Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 August tsamba 14-19
  • Musamakayikire Kuti Yehova Amakhululuka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musamakayikire Kuti Yehova Amakhululuka
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMAKHULULUKA
  • N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUTI TIZIKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA WATIKHULULUKIRA?
  • TISAMAIWALE ZIMENE YEHOVA AMAKUMBUKIRA
  • PITIRIZANI KUKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA AMAKHULULUKA
  • Timapindula ndi Kukhululuka kwa Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Yehova, Mulungu “Wokhululukira”
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”
    Yandikirani Yehova
  • Yehova Amakhululuka Kwambiri Kuposa Aliyense
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 August tsamba 14-19

NKHANI YOPHUNZIRA 34

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu ndi Chiyembekezo Chathu Ndipo Timakudalirani

Musamakayikire Kuti Yehova Amakhululuka

“Inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.”​—SAL. 32:5.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti Yehova amakhululuka. Ndipo tiona umboni wa m’Baibulo wotitsimikizira kuti iye amakhululukira anthu amene alapa.

1-2. Kodi anthu omwe alapa amamva bwanji Yehova akawakhululukira? (Onani chithunzi.)

MFUMU Davide inkadziwa bwino mmene munthu amamvera akamadziimba mlandu chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyo. (Sal. 40:12; 51:3, timawu tapamwamba) Iye anali atachitapo machimo akuluakulu pa moyo wake. Koma analapa mochokera pansi pa mtima ndipo Yehova anamukhululukira. (2 Sam. 12:13) Choncho ankadziwanso mmene munthu amamvera Yehova akamukhululukira.​—Sal. 32:1.

2 Mofanana ndi Davide, inunso mungasangalale ngati mutazindikira kuti Yehova wakuchitirani chifundo. N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova ndi wofunitsitsa kutikhululukira machimo athu, ngakhale akuluakulu. Iye amatikhululukira tikavomereza machimo athu, tikalapa mochokera pansi pa mtima komanso tikamayesetsa kuti tisawabwerezenso. (Miy. 28:13; Mac. 26:20; 1 Yoh. 1:9) Ndipo n’zosangalatsa kudziwa kuti Yehova akakhululuka, zimakhala ngati kuti machimowo sanachitike n’komwe.​—Ezek. 33:16.

Mfumu Davide ali pakhonde ndipo akuimba pogwiritsa ntchito zeze.

Mfumu Davide anapeka nyimbo zambiri za masalimo zomwe zimafotokoza za kukhululuka kwa Yehova (Onani ndime 1-2)


3-4. Kodi mlongo wina anamva bwanji atabatizidwa, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Koma nthawi zina, ena zingawavute kukhulupirira kuti Yehova wawakhululukira. Zimenezi ndi zimene zinachitikira Jennifer yemwe anakulira m’banja la Mboni. Iye ali wachinyamata anayamba kuchita zoipa ndipo ankakhala moyo wachiphamaso. Patapita zaka, iye anabwerera kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Jennifer anati: “Poyamba ndinkakonda kuchita chiwerewere, kuledzera, kukwiya kwambiri komanso ndinkakonda kwambiri ndalama. Ndinkadziwa kuti ngati nditapempha Yehova kuti andikhululukire n’kulapa, nsembe ya Khristu ingandithandize kukhala woyera. Koma ndinkalephera kuutsimikizira mtima wanga kuti Mulungu wandikhululukira.”

4 Kodi nthawi zina inunso zimakuvutani kukhulupirira kuti Yehova wakukhululukirani zimene munalakwitsa? Yehova amafuna musamakayikire kuti iye wakuchitirani chifundo ndipo amafuna muzisangalala ngati mmene Davide anachitira atakhululukidwa. Munkhaniyi, tikambirana chifukwa chake sitiyenera kukayikira kuti Yehova amakhululuka. Tionanso chimene chingatithandize kuti tizikhulupirira zimenezi.

TISAMAKAYIKIRE KUTI YEHOVA AMAKHULULUKA

5. Kodi Satana amafuna tizikayikira chiyani? Perekani chitsanzo.

5 Tikamakhulupirira kuti Yehova amakhululuka, tingapewe umodzi mwa misampha ya Satana. Kumbukirani kuti Satana amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe kuti atisiyitse kutumikira Yehova. Kuti akwaniritse cholinga chakechi, Satana angachititse kuti tizikayikira kuti Mulungu angatikhululukire machimo athu. Chitsanzo pa nkhaniyi, ndi munthu wina wa ku Korinto yemwe anachotsedwa mumpingo chifukwa cha chiwerewere. (1 Akor. 5:1, 5, 13) Munthuyo atalapa, Satana ankafuna kuti abale ndi alongo ake asamukhululukire ndipo asamulandirenso mumpingo. Pa nthawi imodzimodziyo, ankafuna kuti munthu wolapayo azidzimva kuti sangakhululukidwe. Ankafuna kuti iye ‘akhale ndi chisoni chopitirira malire mpaka kutaya mtima’ n’kusiya kutumikira Yehova. Satana sanasinthe, amagwiritsabe ntchito msampha umenewu. Koma ife “tikudziwa bwino ziwembu zake.”​—2 Akor. 2:5-11.

6. N’chiyani chingatithandize kuti tisamadziimbe mlandu?

6 Tikamakhulupirira kuti Yehova watikhululukira, sitingamadziimbe mlandu. Mwachibadwa, tikachimwa timadziimba mlandu. (Sal. 51:17) Zimenezitu n’zabwino chifukwa chikumbumtima chathu chingatilimbikitse kuti tisinthe n’kukonza zinthu. Komabe tikamadziimba mlandu kwa nthawi yaitali pambuyo poti talapa, tingataye mtima n’kusiya kutumikira Yehova. (2 Akor. 7:10, 11) Koma tikamavomereza kuti Yehova watikhululukira timasiya kudziimba mlandu. Zikatero timatumikira Yehova mosangalala komanso tili ndi chikumbumtima chabwino monga mmene iyeyo amafunira. (Akol. 1:10, 11; 2 Tim. 1:3) Koma kodi tingautsimikizire bwanji mtima wathu kuti Yehova watikhululukira?

N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE KUTI TIZIKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA WATIKHULULUKIRA?

7-8. Kodi Yehova anadzifotokoza bwanji kwa Mose, nanga zimenezi zikutitsimikizira chiyani? (Ekisodo 34:6, 7)

7 Muziganizira mmene Yehova anafotokozera zokhudza iyeyo. Mwachitsanzo, taonani zimene Yehova anauza Mose paphiri la Sinai.a (Werengani Ekisodo 34:6, 7.) Pa zinthu zonse zimene Yehova anafotokoza zokhudza makhalidwe ndi njira zake, iye anasankha kudzifotokoza kuti ndi “Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima.” Ndiye kodi Mulungu wotereyu angalephere kukhululukira mtumiki wake yemwe walapa mochokera pansi pa mtima? Ayi ndithu. Kulephera kukhululuka kungakhale kupanda chifundo komanso kuuma mtima, zinthu zimene Yehova sangachite ngakhale pang’ono.

8 Timakhulupirira Yehova akamanena kuti iye ndi wachifundo chifukwa sanganame. (Sal. 31:5) Choncho sitingakayikire ngakhale pang’ono zimene amanena. Ngati mumadziimbabe mlandu chifukwa cha zimene munalakwitsa m’mbuyo, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira kuti Yehova ndi wachifundo ndiponso wokoma mtima, komanso kuti sangalephere kukhululukira aliyense amene walapa? Ndiye kodi pali chifukwa choti ndizikayikirira kuti wandikhululukira ineyo?’

9. Kodi mawu akuti kukhululuka amanena za chiyani? (Salimo 32:5)

9 Muziganizira zimene Baibulo limanena zokhudza kukhululuka kwa Yehova. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Davide anafotokoza pa nkhaniyi. (Werengani Salimo 32:5.) Iye anati: “Inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.” Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “kukhululuka,” amatanthauza “kunyamula” kapena “kuchotsa.” Pamene Yehova anakhululukira Davide, zinali ngati wanyamula machimo ake n’kuwachotsa. Zitatero Davide anayamba kumva bwino chifukwa zinali ngati watula mtolo wolemera. (Sal. 32:2-4) Ifenso Yehova akatikhululukira tikhoza kuyamba kumva bwino mumtima. Tikalapa mochokera pansi pa mtima, tisamapitirize kudziimba mlandu chifukwa cha machimo amene Yehova wawanyamula ndi kuwachotsa.

