Mofanana ndi bwana amene amauza sekilitale wake kuti amulembere uthenga winawake, Mulungu anagwiritsa ntchito anthu okhulupirika kuti alembe Malemba Opatulika
Kodi Mlengi Wathu Amatithandiza Bwanji Kudziwa Malonjezo Ake?
Kungoyambira pamene anthu oyamba analengedwa, Mlengi wathu wakhala akugwiritsa ntchito angelo komanso aneneri pouza anthu malonjezo ake. Kuwonjezera pamenepa, iye anasankha kuti uthenga ndi malonjezo ake zilembedwe. Mulungu akutilonjeza kuti m’tsogolomu tidzasangalala. Ndiye kodi masiku ano malonjezo a Mulungu tingawapeze kuti?
Uthenga wochokera kwa Mulungu umapezeka m’Malemba Opatulika. (2 Timoteyo 3:16) Kodi Mulungu anathandiza bwanji aneneri kuti alembe uthenga wake? (2 Petulo 1:21) Mulungu anaika maganizo ake m’mitima ya amuna osiyanasiyana. Kenako iwo analemba maganizo a Mulunguwo. Zimenezi n’zofanana ndi zomwe zimachitika masiku ano. Mwachitsanzo, bwana akafuna kulemba uthenga winawake, amauza sekilitale wake kuti amulembere uthengawo, ndipo ife tikaulandira timaona kuti wachokera kwa bwanayo osati kwa sekilitale wake. Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti Mulungu anagwiritsa ntchito amuna osiyanasiyana kuti alembe uthenga wake, Mlembi weniweni wa Malemba Opatulika ndi iyeyo.
MAWU A MULUNGU AKUPEZEKA M’ZINENERO ZAMBIRI
Mawu a Mulungu ndi ofunika kwambiri, ndipo iye amafuna kuti anthu onse aziwawerenga ndi kuwamvetsa bwino. Masiku ano, “uthenga wabwino wosatha” ukupezeka mosavuta ku “dziko lililonse, fuko lililonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chivumbulutso 14:6) Mulungu wachititsa kuti buku la Malemba Opatulika lathunthu kapena mbali yake ina lipezeke m’zinenero zoposa 3,000, kuposa buku lina lililonse padziko lapansi.