NKHANI YOPHUNZIRA 25
NYIMBO NA. 96 Baibulo Ndi Chuma
Zimene Tikuphunzira pa Ulosi wa Yakobo Atatsala Pang’ono Kumwalira—Gawo 2
“Aliyense anamupatsa madalitso omuyenerera.”—GEN. 49:28.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tiona zimene tikuphunzira pa ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira wokhudza ana ake 8.
1. Kodi munkhaniyi tikambirana zinthu ziti zimene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira?
ANA a Yakobo anali atakhala momuzungulira pomwe amamvetsera mwatcheru bambo awo akuwadalitsa. Monga tinaonera munkhani yapita ija, zimene Yakobo anauza Rubeni, Simiyoni, Levi ndi Yuda ziyenera kuti zinawadabwitsa kwambiri. Choncho iwo ayenera kuti anali ndi chidwi kuti amve zimene Yakobo anganene kwa ana 8 otsalawo. Tiyeni tione zimene tikuphunzira pa zimene Yakobo anauza Zebuloni, Isakara, Dani, Gadi, Aseri, Nafitali, Yosefe ndi Benjamini.a
ZEBULONI
2. Fotokozani madalitso amene Zebuloni analonjezedwa, komanso mmene anakwaniritsidwira. (Genesis 49:13) (Onaninso bokosi.)
2 Werengani Genesis 49:13. Yakobo ananena kuti ana a Zebuloni azidzakhala m’mbali mwa nyanja chakumadzulo kwa Dziko Lolonjezedwa. Patapita zaka zoposa 200, ana a Zebuloni analandira cholowa chomwe chinali dera limene linali pakati pa nyanja ya Galileya ndi ya Mediterranean. Nayenso Mose analosera kuti: “Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako.” (Deut. 33:18) Mwina zimenezi zikanatanthauza kuti iwo akanatha kumachita malonda mosavuta chifukwa anali pakati pa nyanja ziwiri. Mulimonse mmene zinalili, ana a Zebuloni anali ndi chifukwa chokhalira osangalala.
3. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala ndi zimene tili nazo?
3 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Nthawi zonse timakhala ndi zifukwa zokhalira osangalala posatengera kumene tikukhala kapena mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Tingapitirize kukhala osangalala tikamakhutira ndi zimene tili nazo. (Sal. 16:6; 24:5) Nthawi zina zimakhala zovuta kuti tizisangalala ndi zimene tili nazo chifukwa chongoganizira zinthu zimene tilibe. Choncho tiyeni tiziyesetsa kuona zabwino zimene zikutichitikira.—Agal. 6:4.
ISAKARA
4. Kodi Isakara analonjezedwa chiyani, nanga zinakwaniritsidwa bwanji? (Genesis 49:14, 15) (Onaninso bokosi.)
4 Werengani Genesis 49:14, 15. Yakobo anayamikira Isakara chifukwa chogwira ntchito mwakhama ndipo anamuyerekezera ndi bulu yemwe amakhala ndi mafupa olimba komanso amanyamula katundu wolemera. Yakobo ananenanso kuti Isakara adzapatsidwa dziko labwino. Mogwirizana ndi zimene Yakobo ananena, mbadwa za Isakara zinalandira dziko lomwe linali ndi nthaka yachonde, m’mbali mwa mtsinje wa Yorodano. (Yos. 19:22) Mosakayikira, iwo ankagwira ntchito mwakhama polima minda yawo koma ankagwiranso ntchito mwakhama pothandiza ena. (1 Maf. 4:7, 17) Mwachitsanzo, pamene Woweruza Baraki ndi mneneri Debora anapempha Aisiraeli kuti akamenye nawo nkhondo yolimbana ndi adani awo, fuko la Isakara linadzipereka kukathandiza ndipo ankadziperekanso kukamenya nkhondo pa nthawi zina.—Ower. 5:15.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala akhama pogwira ntchito?
5 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova amayamikira khama limene timachita pomutumikira ngati mmene anayamikirira fuko la Isakara. (Mlal. 2:24) Mwachitsanzo, taganizirani khama limene abale amasonyeza posamalira mpingo. (1 Tim. 3:1) Sikuti abalewa amamenya nkhondo zenizeni, koma amadzipereka poteteza anthu a Mulungu ku zinthu zomwe zingawononge ubwenzi wawo ndi Yehova. (1 Akor. 5:1, 5; Yuda 17-23) Amagwiranso ntchito mwakhama pokonzekera komanso kukamba nkhani zimene zimalimbikitsa mpingo.—1 Tim. 5:17.
