Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 May tsamba 11
  • Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula Mwaumoyo
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muziwafika Pamtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 May tsamba 11
M’bale akumwetulira komanso kugwiritsa ntchito manja pophunzira Baibulo ndi munthu wachikulire.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse

Kuphunzitsa ndi mtima wonse kumachititsa kuti anthu amene tikuwaphunzitsa azimvetsera mwatcheru. Kumasonyezanso kuti timaona kuti uthenga wathu ndi wofunika. Tonsefe tingathe kumaphunzitsa ndi mtima wonse, posatengera komwe tinakulira kapena mmene tilili. (Aro 12:11) Tingachite bwanji zimenezi?

Choyamba, muziganizira kufunika kwa uthenga wanu. Muli ndi mwayi wolengeza “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Aro 10:15) Chachiwiri, muziganizira mmene uthenga wabwino ungathandizire omvera anu. Iwo akufunika kumva uthenga wanu. (Aro 10:13, 14) Chomaliza, muzisonyeza kuti nkhaniyo yakufikani pamtima ndipo manja ndi nkhope yanu zizisonyeza mmene mukumvera mumtima.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​—MUZIPHUNZITSA NDI MTIMA WONSE, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muziwonjezera Luso Lanu Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse.’ Anita akuoneka wokhumudwa Jane atamuuza kuti sakwanitsa kuphunzira Baibulo pa tsiku limeneli.

    Kodi n’chiyani chinachititsa Anita kuti asiye kuphunzitsa Janendi mtima wonse?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muziwonjezera Luso Lanu Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse.’ Jane akuona osasangalala pamene akuphunzira Baibulo.

    Kodi n’chiyani chinathandiza Anita kuti ayambirenso kuphunzitsa Jane ndi mtima wonse?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muziwonjezera Luso Lanu Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse.’ Jane ndi Anita akucheza mosangalala pambuyo pa phunziro la Baibulo.

    Kuphunzitsa ndi mtima wonse kumathandiza anthu

    N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira kwambiri za makhalidwe abwino a omvera athu?

  • Kodi kuphunzitsa ndi mtima wonse kungathandize bwanji amene timawaphunzitsa Baibulo komanso anthu ena?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena