Kodi Nkhondo Komanso Zachiwawa Zimatikhudza Bwanji Tonsefe?
“Kungoyambira pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, zachiwawa zakhala zikungowonjezereka ndipo anthu 2 biliyoni, omwe ndi munthu mmodzi pa anthu 4 alionse padzikoli, akukhala m’malo amene kukuchitika zachiwawa.”
Wachiwiri kwa Mlembi Wamkulu Bungwe la United Nations, Amina J. Mohammed, 26 January 2023.
Nkhondo komanso zachiwawa zingayambike mwadzidzidzi m’malo amene panopa muli mtendere. Ngakhale anthu amene ali m’mayiko akutali ndi kumene zimenezi zikuchitika amakhudzidwanso. Ndipo mavuto amene amayambika chifukwa cha nkhondoyo amakhalapo kwa nthawi yaitali ngakhale itatha. Taonani zitsanzo zotsatirazi:
Kusowa kwa chakudya. Nthambi ya Bungwe la UN yoona za chakudya padziko lonse inanena kuti, “nkhondo ndi zimene zikuchititsa kuti padzikoli anthu ambiri azivutika ndi njala, moti 70 peresenti ya anthu amene akuvutika ndi njala amakhala m’madera amene muli nkhondo komanso zachiwawa.”—World Food Programme.
Mavuto okhudza maganizo komanso thanzi. Anthu akadziwa kuti m’dera lawo mukhoza kuchitika nkhondo amayamba kuda nkhawa komanso kuvutika kwambiri maganizo. Kuwonjezera pa kuvulala, nthawi zambiri anthu a m’madera amene kukuchitika nkhondo amakhalanso ndi mavuto a maganizo. Koma zimakhalanso zovuta kuti alandire thandizo lachipatala.
Kuthawa nkhondo. Malinga ndi zimene inanena nthambi ya bungwe la United Nations yoona za anthu othawa kwawo (United Nations High Commissioner for Refugees), pofika mu September 2023, anthu oposa 114 miliyoni padziko lonse anakakamizika kuthawa kwawo. Nkhondo komanso zachiwawa ndi zimene zikuchititsa kwambiri vutoli.
Mavuto azachuma. Nthawi zambiri anthu amakumana ndi mavuto azachuma oyambitsidwa ndi nkhondo monga kutsika mphamvu kwa ndalama. Anthu akhoza kuvutika ngati boma likugwiritsa ntchito ndalama zambiri pa nkhondo m’malo mozigwiritsa ntchito pa zaumoyo komanso maphunziro. Ndipo pamafunika ndalama zambiri zomangiranso zinthu zimene zinawonongedwa pankhondo.
Kuwonongedwa kwa chilengedwe. Anthu amavutika kwambiri dera lawo likawonongedwa pankhondo. Kuwonongeka kwa madzi, mpweya ndiponso nthaka kumayambitsa matenda osiyanasiyana amene anthu angavutike nawo kwa nthawi yaitali, komanso anthu akhoza kuvulala kapenanso kuphedwa ndi zida zankhondo zimene zinasiyidwa munthaka ngakhale patapita nthawi yaitali kuchokera pamene nkhondo inatha.
N’zosachita kufunsa kuti nkhondo imawonongetsa zinthu zambiri.