DANI
6. Kodi fuko la Dani linapatsidwa utumiki wotani? (Genesis 49:17, 18) (Onaninso bokosi.)
6 Werengani Genesis 49:17, 18. Yakobo anayerekezera Dani ndi njoka imene imatha kulimbana ndi zinthu zazikulu kuposa iyoyo, monga hatchi yankhondo ndi wokwerapo wake. Zimenezi zinkatanthauza kuti Dani adzakhala woopsa ndipo azidzagonjetsa adani a Isiraeli. Pamene ankapita ku Dziko Lolonjezedwa, a fuko la Dani ankateteza mtundu wonsewo ‘polondera kumbuyo’ kwake. (Num. 10:25) Utumikiwu unali wofunika kwambiri ngakhale kuti sunali woonekera kwa Aisiraeli onse.
7. Kodi tiziona bwanji utumiki uliwonse umene tapatsidwa?
7 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kodi munapatsidwapo utumiki umene sunali woonekera kwa anthu ena? Mwina munathandiza nawo pokonza ndi kuyeretsa Nyumba ya Ufumu, kudzipereka kugwira ntchito pamsonkhano wadera kapena wachigawo kapenanso kugwira ntchito zina. Ngati ndi choncho, tikukuyamikirani kwambiri. Nthawi zonse muzikumbukira kuti Yehova amaona komanso amayamikira zonse zimene mumachita pomutumikira. Iye amayamikira kwambiri mukamamutumikira osati chifukwa chofuna kutamandidwa koma chifukwa choti mumamukonda.—Mat. 6:1-4.
GADI
8. Kodi n’chiyani chikanachititsa kuti adani aziukira mosavuta a fuko la Gadi m’Dziko Lolonjezedwa? (Genesis 49:19) (Onaninso bokosi.)
8 Werengani Genesis 49:19. Yakobo analosera kuti fuko la Gadi lizidzaukiridwa ndi achifwamba. Fuko la Gadi linakakhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano ndipo anachita malire ndi mitundu ya adani awo. Malowa ankachititsa kuti adaniwa aziwaukira mosavuta. Komabe a fuko la Gadi ankafuna kukhala komweko chifukwa kunali malo abwino odyetserako ziweto zawo. (Num. 32:1, 5) Anthu a fuko la Gadi anali olimba mtima. Kuwonjezera pamenepo, iwo ankakhulupirira kuti Yehova aziwathandiza kuteteza dziko lawo ku magulu alionse achifwamba. Kwa zaka zingapo, iwo anatumiza asilikali awo kukathandiza mafuko ena kugonjetsa mbali yotsala ya Dziko Lolonjezedwa kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano. (Num. 32:16-19) Iwo sankakayikira kuti Yehova ateteza akazi ndi ana awo pomwe amuna apita kunkhondo. Yehova anawadalitsa chifukwa cha kulimba mtima komanso kudzipereka kwawo.—Yos. 22:1-4.
9. Kodi kukhulupirira Yehova kungakhudze bwanji zimene timasankha kuchita pa moyo wathu?
9 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kuti tipitirize kutumikira Yehova pa nthawi yovuta, tiyenera kumudalira. (Sal. 37:3) Abale ndi alongo ambiri masiku ano amasonyeza kuti amakhulupirira Yehova podzipereka kuti akathandize pa ntchito zomangamanga, kukatumikira komwe kukufunika olalikira ambiri kapenanso kuchita mautumiki ena. Iwo amachita zimenezi chifukwa amakhulupirira ndi mtima wonse kuti nthawi zonse Yehova aziwasamalira.—Sal. 23:1.
ASERI
10. Kodi fuko la Aseri linalephera kuchita chiyani? (Genesis 49:20) (Onaninso bokosi.)
10 Werengani Genesis 49:20. Yakobo analosera kuti fuko la Aseri lidzakhala lolemera kwambiri ndipo ndi zimene zinachitikadi. Dziko limene a fuko la Aseri analandira linali lachonde mu Isiraeli monse. (Deut. 33:24) Dzikolo linalinso kufupi ndi nyanja ya Mediterranean komwe kunali doko la Foinike lomwe linali lolemera kwambiri chifukwa cha nkhani zamalonda. Koma a fuko la Aseri analephera kuchotsa a Akanani m’dzikolo. (Ower. 1:31, 32) Choncho makhalidwe oipa a Akanani komanso chuma zinachititsa kuti a fuko la Aseri ayambe kunyalanyaza kulambira koyera. Mwachitsanzo, Woweruza Baraki atapempha amuna kuti akathandize pa nkhondo yolimbana ndi Akanani, a fuko la Aseri sanapite nawo. Izi zinachititsa kuti fukoli lisaone nawo zodabwitsa zimene Yehova anachita pothandiza Aisiraeli ‘kumadzi a ku Megido.’ (Ower. 5:19-21) A fuko la Aseri ayenera kuti anachita manyazi kumva Baraki ndi Debora akuimba nyimbo yosonyeza kupambana yomwe inali ndi mawu akuti: “Aseri anangokhala phee mʼmbali mwa nyanja.”—Ower. 5:17.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chuma?
11 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Timafunitsitsa kumupatsa Yehova zinthu zabwino kwambiri. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kupewa maganizo amene anthu m’dzikoli amakhala nawo pa nkhani ya ndalama komanso chuma. (Miy. 18:11) Ngakhale kuti ndalama ndi zofunika, sitiyenera kuziona kuti ndi zofunika kwambiri kuposa kutumikira Yehova. (Mlal. 7:12; Aheb. 13:5) Tisamawononge nthawi yathu pofunafuna zinthu zimene ndi zosafunika kwenikweni. M’malomwake timafuna kuchita zonse zomwe tingathe potumikira Yehova podziwa kuti moyo wabwino komanso chitetezo tidzazipeza m’dziko latsopano.—Sal. 4:8.
NAFITALI
12. Kodi zimene Nafitali analonjezedwa zinakwaniritsidwa bwanji? (Genesis 49:21) (Onaninso bokosi.)
12 Werengani Genesis 49:21. Yakobo ananena kuti Nafitali adzalankhula “mawu osangalatsa.” Zimenezi zingaimire mawu amene Yesu analankhula pa utumiki wake. Yesu, yemwe ankadziwika kuti anali Mphunzitsi waluso, ankakonda kupezeka ku Kaperenao, dera limene linali m’gawo la Nafitali. N’chifukwa chake mzindawu unkatchedwa ‘mzinda umene ankakhala.’ (Mat. 4:13; 9:1; Yoh. 7:46) Ponena za Yesu, mneneri Yesaya analosera kuti anthu a ku Zebuloni ndi ku Nafitali adzaona “kuwala kwakukulu.” (Yes. 9:1, 2) Zimene Yesu ankaphunzitsa, zinasonyeza kuti iye anali “kuwala kwenikweni kumene kumaunikira anthu osiyanasiyana.”—Yoh. 1:9.
13. Kodi tingatani kuti zimene timalankhula zizisangalatsa Yehova?
13 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Zolankhula zathu komanso mmene timalankhulira zimakhudza Yehova. Ndiye kodi tingatani kuti tizilankhula “mawu osangalatsa” omwe sangakhumudwitse Yehova? Nthawi zonse tizilankhula zoona. (Sal. 15:1, 2) Tingalimbikitse ena ndi zolankhula zathu tikamafulumira kuwayamikira n’kumapewa kudandaula kapena kuwapezera zifukwa. (Aef. 4:29) Tingakhalenso ndi cholinga choti tiziyamba kukambirana ndi anthu mwaluso kuti tiwalalikire.
YOSEFE
14. Kodi madalitso amene Yosefe analonjezedwa anakwaniritsidwa bwanji? (Genesis 49:22, 26) (Onaninso bokosi.)
14 Werengani Genesis 49:22, 26. Yakobo ayenera kuti ankasangalala kwambiri ndi Yosefe, yemwe Yehova ‘anamusankha pakati pa abale ake.’ Yakobo anamutchula kuti iye anali “mphukira yamtengo wobala zipatso.” Yakobo ndi amene anali mtengowo, ndipo Yosefe anali mphukira yake. Yosefe anali mwana woyamba wa mkazi wake wokondedwa, Rakele. Yakobo anasonyeza kuti Yosefe ndi amene akanalandira cholowa cha Rubeni yemwe anali mwana woyamba wa mkazi wake Leya. (Gen. 48:5, 6; 1 Mbiri 5:1, 2) Pokwaniritsa ulosiwu, Efuraimu ndi Manase omwe anali ana a Yosefe, aliyense analandira cholowa chakechake.—Gen. 49:25; Yos. 14:4.
15. Kodi Yosefe anatani atachitiridwa zinthu zopanda chilungamo?
15 Yakobo ananenanso za ‘oponya mivi ndi uta omwe sanaleke kumuzunza [Yosefe], kumulasa ndi kumusungira chidani.’ (Gen. 49:23) Oponya miviwa anali azichimwene ake omwe anachititsa kuti iye akumane ndi zopanda chilungamo zambirimbiri chifukwa chakuti ankamuchitira nsanje. Koma Yosefe sanakwiyire abale akewo kapena Yehova. Monga mmene Yakobo ananenera, “uta [wa Yosefe] unakhalabe pamalo ake, ndipo manja ake anakhalabe amphamvu ndi ochenjera.” (Gen. 49:24) Yosefe ankadalira Yehova pa mayesero onse omwe anakumana nawo ndipo anakhululukira abale akewo komanso kuwachitira zinthu mokoma mtima. (Gen. 47:11, 12) Yosefe analola kuti mayeserowo amuthandize kukhala munthu wabwino. (Sal. 105:17-19) Zotsatira zake n’zakuti Yehova anamugwiritsa ntchito m’njira yapadera kwambiri.
16. Kodi tingatsanzire bwanji Yosefe tikakumana ndi mayesero?
16 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tisamalole kuti mayesero atisiyitse kukonda Yehova kapenanso Akhristu anzathu. Tizikumbukira kuti Yehova angalole kuti tikumane ndi mayesero enaake n’cholinga choti atiphunzitse. (Aheb. 12:7) Maphunziro amenewo angatithandize kuti tikhale ndi makhalidwe abwino monga chifundo komanso kukhululuka. (Aheb. 12:11) Zikatero tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa tikakhala opirira ngati Yosefe.
BENJAMINI
17. Kodi zimene Benjamini analonjezedwa zinakwaniritsidwa bwanji? (Genesis 49:27) (Onaninso bokosi.)
17 Werengani Genesis 49:27. Yakobo ananena kuti a fuko la Benjamini adzakhala odziwa kumenya nkhondo ndipo anawayerekeza ndi mimbulu. (Ower. 20:15, 16; 1 Mbiri 12:2) Mawu akuti “m’mawa” kapena kuti kumayambiriro kwa ufumu wa Isiraeli, Sauli yemwe anali wa fuko la Benjamini ndi amene anali woyambirira kukhala mfumu. Iye anali msilikali wamphamvu komanso wolimba mtima polimbana ndi Afilisiti. (1 Sam. 9:15-17, 21) “Madzulo,” kapena kuti kumapeto kwa ufumuwo, Mfumukazi Esitere ndi Moredikayi, omwe anali a fuko la Benjamini, anapulumutsa Aisiraeli kuti asaphedwe mu ufumu wa Perisiya.—Esitere 2:5-7; 8:3; 10:3.
18. Kodi tingatsanzire bwanji kukhulupirika kwa mbadwa za Benjamini?
18 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Mosakayikira a fuko la Benjamini ayenera kuti ankanyadira poona kuti mmodzi mwa iwo anakhala mfumu pokwaniritsa lonjezo limene anapatsidwa. Komabe pamene Yehova anapereka ufumuwo kwa Davide, yemwe anali wa fuko la Yuda, anthu a fuko la Benjamini anagwirizana ndi kusinthako. (2 Sam. 3:17-19) Patapita zaka zambiri pamene mafuko ena anaukira fuko la Yuda, a fuko la Benjamini anakhalabe okhulupirika kwa Ayuda ndi mfumu imene Yehova anasankha. (1 Maf. 11:31, 32; 12:19, 21) Ifenso masiku ano tizithandiza mokhulupirika amene Yehova wawasankha kuti azitsogolera anthu ake.—1 Ates. 5:12.
19. Kodi ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira ungatithandize bwanji?
19 Ulosi umene Yakobo ananena atatsala pang’ono kumwalira ndi wothandiza kwambiri. Kuona mmene unakwaniritsidwira kumatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri maulosi opezeka m’Mawu a Yehova. Komanso kuganizira madalitso amene ana a Yakobo anapatsidwa kumatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti tizisangalatsa Yehova.
NYIMBO NA. 128 Tipirire Mpaka Mapeto
a Popereka madalitso kwa ana ake 4 oyambirira, Yakobo anayamba ndi mwana wamkulu kukamalizira wamng’ono, koma podalitsa ana ake ena 8, iye sanatsatire dongosolo limeneli.