MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziyesetsa Kumvetsa Nkhani Yonse
Mukamawerenga nkhani za m’Baibulo, muziyesetsa kumvetsa nkhani yonse. Dziwani mmene zinthu zinalili pa nthawi yomwe nkhaniyo inkachitika, anthu otchulidwa mu nkhaniyo, komanso zimene zinawachititsa kuchita zomwe anachitazo. M’maganizo mwanu, onani malo omwe kunkachitikira nkhaniyo, phokoso lomwe linkamveka, fungo lomwe linkamveka, komanso mmene anthu a m’nkhaniyo ankamvera.
ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI MUZIYESETSA KUMVETSA ZIMENE MUMAWERENGA M’BAIBULO NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa kuti pakhale kusamvana pakati pa Yosefe ndi azichimwene ake?
Kodi ndi zinthu ziti zimene zinkachititsa kuti azichimwene ake a Yosefe azichita zinthu mosaganiza bwino nthawi zina?
Kodi Malemba amatiuza zotani zokhudza Yakobo, bambo ake a Yosefe?
Kodi Yakobo anapereka chitsanzo chotani kwa ana ake pa nkhani yothetsa kusamvana?
Kodi vidiyoyi yakuthandizani bwanji?