Buku Lothandiza Kufufuza Nkhani
Ofalitsa ambiri amagwiritsa ntchito buku lachingelezi lakuti, Watch Tower Publications Index pofufuza nkhani. Koma bukuli limangopezeka m’zinenero zochepa. Choncho panatuluka buku lina lotithandiza kufufuza la mutu wakuti, Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. Bukuli likupezeka m’zinenero 170. Malifalensi omwe ali m’bukuli ndi oyambira m’chaka cha 2000. Bukuli silinasindikizidwe m’zinenero zomwe zili ndi buku la Watch Tower Publications Index, komabe likupezeka m’zinenerozo pa Watchtower Library ya pakompyuta komanso pa Laibulale ya pa Intaneti ya Watchtower. Buku latsopanoli lingakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso a m’Baibulo, kupeza mfundo zomwe mungagwiritse ntchito pa moyo wanu komanso pokonzekera misonkhano ya mpingo ndi kulambira kwa pabanja.