Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w23 July tsamba 32
  • Mfundo Zothandiza Pophunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfundo Zothandiza Pophunzira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Muziyamba ndi Zinthu Zofunika
  • Muziyesetsa Kuti Kuphunzira Kuzikuthandizani!
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mungaphunzirenso Izi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Muzigwiritsa Ntchito Webusaiti Yathu mu Utumiki—“Khalani Bwenzi la Yehova”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Mfundo Zothandiza Pofufuza
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
w23 July tsamba 32

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Muziyamba ndi Zinthu Zofunika

Tonsefe timakhala ndi nthawi yochepa yoti tiziphunzira patokha. Ndiye kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu? Choyamba, muzikhala ndi nthawi yokwanira yoti muwerenge. Mukhoza kupindula kwambiri ngati mutamaphunzira mosamala zinthu zochepa kusiyana ndi kuphunzira zinthu zambiri mothamanga.

Choncho muziona kuti zofunika kwambiri ndi ziti. (Aef. 5:15, 16) Taganizirani mfundo izi:

  • Muziwerenga Baibulo tsiku lililonse. (Sal. 1:2) Ndandanda yowerengera Baibulo ya misonkhano ya mkati mwa mlungu ingakhale poyambira pabwino.

  • Muzikonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda komanso misonkhano ya mkati mwa mlungu. Muzikhala okonzeka kukayankha.​—Sal. 22:22.

  • Ngati n’zotheka, muziyesetsa kupeza nthawi yowerenga zinthu zina zatsopano monga magazini yogawira komanso zinthu zomwe zaikidwa pa jw.org.

  • Muzikonza zoti muphunzire nkhani inayake. Mukhoza kufufuza zokhudza vuto linalake lomwe mukukumana nalo, funso lomwe muli nalo kapena nkhani inayake ya m’Baibulo imene mumafuna mutaimvetsa. Kuti mupeze mfundo zina zoti muphunzire, pitani pa jw.org pa gawo lakuti “Zoti Muchite Pophunzira Baibulo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena