Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 January tsamba 11
  • Sankhani Kutumikira Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sankhani Kutumikira Yehova
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kuti Mukhale Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Munthu Ayenera Kubatizidwa Kuti Akhale Mkhristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Kukwaniritsa Zimene Zimafunika Paubatizo Wachikristu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Ubatizo Umatithandiza kuti Tikhale pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 January tsamba 11
Njira yokhotakhota yoimira kutumikira Yehova. Zikwangwani zomwe zili m’njirayi zikuimira kuphunzira Baibulo, kusonkhana, kulalikira komanso kubatizidwa.

Kodi inuyo muli pati pa ulendo wanu wokabatizidwa?

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Sankhani Kutumikira Yehova

Ngati ndinu wachinyamata ndipo simunabatizidwe kapena ngati mukuphunzira Baibulo, kodi muli ndi cholinga chofuna kubatizidwa? N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi cholinga choti mubatizidwe? Munthu akadzipereka komanso kubatizidwa amakhala pa ubwenzi wapadera ndi Yehova (Sl 91:1) Amakhalanso ndi mwayi wodzapulumuka. (1Pe 3:21) Ndiye kodi mungatani kuti mudzipereke komanso kufika pobatizidwa?

Muyenera kutsimikizira kuti chimene mukuphunzira ndi choonadi. Mukakhala ndi mafunso muzifufuza kuti mupeze mayankho. (Aro 12:2) Muziganizira mbali zimene mukufunika kusintha, ndipo muzisintha chifukwa chofuna kukondweretsa Yehova. (Miy 27:11; Aef 4:​23, 24) Nthawi zonse muzipemphera kwa iye kuti azikuthandizani. Musamakayikire kuti Yehova adzakuthandizani ndi mzimu wake woyera, womwe ndi wamphamvu. (1Pe 5:​10, 11) Musamaganize kuti n’kungotaya nthawi kuchita khama kuti muyenerere kubatizidwa. Kutumikira Yehova ndi chinthu chabwino kwambiri kuposa chilichonse.​—Sl 16:11.

ONERANI VIDIYO YAKUTI, ZIMENE MUNTHU ANGACHITE KUTI ABATIZIDWE NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi anthu ena anafunika kulimbana ndi mavuto ati kuti abatizidwe?

  • Kodi mungatani kuti mukhale ndi chikhulupiriro chomwe chingakuthandizeni kuti mudzipereke kwa Yehova?

  • Kodi n’chiyani chinachititsa ena kuti achite zinthu zomwe zinawathandiza kuti ayenerere kubatizidwa?

  • Kodi anthu amene amasankha kutumikira Yehova amapeza madalitso otani?

  • Kodi kudzipereka komanso kubatizidwa zimatanthauza chiyani?

Kumapeto kwa nkhani ya ubatizo, wokamba nkhaniyo amapempha amene akufuna kubatizidwa kuti aimirire n’kuyankha mokweza mafunso awiri otsatirawa:

Kodi munalapa machimo anu, kudzipereka kwa Yehova komanso kuvomereza njira yake yopulumutsira anthu kudzera mwa Yesu?

Kodi mukudziwa kuti mukabatizidwa muzidziwika kuti ndinu wa Mboni za Yehova komanso kuti muli m’gulu lake?

Akayankha mafunso amenewa kuti inde, amakhala kuti ‘akulengeza poyera’ kuti amakhulupirira dipo ndipo anadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse.​​—Aro 10:​9, 10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena