Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 July tsamba 13
  • Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo mu September

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo mu September
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yapadera Yogawira Bulosha Latsopano
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Thandizani Osoŵa Chidziŵitso Kuti Azindikire
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 July tsamba 13
Zithunzi zosonyeza banja lomwe linali munkhani yakuti “Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi​—Upainiya,” likulalikira: 1. Mlongo ndi mwana wake akugwiritsa ntchito kabuku kakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” pokambirana ndi mayi wina amene amupeza pakhomo pake. 2. Agogo akugwiritsa ntchito kabuku kakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” pochititsa phunziro pafoni. 3. M’bale ndi mlongo akulalikira pogwiritsa ntchito kashelefu ndipo aikapo timabuku takuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale” komanso chikwangwani chodziwitsa anthu za phunziro la Baibulo laulere.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo mu September

M’mwezi wa September, tidzagwira mwakhama ntchito yapadera yoyambitsa maphunziro a Baibulo ku nyumba ndi nyumba pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Ofalitsa angasankhe kudzachita upainiya wothandiza wa maola 30. Kodi tidzagwira bwanji ntchito yapaderayi?

  • Pa Ulendo Woyamba: Gwiritsani ntchito tsamba lomaliza la kabukuka kuti mukope chidwi cha munthuyo, komanso mumusonyeze mmene phunziro la Baibulo limachitikira. Anthu enanso osafunika kuwaiwala ndi amene anasonyezapo chidwi m’mbuyomu komanso maulendo obwereza. Ngakhale kuti panthawiyo anakana kuphunzira, panopa akhoza kuchita chidwi ndi kabukuka komanso njira yatsopano imene tikugwiritsa ntchito pophunzira. Musasiye kabukuka pakhomo pamene palibe anthu, kapena kutumiza limodzi ndi makalata kwa anthu amene sanasonyeze chidwi m’mbuyomu. Komiti ya Utumiki ya Mpingo ingakonze misonkhano yowonjezera yokonzekera utumiki m’mwezi umenewu.

  • Njira Zina: Ngati mpingo wanu umagwiritsa ntchito timashelefu, muikepo timabuku takuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Afotokozereni anthu amene asonyeza chidwi kuti tikhozanso kumaphunzira nawo Baibulo pogwiritsa ntchito kabukuka. Tingawasonyeze mwachidule mmene phunziro la Baibulo limachitikira, kapena tingapangane nawo kuti tidzawasonyeze nthawi ina. Woyang’anira utumiki angakonze zoti ofalitsa oyenerera akalalikire ku dera la malonda limene lili m’gawo lawo. Mungayambitsenso maphunziro a Baibulo kwa anthu amene mumagwira nawo ntchito kapena amene mumakumana nawo mukamalalikira mwamwayi.

Yesu anatilamula kuti ‘tiphunzitse anthu.’ (Mt 28:19, 20) Tikukhulupirira kuti ntchito yapaderayi itithandiza kukwaniritsa cholinga chathuchi pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena