Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Tiziuza Anthu Zokhudza Ufumu Molimba Mtima
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Lemba la 2 Timoteyo 1:7, 8, limatilimbikitsa kuti tizilalikira molimba mtima. Choncho potsatira malangizo amenewa tiyenera kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu molimba mtima. Komano kodi tingachite bwanji zimenezi?
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Ganizirani munthu amene mukufuna kumuuza za Ufumu. Kenako pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kuti muthe kulankhula ndi munthuyo molimba mtima.