MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzigwiritsa Ntchito Mfundo za M’Baibulo Pothandiza Ana Anu Kuti Zinthu Ziwayendere Bwino
Makolo a Chikhristu amafuna kuti ana awo azisangalala potumikira Yehova. Iwo angathandize ana awo kuti zinthu ziwayendere bwino pogwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.—Miy 22:6.
Muzikhala omasuka kuti ana anu azilankhula nanu mosavuta.—Yak 1:19
Muzikhala chitsanzo chabwino.—De 6:6
Muzichita zinthu zokhudza kulambira nthawi zonse.—Aef 6:4
ONERANI VIDIYO YAKUTI MANGANI NYUMBA YOLIMBA—MUZIPHUNZITSA ANA ANU ‘M’NJIRA YOWAYENERERA’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi makolo angasonyeze bwanji kuti amaganizira ana awo?
Kodi makolo angagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Yakobo 1:19?
Kodi makolo angatani ngati pali mavuto?