Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb18 April tsamba 7
  • Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Tiziphunzitsa Mfundo za Choonadi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Zimene Tinganene
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Zimene Tinganene
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18 April tsamba 7

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizigwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa

Akulalikira pogwiritsa ntchito Baibulo ndi kabuku

Kupanga ophunzira kuli ngati kumanga nyumba. Kuti munthu amange nyumba amafunika kuphunzira mmene angagwiritsire ntchito mwaluso zida zake zomangira. Nafenso tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito mwaluso chida chathu chachikulu chomwe ndi Baibulo. (2 Tim. 2:15) Tiyeneranso kumagwiritsa ntchito bwino mabuku ndi mavidiyo omwe timagwiritsa ntchito pophunzitsa n’cholinga choti tipange ophunzira.a

Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito mwaluso Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa? (1) Pemphani woyang’anira kagulu kanu kuti akuthandizeni, (2) muzilalikira limodzi ndi ofalitsa aluso kapena apainiya, komanso (3) muziyeserera nthawi zonse. Mukamagwiritsa ntchito mabuku komanso mavidiyo athu mwaluso, muzisangalala kwambiri kugwira ntchito yomanga mwauzimu yomwe ikuchitika masiku ano.

MAGAZINI

Nsanja ya Olonda
Galamukani!

TIMABUKU

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu

MABUKU

Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukondani’?

TIMAPEPALA

Kodi Baibulo mumalikhulupirira?
Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji m’tsogolo?
Kodi n’chiyani chingathandize kuti banja likhale losangalala?
Kodi ndani kwenikweni akulamulira dziko?
Kodi mavuto amene tikukumana nawowa adzathadi?
Kodi n’zoonadi kuti akufa adzauka?
Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?
Kodi tingapeze kuti mayankho a mafunso ofunika kwambiri okhudza moyo?

MAVIDIYO

N’chifukwa chiyani muyenera kuphunzira Baibulo?
Kodi phunziro la Baibulo limachitika bwanji?
Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani?
Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?

TIMAPEPALA TOITANIRA

Kapepala Koitanira Anthu Kumisonkhano

MAKADI

Khadi lodziwitsa anthu

a Pali mabuku ena omwe sali m’gulu la Zinthu Zomwe Timagwiritsa Ntchito Pophunzitsa, omwe analembedwera anthu ena. Mukhoza kugwiritsa ntchito mabuku amenewa ngati pakufunika kutero.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena