MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Yehova Akuthandiza Kuti Ukhale Wolimba Mtima
Ngati muli pasukulu, kodi nthawi zina mumachita mantha kulalikira kapena kuwauza anthu ena kuti ndinu wa Mboni za Yehova? Ngati ndi choncho, kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti ‘muzilimba mtima’ kuuza ena za Yehova? (1 Ates. 2:2) Ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi? Onerani vidiyo yakuti Yehova Akuthandiza Kuti Ukhale Wolimba Mtima, kenako yankhani mafunso otsatirawa:
Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chomwe chinathandiza Sofiya kukhala wolimba mtima?
Kodi kuyeserera zoti akalankhule kunamuthandiza bwanji Sofiya?
N’chifukwa chiyani muyenera kumalalikira kwa anzanu akusukulu?
Ngati simuli pasukulu, kodi mwaphunzira zotani m’vidiyoyi?