Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 June tsamba 20-25
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Afike Poyamba Kutumikira Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Afike Poyamba Kutumikira Yehova
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUDZIWA CHIMENE CHIKUMULEPHERETSA KUPITA PATSOGOLO
  • MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIKONDA KWAMBIRI YEHOVA
  • MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIONA KUTI KUTUMIKIRA YEHOVA NDI KOFUNIKA KWAMBIRI
  • MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIPIRIRA MAVUTO OMWE ANGAKUMANE NAWO
  • MUZISONYEZA WOPHUNZIRA WANU KUTI MUMAMUKHULUPIRIRA
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 June tsamba 20-25

NKHANI YOPHUNZIRA 27

NYIMBO NA. 79 Athandizeni Kukhala Olimba

Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Afike Poyamba Kutumikira Yehova

“Khalani ndi chikhulupiriro cholimba . . . khalani amphamvu.”​—1 AKOR. 16:13.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene tingachite kuti tithandize wophunzira Baibulo kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kukhala wolimba mtima n’kusankha kuti azitumikira Yehova.

1-2. (a) N’chifukwa chiyani ophunzira Baibulo ena amazengereza kuyamba kutumikira Yehova? (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

KODI pa nthawi ina inunso munazengereza kukhala wa Mboni za Yehova? Mwina munkaopa kuti anzanu, ogwira nawo ntchito kapena achibale akhumudwa mukakhala wa Mboni. Kapenanso munkaona kuti simungakwanitse kutsatira mfundo za Mulungu. Ngati ndi choncho, mungamvetse chifukwa chake ophunzira Baibulo ena amazengereza kuti asankhe kuyamba kutumikira Yehova.

2 Yesu anazindikira kuti zinthu ngati zimenezi zikhoza kulepheretsa munthu kuyamba kutumikira Yehova. (Mat. 13:20-22) Komabe iye sanasiye kuthandiza anthu amene ankazengereza kumutsatira. M’malomwake anaphunzitsa ophunzira ake kudziwa mmene angathandizire anthu oterowo (1) kudziwa zinthu zomwe zikuwalepheretsa kupita patsogolo, (2) kukonda kwambiri Yehova, (3) kuona zimene ayenera kuika pamalo oyamba, komanso (4) kulimbana ndi mavuto omwe akukumana nawo. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene Yesu anauza ophunzira akezi tikamagwiritsa ntchito buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale pothandiza wophunzira Baibulo kuti azitumikira Yehova?

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUDZIWA CHIMENE CHIKUMULEPHERETSA KUPITA PATSOGOLO

3. Kodi mwina n’chiyani chinkalepheretsa Nikodemo kukhala wotsatira wa Yesu?

3 Nikodemo, yemwe anali mmodzi wa oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda, pa nthawi ina anali ndi vuto lomwe linkamulepheretsa kukhala wophunzira wa Yesu. Patangopita miyezi 6 kuchokera pamene Yesu anayamba utumiki wake, Nikodemo anazindikira kuti Yesu anatumidwa ndi Mulungu. (Yoh. 3:1, 2) Koma iye anasankha kukumana ndi Yesu mwamseri “chifukwa ankaopa Ayuda.” (Yoh. 7:13; 12:42) Mwina iye ankaganiza kuti ataya zinthu zambiri akakhala wophunzira wa Yesu.a

4. Kodi Yesu anathandiza bwanji Nikodemo kudziwa zimene Mulungu ankafuna kuti iye achite?

4 Nikodemo ankadziwa Chilamulo, komabe ankafunika kuthandizidwa kuti adziwe zimene Yehova ankafuna kuti iye achite. Ndiye kodi Yesu anamuthandiza bwanji? Yesu sanaumire nthawi yake ndipo anakonza zokumana ndi Nikodemo usiku. Yesu anamufotokozera bwinobwino zimene ankafunika kuchita kuti akhale wotsatira wake. Pomuuza zimene ankayenera kuchita, anamufotokozera momveka bwino kuti ankayenera kulapa machimo, kubatizidwa m’madzi komanso kukhulupirira Mwana wa Mulungu.​—Yoh. 3:5, 14-21.

5. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kudziwa zimene zikumulepheretsa kupita patsogolo?

