthawi zambiri anthu oterewa amakhala anzeru ndipo akhoza kuphunzira. Ndiye muziyesetsa kuwapatsa ulemu ndipo muziwasonyeza kuti ndi ofunika. (1 Pet. 3:15) Anthu oterewa akaona kuti akuchita bwino komanso zomwe akuphunzira zikuwathandiza, amapitiriza kuphunzira. Choncho muziwayamikira akamachita bwino.
Anthu amene sadziwa kuwerenga amachita manyazi komanso amadzikayikira. Choncho chinthu choyamba chomwe tingachite n’kuwathandiza kukhala omasuka
4. Kodi mungathandize bwanji anthu amene amavutika kuwerenga kuti azikonzekera phunziro?
4 Mungachite bwino kulimbikitsa munthuyo kuti azikonzekera phunziro ngakhale kuti amavutika kuwerenga. Ofalitsa ena a ku South Africa amauza ophunzira awo kuti azipempha munthu wina amene amadziwa bwino kuwerenga kuti aziwawerengera. M’bale wina wa ku Britain amapatsa ophunzira ake kwa nthawi yochepa buku lake lomwe wakonzekera. Iye amachita zimenezi kuti ophunzirawo aone kuti zimakhala zosavuta kupeza mayankho ngati wadula mizere m’munsi mwa yankho. M’bale wina wa ku India amauza ophunzira ake kuti aziona komanso kuganizira zithunzi za m’nkhani yomwe adzaphunzire mlungu wotsatira.
5. Tikamachititsa phunziro, kodi tingasonyeze bwanji kuleza mtima?
5 Muzileza Mtima: Kaya mukugwiritsa ntchito kabuku kati, muzikambirana mfundo zazikulu zokha ndipo muzithandiza wophunzira wanuyo kumvetsa mfundozo. Ngati mwangoyamba kumene, zingakhale bwino kuti muziphunzira nthawi yochepa, mwina mphindi 10 kapena 15 basi. Musamaphunzire zinthu zambirimbiri nthawi imodzi, muyenera kungophunzira ndime zochepa basi. Muzileza mtima wophunzirayo akamachedwa powerenga. Akayamba kukonda Yehova, angayambenso kuyesetsa kuti aziwerenga bwino. Kuti mum’thandize kuchita zimenezi, ndi bwino kumuitanira kumisonkhano ya mpingo mukangoyamba kuphunzira naye.
6. Kodi tingathandize bwanji ophunzira athu kuti adziwe kuwerenga?
6 Ophunzira Baibulo akadziwa kuwerenga, amapita patsogolo msanga mwauzimu. (Sal. 1:1-3) Ofalitsa ambiri amathandiza ophunzira awo kuwerenga pogwiritsa ntchito kabuku kakuti, Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba, ndipo amachita zimenezi kwa mphindi zingapo akamaliza phunziro. Ngati wophunzirayo wayamba kugwa ulesi, muuzeni zinthu zimene akuchita bwino. Zimenezi zingamulimbikitse kuti apitirize kuphunzira. Muzimutsimikizira kuti Yehova adalitsa khama lake ndipo mulimbikitseni kuti azipempha Yehovayo kuti amuthandize. (Miy. 16:3; 1 Yoh. 5:14, 15) Ofalitsa ena amalimbikitsa ophunzira awo kuti ayambe ndi zinthu zing’onozing’ono monga kuphunzira afabeti, kupeza malemba m’Baibulo ndipo kenako kuwerenga timabuku tosavuta. Nthawi zambiri musanayambe kuphunzitsa munthu kuwerenga, muyenera kumuthandiza kaye kuti adziwe kufunika kowerenga.
7. N’chifukwa chiyani si bwino kulephera kuphunzitsa munthu Baibulo chifukwa choti sadziwa kuwerenga kapena sawerenga bwino?
7 Yehova saona kuti anthu amene sanaphunzire ndi osafunika. (Yobu 34:19) Iye amaona mtima wa munthuyo. (1 Mbiri 28:9) Choncho musalephere kuphunzitsa munthu Baibulo chifukwa choti sadziwa kuwerenga kapena sawerenga bwino. Monga taonera, pali timabuku tambiri timene mungagwiritse ntchito kuti muyambe kuphunzira naye. Kenako mungasinthe phunzirolo n’kuyamba kuphunzira naye buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kuchita zimenezi kungathandize wophunzirayo kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa.