Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsamba 9
  • Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mwakonzekera?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana Ndi Zachiwawa?
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Mavuto Azachuma?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 May tsamba 9
Banja likusunga chakudya, madzi, komanso zinthu zina pokonzekera ngozi zogwa mwadzidzidzi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”

Pamene tili kumapeto kwa “masiku otsiriza” ano, mavuto amene tikukumana nawo aziwonjezereka. (2Ti 3:1; nwtsty mfundo yothandiza pophunzira Mt 24:8) Kukachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, nthawi zambiri anthu a Yehova amalandira malangizo mwamsanga omwe akhoza kupulumutsa moyo wawo. Kuti tidzapulumuke kukadzachitika ngozi zadzidzidzi m’tsogolo, tikufunika kukonzekera panopa, mwakuthupi komanso mwauzimu.​—Lu 16:10.

  • Konzekerani mwauzimu: Khalani ndi dongosolo labwino lochitira zinthu zauzimu. Phunzirani njira zosiyanasiyana zolalikirira. Musade nkhawa ngati kwa kanthawi simukutha kuchitanso zinthu limodzi ndi mpingo wanu. (Yes 30:15) Muzikumbukira kuti Yehova komanso Yesu ali nanu nthawi zonse.​—od 176 ¶15-17

  • Konzekerani mwakuthupi: Kuwonjezera pa kukhala ndi chikwama chomwe muli zinthu zofunika zomwe mungatenge ngati patachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, banja lililonse liyenera kusunga chakudya chokwanira, madzi, mankhwala, komanso zinthu zina zomwe lingagwiritse ntchito ngati patafunika kuti lisachoke panyumba kwa nthawi yayitali ndithu.​—Miy 22:3; g17.5 4, 6

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGACHITE POKONZEKERA MASOKA ACHILENGEDWE, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Zimene Tingachite Pokonzekera Masoka Achilengedwe.’ M’bale akuwerenga Baibulo.

    Kodi tingakonzekere bwanji mwauzimu masoka asanachitike?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Zimene Tingachite Pokonzekera Masoka Achilengedwe.’ Chikwama, manambala a foni, komanso mapu osonyeza kumene banja lingakumane ngati patachitika ngozi.

    N’chifukwa chiyani tiyenera . . .

    • kumalankhula ndi akulu nthawi zonse?

    • kukhala ndi zinthu zomwe tingazigwiritse ntchito pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi?

    • kukambirana mitundu ya masoka omwe angachitike komanso zimene tingachite masokawo akachitika?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Zimene Tingachite Pokonzekera Masoka Achilengedwe.’ Njira zomwe tingathandizire ena pakachitika ngozi. 1. M’bale akuwapempherera. 2. Abale ongodzipereka akugwira nawo ntchito yopereka thandizo kwa anthu okhudzidwa. 3. M’bale akupereka ndalama zothandizira pa ntchito ya padziko lonse.

    Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tingachite pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi tsoka linalake?

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mliri wa COVID-19 wandiphunzitsa chiyani pa nkhani yokhala wokonzeka?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena