CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 13-14
“Ndakupatsani Chitsanzo”
Pamene Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake, anawaphunzitsa kuti akhale odzichepetsa komanso azigwira ntchito zooneka zotsika pothandiza abale awo.
Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndine wodzichepetsa . . .
ndikasemphana maganizo ndi anthu ena?
ena akandipatsa malangizo?
ndikamagwira nawo ntchito yosamalira kapena kukonza Nyumba ya Ufumu?