5 Ngakhale wophunzira Baibulo yemwe amamvetsa bwino Malemba, angafunike kuthandizidwa kudziwa zimene zikumulepheretsa kupita patsogolo. Mwachitsanzo, zina zomulepheretsa zingakhale ntchito yolembedwa kapenanso kutsutsidwa ndi achibale. Choncho muzipeza nthawi yoti mumuthandize. Mwina mungamupemphe kuti mukayende kapenanso kumuitanira kunyumba kwanu. Pa nthawi ngati imeneyi, mungamupemphe kuti amasuke n’kukufotokozerani mavuto amene akukumana nawo. Muzilimbikitsa wophunzirayo kusintha ngati pakufunikira kutero, osati kuti akusangalatseni inuyo, koma kuti asonyeze kuti amakonda Yehova.

6. Kodi mungathandize bwanji wophunzira Baibulo kuti alimbe mtima n’kuyamba kutsatira zimene akuphunzira? (1 Akorinto 16:13)

6 Wophunzira Baibulo akamakhulupirira kuti Yehova angamuthandize kutsatira mfundo za m’Baibulo, angalimbe mtima n’kuyamba kutsatira zimene akuphunzira. (Werengani 1 Akorinto 16:13.) Zomwe mumachita zikufanana ndi zimene mphunzitsi amachita. Pa nthawi imene munali pasukulu, kodi munkakonda mphunzitsi wotani? Mosakayikira, munkakonda mphunzitsi amene ankaleza nanu mtima n’kumakuthandizani kuona kuti mungathe kuchita zambiri. Mofanana ndi zimenezi, mphunzitsi wabwino wa Baibulo amaphunzitsa wophunzirayo kudziwa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita, komanso amamutsimikizira kuti Yehova angamuthandize kusintha ngati pakufunika kutero. Kodi mungatani kuti mukhale mphunzitsi wotereyu?

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIKONDA KWAMBIRI YEHOVA

7. Kodi Yesu anathandiza bwanji anthu amene ankamumvetsera kuti azikonda kwambiri Yehova?

7 Yesu ankadziwa kuti kukonda Mulungu kukanathandiza ophunzira ake kuti azigwiritsa ntchito zimene ankaphunzira. Nthawi zambiri iye ankawaphunzitsa zinthu zowathandiza kuti azikonda kwambiri Atate wawo wakumwamba. Mwachitsanzo, pa nthawi ina iye anayerekezera Yehova ndi bambo amene amapereka zinthu zabwino kwa ana ake. (Mat. 7:9-11) N’kutheka kuti ena mwa anthu amene ankamumvetsera sanakhalepo ndi bambo wachikondi ngati ameneyu. Taganizirani mmene iwo anamvera Yesu atafotokoza fanizo la bambo wachifundo amene analandira ndi manja awiri mwana wake amene anasochera. Iwo ayenera kuti anaona mmene Yehova amakondera ana ake a padziko lapansi.​—Luka 15:20-24.

8. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kuti azikonda kwambiri Yehova?

8 Inunso mungathandize wophunzira Baibulo kuti azikonda kwambiri Yehova pomamufotokozera nthawi zonse makhalidwe abwino amene Mulungu ali nawo. Pa phunziro lililonse muzimuthandiza kuona kugwirizana komwe kulipo pakati pa zimene akuphunzira ndi mfundo yakuti Yehova ndi wachikondi. Mukamakambirana zokhudza dipo, muzimufotokozera mmene dipolo limamukhudzira. (Aroma 5:8; 1 Yoh. 4:10) Wophunzirayo akhoza kuyamba kukonda kwambiri Yehova akamaganizira kuti Yehovayo amamukonda iyeyo payekha.​—Agal. 2:20.

9. Kodi n’chiyani chinathandiza Michael kuti ayambe kutumikira Yehova?

9 Taganizirani chitsanzo cha Michael wa ku Indonesia. Iye anakulira m’banja la Mboni koma sanabatizidwe. Ali ndi zaka 18, anapita kudziko lina kukagwira ntchito yoyendetsa magalimoto akuluakulu. Kenako anakwatira koma anasiya banja lake ku Indonesia n’kupita kukapitiriza kugwira ntchito kudziko lina. Pa nthawiyi mkazi wake ndi mwana wake anayamba kuphunzira Baibulo ndipo ankapita patsogolo. Mayi ake atamwalira, Michael anaganiza zobwerera ku Indonesia kuti azikasamalira bambo ake ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Pokambirana mbali yakuti “Fufuzani Mozama” mu phunziro 27, m’buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, Michael anakhudzidwa kwambiri. Poganizira mmene Yehova anamvera ataona Mwana wake akuvutika, Michael anagwetsa misozi. Iye anayamba kuyamikira kwambiri mphatso ya dipo ndipo izi zinamuthandiza kuti asinthe zinthu pa moyo wake n’kubatizidwa.

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIONA KUTI KUTUMIKIRA YEHOVA NDI KOFUNIKA KWAMBIRI

10. Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kuti aziona kuti kuika Yehova pamalo oyamba ndi kofunika kwambiri? (Luka 5:5-11) (Onaninso chithunzi.)

10 Ophunzira a Yesu anamuzindikira mwamsanga kuti iye anali Mesiya. Koma ankafunika kuthandizidwa kuti aziona ntchito yolalikira kukhala yofunika kwambiri pa moyo wawo. Petulo ndi Andireya anali atakhala ophunzira a Yesu kwa kanthawi pamene iye anawauza kuti azimutsatira nthawi zonse. (Mat. 4:18, 19) Iwo ankachita bizinesi ya nsomba ndipo n’kutheka kuti ankachita limodzi ndi Yakobo ndi Yohane. (Maliko 1:16-20) Pamene Petulo ndi Andireya “anasiya maukonde awo,” ayenera kuti anapeza njira zoti azipeza zofunika za mabanja awo kwinaku akutsatira Yesu. Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti aziona ntchito yolalikira kukhala yofunika kuposa ndalama? Nkhani ya m’buku la Luka imatifotokozera kuti Yesu anachita chodabwitsa chomwe chinawathandiza kuti azikhulupirira kwambiri kuti Yehova adzawapatsa zosowa zawo.​—Werengani Luka 5:5-11.

Petulo ndi Andireya akusiya maukonde awo pomwe Yesu akuwaitana kuti amutsatire. Asodzi ena atsala pomwe akuluka maukonde awo.

Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yesu poona mmene anathandizira ophunzira ake kuti aziika Yehova pamalo oyamba? (Onani ndime 10)b


11. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji zimene zinachitika pa moyo wathu kuti tilimbikitse chikhulupiriro cha amene tikuphunzira naye Baibulo?

11 Sitingathe kuchita zodabwitsa ngati Yesu, koma tingathe kufotokozera wophunzira Baibulo mmene Yehova amathandizira anthu amene amaika kumulambira pamalo oyamba. Mwachitsanzo, kodi mumakumbukira mmene Yehova anakuthandizirani mutayamba kupezeka pamisonkhano yampingo? Mwina munkafunika kukambirana ndi abwana anu kuti simuzigwiranso ovataimu ngati inkaombana ndi nthawi yoti mukapezeke kumisonkhano. Mukamamuuza zimene zinakuchitikiranizo, muzimufotokozera mmene chikhulupiriro chanu chinalimbira kuona mmene Yehova akukuthandizirani pa zimene munasankha kuti muziika kumulambira pamalo oyamba.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kupita kuphunziro lathu ndi ofalitsa osiyanasiyana? (b) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mavidiyo pothandiza wophunzira wanu? Perekani chitsanzo.

12 Wophunzira wanu angapindulenso kumva mmene Akhristu ena anasinthira zinthu pa moyo wawo kuti aziika kulambira Yehova pamalo oyamba. Choncho mukamachititsa phunziro la Baibulo, muzipita ndi abale ndi alongo omwe anakumana ndi zinthu zosiyanasiyana pa moyo wawo. Muziwafunsa kuti afotokoze mmene anaphunzirira choonadi komanso zimene anachita kuti aziika kutumikira Yehova pamalo oyamba. Kuwonjezera pamenepo, muzionera ndi wophunzira wanuyo mavidiyo a pagawo lakuti “Fufuzani Mozama” kapena “Onani Zinanso” m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Mwachitsanzo, mukamaphunzira phunziro 37, mungakambirane mfundo za muvidiyo yakuti Yehova adzatisamalira.

MUZITHANDIZA WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI AZIPIRIRA MAVUTO OMWE ANGAKUMANE NAWO

13. Kodi Yesu anathandiza bwanji ophunzira ake kukonzekera kutsutsidwa?

13 Mobwerezabwereza, Yesu anauza ophunzira ake kuti adzazunzidwa ndi anthu ena ngakhalenso achibale awo. (Mat. 5:11; 10:22, 36) Chakumapeto kwa utumiki wake, iye anachenjeza ophunzirawo kuti akhoza kuphedwa chifukwa cholambira Yehova. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20; 16:2) Choncho anawauza kuti azikhala tcheru akamalalikira. Anawalangizanso kuti asamakangane ndi otsutsa komanso kuti azikhala osamala kwambiri.

14. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kukonzekera kutsutsidwa? (2 Timoteyo 3:12)

14 Tingathandize ophunzira kukonzekera kutsutsidwa powafotokozera zimene angayembekezere kukumana nazo kuchokera kwa ogwira nawo ntchito, anzawo komanso achibale. (Werengani 2 Timoteyo 3:12) Anzawo ena a kuntchito angamawanyoze chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Anthu ena ngakhalenso achibale angamanyoze zimene amakhulupirira. Tikawakonzekeretsa mwamsanga, zingawathandize kuti adzakhale okonzeka akamatsutsidwa.

15. N’chiyani chingathandize wophunzira Baibulo kuti apirire achibale ake akamamutsutsa?

15 Wophunzira Baibulo akamatsutsidwa ndi achibale, muzimulimbikitsa kuti aziganizira chomwe chachititsa achibalewo kuti akhumudwe. Mwina iwo angamaone kuti wachibale wawoyo wasocheretsedwa kapenanso zikhoza kungokhala kuti iwo amadana ndi a Mboni za Yehova. Ngakhalenso achibale ake a Yesu, pa nthawi ina sankasangalala ndi zimene iye ankachita. (Maliko 3:21; Yoh. 7:5) Muzithandiza wophunzirayo kuti azikhala woleza mtima komanso azilankhula mokoma mtima ndi ena kuphatikizapo achibale ake.

16. Kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kuti azifotokoza mwaluso zimene amakhulupirira?

16 Ngakhale kuti achibale ake angasonyeze chidwi, ndi bwino kuti wophunzirayo asamawafotokozere zinthu zambiri pa nthawi imodzi kuopera kuti akhoza kutopa nazo ndipo izi zingachititse kuti asafunenso kumvetsera. Choncho muzimulimbikitsa kuti azifotokoza zimene amakhulupirira m’njira yoti adzathe kukambirananso nthawi ina. (Akol. 4:6) Mwinanso angalimbikitse achibale akewo kuti azilowa pa jw.org. Izi zingawathandize kuti aziphunzira zambiri zokhudza a Mboni za Yehova pa nthawi yawo.

17. Kodi mungathandize bwanji wophunzira wanu kuti azitha kuyankha anthu amene amakhala ndi maganizo olakwika okhudza a Mboni za Yehova? (Onaninso chithunzi.)

17 Mungagwiritse ntchito gawo la pa jw.org lakuti “Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri” pothandiza wophunzira wanu kudziwa mmene angayankhire mafunso omwe achibale ndi anzake a kuntchito angamufunse. (2 Tim. 2:24, 25) Kumapeto kwa phunziro lililonse m’buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, muzikambirana gawo lakuti “Zimene Ena Amanena.” Muzimulimbikitsa wophunzirayo kuti aziyeserera kuyankha m’mawu akeake. Muzimuthandiza ngati akufunika kukonza mayankho akewo kuti akhale abwino. Zimenezi zingamuthandize kuti azifotokoza molimba mtima zimene amakhulupirira.

Mlongo akuthandiza wophunzira Baibulo kukonzekera kuti azilalikira kwa ena. Wophunzirayo akulalikira mlongoyo pogwiritsa ntchito kapepala kakuti “Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?”

Muzikonzekera ndi wophunzira wanu pomuthandiza kuti aziuza ena zimene amakhulupirira (Onani ndime 17)c


18. Kodi tingathandize bwanji wophunzira wathu kuti ayambe kulalikira ndi mpingo? (Mateyu 10:27)

18 Yesu analamula ophunzira ake kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu onse. (Werengani Mateyu 10:27.) Wophunzira akayamba msanga kufotokozera ena zimene amakhulupirira, m’pamenenso amayamba kudalira kwambiri Yehova. Ndiye kodi mungamuthandize bwanji kuti akhale ndi cholinga chimenechi? Pakalengezedwa za ntchito yapadera yolalikira, muzilimbikitsa wophunzirayo kuti aziganizira zimene angachite kuti ayenerere kukhala wofalitsa. Mungamufotokozere chifukwa chake ambiri amaona kuti zimakhala zosavuta kuyamba kulalikira pa nthawi ngati imeneyi. Angapindulenso ngati atakhala ndi cholinga choti azikamba nkhani pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Akamakwaniritsa cholinga chimenechi, adzaphunzira mmene angafotokozere bwino zimene amakhulupirira.

