Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb21 November tsamba 9
  • Kodi Alongo Angatani Kuti Azichita Zambiri Potumikira Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Alongo Angatani Kuti Azichita Zambiri Potumikira Yehova?
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Muzilimbikitsa Alongo Mumpingo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Kodi Mumaona Akazi Ngati Mmene Yehova Amawaonera?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • ‘Akazi Amene Agwiritsa Ntchito mwa Ambuye’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21 November tsamba 9
Zithunzi zosonyeza alongo akusangalala kuchita mautumiki osiyanasiyana: 1. Mlongo ali mu utumiki. 2. Mlongo akugwira ntchito ya zomangamanga. 3. Mlongo akuyeretsa m’Nyumba ya Ufumu. 4. Mlongo akusonyeza mlongo wina wachikulire mmene angagwiritsire ntchito tabuleti. 5. Mlongo akuthandiza mwana wake kuyankha pamisonkhano. 6. Alongo awiri akulalikira kunja kukuzizira.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Alongo Angatani Kuti Azichita Zambiri Potumikira Yehova?

Alongo amathandiza kwambiri pa ntchito za Ufumu. (Sl 68:11) Amachititsa maphunziro a Baibulo ambiri ndiponso apainiya okhazikika ambiri ndi alongo. Alongo akhama masauzande ambiri akutumikira pa Beteli, akuchita umishonale, akuchita utumiki wa zomangamanga wongodzipereka kapena wanthawi zonse komanso akugwira ntchito yomasulira. Alongo olimba mwauzimu amalimbitsa mabanja awo komanso mipingo yawo. (Miy 14:1) Ngakhale kuti alongo sangatumikire monga akulu kapena atumiki othandiza, komabe akhoza kukhala ndi zolinga mumpingo. Ngati ndinu mlongo, kodi mungatani kuti muzichita zambiri potumikira Yehova?

  • Muzikhala ndi makhalidwe abwino.—1Ti 3:11; 1Pe 3:3-6

  • Muzithandiza alongo amumpingo mwanu omwe sadziwa zambiri.​—Tit 2:3-5

  • Muziyesetsa kuchita zambiri komanso kuthera nthawi yambiri mu utumiki

  • Mungaphunzire chinenero china

  • Mungasamukire kumene kukufunika olalikira ufumu ambiri

  • Mungafunsire utumiki wa pa Beteli kapena utumiki wa zomangamanga

  • Mungafunsire Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu

ONERANI VIDIYO YAKUTI “AKAZI OGWIRA NTCHITO MWAKHAMA POTUMIKIRA AMBUYE,” NDIPO KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • Kodi zomwe mlongo aliyense wafotokoza zakulimbikitsani bwanji?

Alongo atatu omwe anaoneka mu vidiyo yakuti “Akazi Ogwira Ntchito Mwakhama Potumikira Ambuye.”
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena