Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 September tsamba 3
  • ‘Muzitsatira Chilamulo cha Yehova’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Muzitsatira Chilamulo cha Yehova’
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Khulupirirani Mawu a Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Lolani Kuti Mawu a Mulungu Aunike Njira Yanu
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kodi Mumawakonda Motani Mawu a Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Ha! Ndikondadi Chilamulo Chanu”
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 September tsamba 3

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MASALIMO 119

‘Muzitsatira Chilamulo cha Yehova’

Kutsatira chilamulo cha Yehova kumatanthauza kumvera chilichonse chimene Yehova amatiuza. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe ankadalira Yehova komanso kutsatira chilamulo chake ngati mmene wamasalimo anachitira.

Wamasalimo ankagwiritsa ntchito ndodo akamayenda

Kutsatira chilamulo cha Yehova n’kumene kumatichititsa kukhalabe osangalala

119:1-8

Yoswa akuwerenga mpukutu

Yoswa ankadalira kwambiri Yehova akamachita zinthu. Ankadziwa kuti ankayenera kumadalira Yehova ndi mtima wake wonse kuti akhale wosangalala komanso kuti zinthu zizimuyendera bwino

Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tikhale olimba mtima tikamakumana ndi mavuto

119:33-40

Yeremiya akupemphera

Yeremiya anali wolimba mtima komanso ankadalira Yehova pamene ankakumana ndi mavuto. Iye ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo sanasiye kuchita utumiki wake

Kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti tizilalikira molimba mtima

119:41-48

Paulo akulalikira Bwanamkubwa Felike

Paulo sankachita mantha kulalikira uthenga wochokera kwa Mulungu kwa munthu aliyense. Pamene ankalalikira uthenga wabwino kwa Bwanamkubwa Felike, iye ankakhulupirira kuti Yehova amuthandiza

Wamasalimo ankagwiritsa ntchito ndodo akamayenda

Kodi ndi pa nthawi iti pamene ndingasonyeze kulimba mtima ndikamalalikira?

  • Kusukulu

  • Kuntchito

  • Achibale

  • Anthu Ena

Salimo 119 linalembedwa motsatira zilembo za afabeti. N’kutheka kuti zimenezi zinkathandiza anthu kuti asamaiwale mawu a m’Salimoli. Salimoli lili m’zigawo 22 ndipo chigawo chilichonse chili ndi mavesi 8. Vesi lililonse m’zigawozi limayamba ndi chilembo chofanana cha afabeti ya Chiheberi. Ndiye popeza afabeti ya Chiheberi ili ndi zilembo 22, Salimo 119 lili ndi mavesi 176 ndipo ndi limene lili lalitali kwambiri kuposa masalimo onse m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena