Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp20 No. 3 tsamba 14-15
  • Mukhoza Kusangalala ndi Madalitso Ochokera kwa Mlengi Wathu Mpaka Kalekale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukhoza Kusangalala ndi Madalitso Ochokera kwa Mlengi Wathu Mpaka Kalekale
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zozizwitsa za Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Yesu Amakonda Anthu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2020
wp20 No. 3 tsamba 14-15
Anthu osiyanasiyana akucheza mosangalala m’dziko latsopano.

“Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake. Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.”​—SALIMO 67:6

Mukhoza Kusangalala ndi Madalitso Ochokera kwa Mlengi Wathu Mpaka Kalekale

Mulungu analonjeza mneneri Abulahamu kuti “mitundu yonse yapadziko lapansi” idzapeza madalitso kudzera mwa mmodzi mwa mbadwa zake. (Genesis 22:18) Kodi ndi ndani anadzakhala mbadwa imeneyi?

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Mulungu anapatsa Yesu, yemwe anali mbadwa ya Abulahamu, mphamvu zochita zozizwitsa zikuluzikulu. Zozizwitsa zimene anachitazi zinasonyeza kuti kudzera mwa Yesu, anthu amitundu yonse adzalandira madalitso amene Mulungu analonjeza Abulahamu.​—Agalatiya 3:14.

Zozizwitsa zimene Yesu anachita zinathandiza anthu kuzindikira kuti iye ndi amene Mulungu anamusankha kuti adzadalitse anthu. Zinasonyezanso mmene Mulungu adzamugwiritsire ntchito podalitsa anthu mpaka kalekale. Taonani mmene zozizwitsa zimene Yesu anachita zikusonyezera makhalidwe ake ena ochititsa chidwi.

Ankachita zinthu mwachikondi—Yesu anachiritsa odwala.

Nthawi ina munthu wina wakhate anachonderera Yesu kuti amuchiritse. Yesu anamukhudza ndi kumuyankha kuti: “Ndikufuna.” Nthawi yomweyo khatelo linatha.​—Maliko 1:40-42.

Anali wopatsa​—Yesu anadyetsa anthu anjala.

Yesu sanafune kuti anthu abwerere kwawo ali ndi njala. Kawiri konse iye anadyetsa anthu masauzande ambirimbiri pochulukitsa mitanda ya mkate yochepa ndi tinsomba tochepa. (Mateyu 14:17-21; 15:32-38) Anthuwo atadya, onse anakhuta ndipo chakudya chinatsala chambirimbiri.

Anali wachifundo​—Yesu anaukitsa akufa.

Mwana wamwamuna mmodzi yekha wa mkazi wamasiye atamwalira, Yesu “anawamvera chifundo” mayiwo ndipo anaukitsa mwanayo chifukwa anali yekhayo amene akanawasamalira.​—Luka 7:12-15.

ANTHU ADZALANDIRA MADALITSO OSATHA PADZIKO LAPANSI

Yesu anasonyeza kale kuti Mulungu ali ndi mphamvu zodalitsira anthu. Posachedwapa Yesu akadzabweranso monga mmene analonjezera, Mulungu adzamugwiritsa ntchito pochita zozizwitsa zazikulu padzikoli kuposa zimene anachitapo.

Kodi moyo udzakhala wotani padzikoli Mulungu akadzakwaniritsa lonjezo lake limene anauza Abulahamu? Anthu amene amakonda ndi kulemekeza Mulungu “adzalandira dziko lapansi ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” (Salimo 37:11) “Imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”​—Chivumbulutso 21:4.

Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala mwamtendere padziko lapansi kwamuyaya. Kuti mudziwe zambiri zokhudza madalitso amene ulamuliro wa Mulungu udzabweretse posachedwapa, tikukupemphani kuti mupite pa www.jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena