Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 September tsamba 5
  • Pitirizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikira
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • N’chiyani Chingatithandize Kuti Tizisankha Zinthu Mwanzeru?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Mawu Oyamba
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2024
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 September tsamba 5

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Pitirizani Kuphunzitsa Mphamvu Zanu za Kuzindikira

Munthu amene amachita masewera othamanga amafunika kumadziphunzitsa kuti akhalebe ndi luso. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kumachita khama kuti tipitirize kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikira. (Ahe 5:14) Ngakhale kuti nthawi zina tikhoza kukhala ndi maganizo ofuna kutengera zimene ena asankha, tiyenera kumadziphunzitsa kuti tiziganiza komanso kusankha zochita patokha. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.​—Aro 14:12.

Sitikuyenera kuganiza kuti tikhoza kupanga zosankha zabwino chabe chifukwa chakuti tinabatizidwa kalekale. Kuti tizisankha zinthu mwanzeru, tiyenera kumadalira Yehova, Mawu ake, komanso gulu lake.​—Yos 1:7, 8; Miy 3:5, 6; Mt 24:45.

ONERANI VIDIYO YAKUTI “KHALANI NDI CHIKUMBUMTIMA CHABWINO,” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino.” Emma ndi mwamuna wake akuona khadi lowaitanira ku ukwati.

    Kodi Emma ankafunika kusankha chiyani?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino.” Amy akufotokoza maganizo ake mwamphamvu.

    N’chifukwa chiyani sitiyenera kusankhira ena zochita pazinthu zomwe aliyense akufunika kusankha yekha potengera chikumbumtima chake?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino.” Emma akupempha malangizo kwa Mlongo Charlotte ndi M’bale Allan.

    Kodi ndi malangizo anzeru ati amene banja lina linapereka kwa Emma?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Khalani ndi Chikumbumtima Chabwino.” Emma akufufuza pogwiritsa ntchito “LAIBULALE YA PA INTANETI” pa kompyuta yake.

    Kodi Emma anapeza kuti malangizo othandiza okhudza vuto lomwe anakumana nalo?

Kodi ndiyenera kudalira chiyani ndikamasankha zochita?

  • Maganizo anga

  • Maganizo a anthu ena

  • Mfundo za m’Baibulo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena