Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb22 September tsamba 5
  • Banja Ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Banja Ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Pabanja Ndi Kusakhala Pabanja?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kukonzekera Ukwati Wachipambano
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
mwb22 September tsamba 5
Banja likulalikira limodzi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Banja Ndi Mgwirizano wa Moyo Wonse

Mabanja a Chikhristu amene amayenda bwino amalemekeza Mulungu, ndiponso onse mwamuna ndi mkazi, amakhala osangalala. (Mko 10:9) Kuti Mkhristu adzakhale ndi banja lolimba komanso losangalala, ayenera kutsatira mfundo za m’Baibulo akamasankha munthu wokwatirana naye.

Musakhale pachibwenzi ndi wina aliyense mpaka ‘mutapitirira pachimake pa unyamata,’ yomwe ndi nthawi imene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu kwambiri ndipo chingakupangitseni kuti musamaganize bwino. (1Ak 7:36) Muzigwiritsa ntchito mwanzeru nthawi imene simunalowe m’banja polimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso kukulitsa makhalidwe amene Akhristu ayenera kukhala nawo. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mudzakhale ndi banja losangalala.

Musanatsimikize zokwatirana ndi winawake, muzikhala ndi nthawi yokwanira kuti mudziwe bwino “munthu wobisika wamumtima.” (1Pe 3:4) Ngati mwayamba kukayikira kwambiri kuti munthu amene mukufuna kukwatirana naye alidi woyenerera, kambiranani naye. Mofanana ndi mmene zimakhalira ndi mabwenzi apamtima, anthu okwatirana ayenera kumaganizira kwambiri zimene iwowo angachitire mnzawoyo, osati zimene angawachitire. (Afi 2:3, 4) Ngati mutamatsatira mfundo za m’Baibulo musanalowe m’banja, zidzakhala zosavuta kuti mukadzakwatira mudzapitirize, ndipo zimenezi zidzakuthandizani kuti mudzakhale ndi banja losangalala.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KUKONZEKERA KULOWA M’BANJA​—GAWO 3: “KUWERENGERA NDALAMA ZIMENE MUDZAWONONGE,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi chibwenzi cha mlongoyu ndi Shane chinkayenda bwanji?

  • Kodi mlongoyu anazindikira chiyani pamene ankayamba kumudziwa bwino?

  • Kodi makolo ake anamuthandiza bwanji, nanga anasankha bwanji zinthu mwanzeru?

M’bale amene ali pachibwenzi ndi mlongo angaganizire mafunso awa:

Kodi ali ndi makhalidwe ati a Chikhristu? Kodi amasonyeza bwanji kuti amaika zinthu zokhudza Ufumu pa malo oyamba? Kodi amasonyeza kuti amagonjera malangizo a gulu? Kodi amasonyeza kuti amaganizira anthu ena?

Mlongo amene ali pachibwenzi ndi m’bale angaganizire mafunso awa:

Kodi ali ndi makhalidwe ati a Chikhristu? Kodi amaona kuti zinthu zokhudza kulambira komanso udindo wake mumpingo ndi zofunika kwambiri kuposa ntchito, ndalama, masewera ndiponso zosangalatsa? Kodi amachita bwanji zinthu ndi anthu a m’banja lake? Kodi amasonyeza kuti amaganizira anthu ena?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena