Kodi Tingatani Kuti Tiziwafika pa Mtima Anthu Amene Timaphunzira Nawo?
1. Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa zinawakhudza bwanji omvera ake?
1 Yesu Khristu ankawafika pamtima anthu amene ankawalalikira. Pa nthawi ina, mitima ya ophunzira ake ‘inanthunthumira’ atawafotokozera Malemba momveka bwino. (Luka 24:32) Popeza kuti kumvera kumachokera mumtima, kodi tingatani kuti tiziwafika pamtima ophunzira athu kuti asinthe n’kuyamba kutumikira Mulungu?—Aroma 6:17.
2. Kodi kuchita zinthu mozindikira komanso mwaluso kungathandize bwanji kuti tizifika pamtima anthu amene timaphunzira nawo?
2 Muzichita Zinthu Mozindikira Komanso Mwaluso: Anthu ambiri sasintha mukangowauza kuti izi n’zolakwika ndipo zolondola ndi izi. Komanso kuwawerengera malemba ambirimbiri osonyeza kuti chipembedzo chawo chimaphunzitsa zabodza, kungangopangitsa kuti asiye kuphunzira. Ndiye kodi tingatani kuti tiwathandize? Tiyenera kudziwa zimene zimawachititsa kuti azikhulupirira komanso kuchita zinazake. Kuti tidziwe zimenezi, tiyenera kuwafunsa mafunso amene angathandize kuti anene maganizo awo. (Miy. 20:5) Tikamva maganizo awowo, tingadziwe malemba amene tingawawerengere kuti tiwafike pamtima. Choncho tiyenera kukhala oleza mtima komanso tiyenera kumvetsera akamafotokoza maganizo awo. (Miy. 25:15) Kumbukirani kuti anthu ena amasintha mofulumira ndipo ena amatenga nthawi kuti asinthe. Komanso dziwani kuti mzimu wa Yehova ndi umene ungathandize munthu kuti asinthe zochita ndiponso maganizo ake.—Maliko 4:26-29.
3. Kodi tingathandize bwanji anthu amene timaphunzira nawo kuti akhale ndi makhalidwe abwino?
3 Athandizeni Kuti Akhale Ndi Makhalidwe Abwino: Nkhani za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti Mulungu ndi wabwino komanso ndi wachikondi, zingamuthandize munthu amene tikuphunzira naye kukhala ndi makhalidwe abwino. Tingamuwerengere malemba ngati Salimo 139:1-4 kapena Luka 12:6, 7 pomusonyeza kuti Mulungu amakonda aliyense. Munthu akayamba kukhala ndi mtima woyamikira zinthu zabwino zimene Yehova wamuchitira, amayamba kumukonda ndipo amadzipereka kwa iye. (Aroma 5:6-8; 1 Yoh. 4:19) Komanso akadziwa kuti Yehova amasangalala kapena kukhumudwa ndi khalidwe lake, angayambe kuchita zinthu zimene zimasangalatsa ndiponso kulemekeza Yehovayo.—Sal. 78:40, 41; Miy. 23:15.
4. Tikamaphunzitsa anthu Baibulo, kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza ufulu wawo wosankha?
4 Yehova sakakamiza aliyense kuti azimvera malamulo ake. Koma amangotiuza zotsatira zabwino zomwe zingakhalepo tikamvera malamulo ake, ndipo zimakhala kwa ife kumvera kapena ayi. (Yes. 48:17, 18) Ifenso tizitsanzira Yehova pa nkhani imeneyi. Tiziphunzitsa anthu m’njira yoti asankhe okha kutsatira zimene akuphunzirazo kapena ayi. Munthu akaona yekha kufunika koti asinthe, amasinthadi ndipo amatumikira Yehova mpaka kalekale. (Aroma 12:2) Amayambanso kukonda kwambiri Yehova yemwe “amayesa mitima.”—Miy. 17:3.