CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 11-12
Muzitsanzira Yesu pa Nkhani Yochitira Ena Chifundo
Kodi n’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti Yesu ankachitira kwambiri chifundo anthu ena?
Ngakhale kuti sanakumanepo ndi mavuto onse omwe anthu ankakumana nawo, iye ankadziyerekezera kuti ndi munthu winayo n’kumamva ululu umene munthuyo akumva
Iye sanachite manyazi kulira pagulu
Akaona anthu akuvutika ankachitapo kanthu n’kuwathandiza