MUZISONYEZA WOPHUNZIRA WANU KUTI MUMAMUKHULUPIRIRA

19. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira ophunzira ake, nanga tingamutsanzire bwanji?

19 Asanapite kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti, nthawi ina, iwo adzakhalanso naye limodzi. Sankadziwa kuti Yesu ankatanthauza kuti iwo adzapita kumwamba. Komabe Yesu ankangoganizira za kukhulupirika kwawo, osati kukayikira kwawo. (Yoh. 14:1-5, 8) Iye ankadziwa kuti pankafunika nthawi yokwanira kuti iwo amvetse zinthu zina, monga zokhudza chiyembekezo chopita kumwamba. (Yoh. 16:12) Ifenso tizisonyeza kuti timakhulupirira kuti wophunzira wathu amafuna kusangalatsa Yehova.

Wophunzira akayamba msanga kufotokozera ena zimene amakhulupirira, m’pamenenso amayamba kudalira kwambiri Yehova

20. Kodi mlongo wina wa ku Malawi anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira wophunzira wake?

20 Tisamakayikire kuti wophunzira wathu amafuna kuchita zinthu zoyenera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina wa ku Malawi dzina lake Chifundo. Iye ankaphunzira Baibulo ndi mayi wina wa Chikatolika dzina lake Alinafe pogwiritsa ntchito buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Atafika kumapeto kwa phunziro 14, Chifundo anafunsa wophunzirayo maganizo ake pa nkhani yogwiritsa ntchito zifaniziro polambira. Alinafe atakwiya ndi funsoli anayankha kuti: “Munthu aliyense angasankhe kugwiritsa ntchito zifaniziro kapena ayi.” Chifundo ankangoganiza kuti phunzirolo silipitiriranso, koma moleza mtima anapitirizabe kuphunzira ndi Alinafe akumayembekezera kuti tsiku lina adzamvetsa bwino mfundo imeneyi. Patapita miyezi yochepa, Chifundo anafunsa wophunzirayu funso limene lili m’phunziro 34 kuti: “Pofika pano, kodi kuphunzira Baibulo komanso zokhudza Mulungu woona Yehova kwakuthandizani bwanji?” Pofotokoza zimene Alinafe anayankha, Chifundo anati: “Iye anafotokoza mfundo zambiri zosangalatsa. Imodzi mwa mfundozo inali yakuti a Mboni za Yehova sachita zilizonse zimene Baibulo silivomereza.” Pasanapite nthawi yaitali, Alinafe anasiya kugwiritsa ntchito zifaniziro ndipo anabatizidwa.

21. Kodi tingalimbikitse bwanji wophunzira kuti akhale wofunitsitsa kusankha kutumikira Yehova?

21 Ngakhale kuti Yehova ndi “amene amakulitsa,” tili ndi udindo wothandiza wophunzira Baibulo kuti apite patsogolo. (1 Akor. 3:7) Pali zambiri zimene timachita kuwonjezera pa kumuphunzitsa kuti adziwe zimene Mulungu amafuna. Timamuthandiza kuti azikonda kwambiri Yehova. Timamulimbikitsanso kuti azisonyeza kuti amakonda Yehova ndiponso kumuika pamalo oyamba. Timamuphunzitsanso kuti azidalira Yehova akakumana ndi mavuto. Tikamamusonyeza kuti timamudalira, timamuthandiza kuti asamakayikire kuti angathe kutsatira mfundo za Yehova komanso kusankha kumutumikira.

KODI TINGATHANDIZE BWANJI WOPHUNZIRA BAIBULO KUTI . . .

  • adziwe zimene zikumulepheretsa kupita patsogolo?

  • azikonda kwambiri Yehova?

  • aziika Yehova pamalo oyamba?

NYIMBO NA. 55 Musaope

a Patapita zaka ziwiri ndi hafu kuchokera pamene anakumana ndi Yesu, Nikodemo anali adakali mmodzi wa oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda. (Yoh. 7:45-52) Olemba mbiri ena amanena kuti Nikodemo anakhala wophunzira pambuyo poti Yesu waphedwa.​—Yoh. 19:38-40.

b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Petulo ndi asodzi ena akusiya bizinesi yawo ya nsomba kuti azitsatira Yesu.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Mlongo akuthandiza wophunzira Baibulo kukonzekera kuti azilalikira kwa ena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena