Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp21 No. 2 tsamba 10-12
  • Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale M’dziko Latsopano?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale M’dziko Latsopano?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “KUDZIWA MULUNGU” KUNGATITHANDIZE KUTI TIDZAPULUMUKE
  • MUZIWERENGA MAWU A MULUNGU TSIKU LILILONSE
  • MUZIPEMPHERA KWA MULUNGU KUTI AZIKUTHANDIZANI
  • Kodi Mulungu Wachita Zinthu Ziti?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Mudzakhale ndi Moyo Wosatha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Njira ya Kukhalira ndi Moyo Kosatha
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Ungathe Kukhala M’dziko Latsopano la Mulungu Lamtendere
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
wp21 No. 2 tsamba 10-12

Kodi Mungatani Kuti Mudzakhale M’dziko Latsopano?

Nkhani zapitazi zafotokoza kuti posachedwapa Mulungu awononga maboma a anthu ndi kuthetsa mavuto onse padzikoli. N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti zimenezi zidzachitikadi? N’chifukwa chakuti Mawu a Mulungu omwe ndi Baibulo analonjeza kuti:

“Dziko likupita.”​—1 YOHANE 2:17.

Sitikukayikiranso kuti padzakhala opulumuka chifukwa vesi lili pamtundali limanenanso kuti:

“Wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”

Choncho, tiyenera kuchita zimene Mulungu amafuna ngati tikufuna kudzapulumuka. Kuti tidziwe zimene Mulungu amafuna, choyamba tiyenera kumudziwa bwino.

“KUDZIWA MULUNGU” KUNGATITHANDIZE KUTI TIDZAPULUMUKE

Zithunzi: 1. Nesi yemwe wakhumudwa komanso kutopa wakhala pansi. 2. Wapita kukapuma m’chipinda chodyera ndipo akuona nesi wina yemwe akuwerenga magazini mosangalala. 3. Nesi mnzake akumuwerenga lemba la m’Baibulo komanso akumupatsa kadi lofotokoza za webusaiti ya jw.org.

Yesu ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona.” (Yohane 17:3) Tifunika “kudziwa” Mulungu kuti tidzapulumuke mapeto a dzikoli n’kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Zimenezi zimaphatikizapo zambiri kuposa kungodziwa kuti Mulungu aliko komanso kudziwa zinthu zochepa zokhudza iyeyo. Timafunika kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Ngati tikufuna kuti munthu winawake akhale mnzathu wapamtima tifunika kupeza nthawi yocheza naye. N’zimenenso tiyenera kuchita kuti Mulungu akhale mnzathu wapamtima. Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

Mfundo Zimene Baibulo Limatiphunzitsa

Nesi uja ali kunyumba kwake ndipo watsegula webusaiti ya jw.org.

Limatiphunzitsa kuti Mulungu ankafuna kuti tizikhala m’Paradaiso.

Mulungu atalenga Adamu ndi Hava anawaika m’malo okongola kwambiri otchedwa munda wa Edeni. Iwo anali angwiro ndipo Mulungu anawapatsa chilichonse chimene ankafunikira kuti azikhala mosangalala. Akanatha kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Ndipotu Adamu ndi Hava akanapitirizabe kumvera Mulungu sakanafa. Koma iwo anasankha kusamvera lamulo limene Mulungu anawapatsa ngakhale kuti linali losavuta kulitsatira.

Limatiphunzitsa chifukwa chake timakumana ndi mavuto.

Chifukwa chakuti Adamu sanamvere Mulungu anataya mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale ndipo zimenezi zinakhudza anthu onse. Baibulo limafotokoza kuti: “Monga mmene uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Makolo akakhala ndi chilema chinachake mwana amatha kutengera chilemacho. Ndi mmenenso zinakhalira kuti Adamu apatsire uchimo ana ake onse. Choncho, timakalamba ndi kufa chifukwa chakuti tinatengera uchimo kwa Adamu ndi Hava.

Limatiphunzitsa zimene Mulungu watichitira kuti tidzapeze moyo wosatha.

Baibulo limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Mulungu anatumiza Yesu padzikoli kuti adzatifere. Poganizira zimene Mulungu anachitazi munthu wina wazaka 86, wa ku India dzina lake Prabhakar, ananena kuti: “Zimene Yehovaa anachitazi zimasonyeza kuti amandikonda kwambiri. Ndikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha chifukwa cha chikondi chake.”

Limatiphunzitsa zimene tingachite posonyeza kuyamikira zomwe Mulungu watichitira.

Baibulo limanena kuti tingasonyeze kuyamikira zimene Mulungu watichitira tikamapitiriza “kusunga malamulo ake.” (1 Yohane 2:3) Yehova Mulungu wathu wachikondi amatiuza zimene tiyenera kuchita kuti tizisangalala ndi moyo panopa. (Yesaya 48:17, 18) Mulungu safuna kuti tizivutika. Iye amatilonjeza kuti tikamatsatira malangizo ake, tizikhala mosangalala panopa komanso tidzakhala ndi moyo mpaka kalekale.

MUZIWERENGA MAWU A MULUNGU TSIKU LILILONSE

Nesi akuyang’ana kumwamba pambuyo powerenga Baibulo pa nthawi yopuma.

Mukhoza kudzapulumuka mapeto a dzikoli mukamapemphera kwa Mulungu kuti akuthandizeni komanso mukamachita zimene iye amafuna

Kuti tikhale ndi moyo timafunikira kudya tsiku lililonse. Koma Yesu anati: “Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”​—Mateyu 4:4.

Masiku ano mawu amene Yehova ananena timawapeza m’Baibulo. Mukamawerenga buku lopatulikali mudziwa zimene Mulungu anachita kale, zimene akuchita panopa ndiponso zimene adzachite m’tsogolo.

MUZIPEMPHERA KWA MULUNGU KUTI AZIKUTHANDIZANI

Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kumvera Mulungu koma zikukuvutani kusiya makhalidwe amene iye amadana nawo? Ngati ndi choncho, mungachite bwino kuyesetsa kumudziwa bwino Mulungu.

Taganizirani za mayi wina yemwe tangomutchula kuti Sakura, amene poyamba ankakonda kuchita zachiwerewere. Atayamba kuphunzira Baibulo anaphunzira lamulo la Mulungu lakuti “thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Sakura anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize ndipo anakwanitsa kusiya khalidwe loipali. Komabe panopa akuyesetsa kuti asayambirenso khalidwe loipali. Iye akuti: “Ndikayamba kuganizira zinthu zachiwerewere ndimapemphera kwa Yehova moona mtima chifukwa ndimadziwa kuti pandekha sindingakwanitse kulimbana ndi vutoli. Pemphero landithandiza kwambiri kuti ndiyandikire Yehova.” Mofanana ndi Sakura, anthu mamiliyoni ambiri akuphunzira Baibulo n’cholinga choti amudziwe bwino Mulungu. Mulungu amawapatsa mphamvu zowathandiza kusintha n’kumachita zimene iye amafuna.​—Afilipi 4:13.

Mukamudziwa bwino Mulungu m’pamene amayamba kukukondani ndipo mumakhala mnzake wapamtima. (Agalatiya 4:9; Salimo 25:14) Mukatero mudzapulumuka n’kukhala m’dziko latsopano la Mulungu. Koma kodi moyo udzakhala wotani m’dziko latsopano? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

a Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena