MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Uziona Akazi Achikulire Ngati Amayi Ako, Akazi Achitsikana Ngati Alongo Ako
Malemba amatiuza kuti tiziona Akhristu achikulire ngati amayi ndi abambo athu komanso tiziona Akhristu achinyamata ngati abale athu. (Werengani 1 Timoteyo 5:1, 2.) Makamaka abale, ayenera kumachita zinthu mwaulemu ndi alongo.
M’bale sayenera kukopa kapena kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti mlongo asakhale womasuka. (Yob 31:1) M’bale wosakwatira sayenera kuseweretsa maganizo a mlongo wosakwatiwa pomuchititsa kuganiza kuti akufuna kukhala naye pachibwenzi, pomwe m’baleyo alibe maganizo amenewo.
Akulu ayenera kuchita zinthu mokoma mtima ndi alongo omwe afunsa funso kuti adziwe zinazake kapena omwe atchula nkhani inayake yomwe akuluwo angafunike kuisamalira. Akulu ayenera kuchita zinthu moganizira alongo omwe alibe amuna owasamalira.—Ru 2:8, 9.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZISONYEZA CHIKONDI CHOSATHA MUMPINGO WACHIKHRISTU—MUZIKONDA AKAZI AMASIYE NDI ANA AMASIYE, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi abale ndi alongo anasonyeza bwanji chikondi chachikulu kwa Mlongo Myint?
Kodi chikondi chimene abale ndi alongo anasonyeza kwa Mlongo Myint chinathandiza bwanji kuti dzina la Yehova lilemekezedwe?
Kodi chikondi chimene abale ndi alongo anasonyeza kwa Mlongo Myint chinathandiza bwanji ana ake?
Kodi ndi njira zina ziti zimene mungasonyezere kuti mumaganizira alongo mumpingo wanu?