CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 9-10
Masomphenya Olimbitsa Chikhulupiriro
Taganizirani mmene Yesu anamvera pa nthawi ya kusandulika kwake, pamene Atate ake ananena kuti amakondwera naye! N’zosachita kufunsa kuti zimenezi zinamulimbikitsa kuti apirire mayesero omwe ankayembekezera kukumana nawo. Masomphenyawa analimbikitsanso Petulo, Yakobo ndi Yohane. Iwo anaona kuti Yesu ndi Mesiyadi ndipo ankachita bwino kumumvera. Patadutsa zaka 32 kuchokera nthawi imeneyi Petulo anatchula za masomphenya omwe anaonawa ndipo ananena kuti anamulimbikitsa kuti azikhulupirira kwambiri ‘mawu aulosi.’—2 Pet. 1:16-19.
Ngakhale kuti ifeyo sitinaone nawo masomphenyawa, timaona kukwaniritsidwa kwake masiku ano. Panopa Yesu akulamulira monga Mfumu yamphamvu. Posachedwapa ‘apambana pa nkhondo yolimbana’ ndi adani ake, ndipo zimenezi zidzabweretsa dziko latsopano lolungama.—Chiv. 6:2.
Kodi kukwaniritsidwa kwa maulosi a m’Baibulo kumalimbitsa bwanji chikhulupiriro chanu?