Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda February 1
“Tabwera kuti tikupatseni kapepala aka. Kapepala kameneka kakufotokoza mmene malangizo a m’Baibulo angatithandizire. Kapepala kanu ndi aka. [Apatseni kapepala kakuti, Kodi Baibulo Mumalikhulupirira?] Anthu ena amafuna kudziwa ngati m’Baibulo angapezemo malangizo omwe angawathandize pa ntchito yawo. Taonani zimene lemba ili limanena pa nkhani ya ntchito. [Werengani Mlaliki 3:13.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize kuti tizisangalala ndi ntchito yathu.”
Galamukani! February
“Tabwera kuti tikambirane nanu mwachidule nkhani yomwe ili mu Galamukani! ya mwezi uno. Magaziniyi ili ndi yankho la funso ili. [Musonyezeni funso lomwe lili pachikuto cha Galamukani! ya February.] Ndikufuna kumva maganizo anu palemba ili. [Werengani Miyambo 29:11.] Kodi mfundo imeneyi ndi yothandiza masiku ano? [Yembekezerani ayankhe.] Magaziniyi ikutchula mfundo 4 za m’Baibulo ndipo ikufotokoza mmene mfundozi zingatithandizire pa moyo wathu.”