10-11. Kodi mawu akuti “wokonzeka kukhululuka” amatiuza chiyani zokhudza Yehova? (Salimo 86:5)

10 Werengani Salimo 86:5. Palembali, Davide ananena kuti Yehova ndi “wokonzeka kukhululuka.” Pofotokoza mawuwa, buku lina linanena kuti: “Yehova ndi ‘wokhululuka,’ umu ‘ndi mmene alili.’” N’chifukwa chiyani Yehova amakhululuka? Mbali yotsatira ya vesili imati: “Mumasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana inu.” Monga tinaonera munkhani yapita ija, chikondi chokhulupirika ndi chimene chimachititsa Yehova kuti asamasiye atumiki ake okhulupirika. Chikondichi ndi chimene chimachititsanso kuti ‘azikhululukira ndi mtima wonse’ anthu onse amene alapa. (Yes. 55:7) Ngati nthawi zina zimakuvutani kukhulupirira kuti Yehova wakukhululukirani, mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimakhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu wokhululuka, yemwe amakhala wokonzeka kukhululukira onse omwe alapa ndipo amupempha kuti awasonyeze chifundo? Ndiye kodi sindiyenera kukhulupirira kuti anandikhululukiranso ineyo nditamupempha kuti andichitire chifundo?’

11 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amamvetsa mmene anatipangira komanso kuti si ife angwiro. (Sal. 139:1, 2) Zimenezi zafotokozedwa bwino musalimo linanso la Davide lomwe limatithandiza kuti tizikhulupirira kuti Yehova amakhululuka.

TISAMAIWALE ZIMENE YEHOVA AMAKUMBUKIRA

12-13. Mogwirizana ndi Salimo 103:14, kodi Yehova amakumbukira chiyani zokhudza ifeyo, nanga zimenezi zimamulimbikitsa kuchita chiyani?

12 Werengani Salimo 103:14. Davide ananena kuti Yehova “amakumbukira kuti ndife fumbi.” Ndi mawu amenewa, Davide anafotokoza chifukwa chake Yehova amakhala wokonzeka kukhululukira atumiki ake omwe alapa. Chifukwa chake n’chakuti amadziwa kuti ndife ochimwa. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tionenso mawu a Davidewa.

13 Davide ananena kuti Yehova ‘amadziwa bwino mmene anatipangira.’ Iye anapanga Adamu “kuchokera kudothi.” Choncho amadziwa kuti ngakhale munthu wangwiro amafunika zinthu zina monga kudya, kugona komanso kupuma. (Gen. 2:7) Koma pamene Adamu ndi Hava anachimwa, anthu anakhala fumbi, kapena kuti dothi, m’njira inanso. Popeza kuti ndife mbadwa zawo, tinatengera uchimo womwe umachititsa kuti tizichita zoipa. Sikuti Yehova amangodziwa kuti ndife ochimwa. Davide ananena kuti iye ‘amakumbukira’ zimenezi. Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “kukumbukira,” angatanthauze kuchita zinthu mwachifundo. Tingati mawu a Davidewa akutanthauza kuti Yehova amamvetsa kuti nthawi zina tingalakwitse zinthu. Ndipo zimenezo zikachitika ifeyo n’kulapa mochokera pansi pa mtima, amatisonyeza chifundo n’kutikhululukira.​—Sal. 78:38, 39.

14. (a) Kodi Davide anafotokoza kuti kukhululuka kwa Yehova kumafika mpaka pati? (Salimo 103:12) (b) Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Yehova anakhululukira Davide? (Onani bokosi lakuti, “Yehova Amakhululuka Komanso Amaiwala.”)

14 Kodi Yehova amakhululuka kufika pati? (Werengani Salimo 103:12.) Davide ananena kuti Yehova akakhululuka, amaika machimo athu “kutali ndi ife” ngati “mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa.” Nthawi zonse kum’mawa kumatalikirana kwambiri ndi kumadzulo ndipo mbali ziwirizi sizingakumane. Ndiye kodi zimenezi zikutiuza chiyani zokhudza machimo amene Yehova watikhululukira? Buku lina linayerekezera zimenezi motere: “Mulungu akachotsa machimo athu n’kuwaika kutali ndi ife, zimakhala ngati wachotseratu chinthu moti ngakhale fungo lake silingamvekenso.” Tangoganizani, kafungo kenakake kangamuchititse munthu kukumbukira zinazake. Koma Yehova akakhululuka, zimakhala ngati wachotseratu kafungo kalikonse komwe kakanachititsa kuti akumbukire tchimo lathu n’kutiimba nalo mlandu.​—Ezek. 18:21, 22; Mac. 3:19.

Zithunzi: 1. Mfumu Davide ali padenga la nyumba yake ndipo akuona Batiseba a kusamba. 2. Akupemphera mochokera pansi pa mtima. 3. Akuganizira pomwe akulemba.

Yehova Amakhululuka Komanso Amaiwala

Yehova akatikhululukira, amaiwala machimo athu m’njira yoti m’tsogolo sangadzatiimbenso mlandu chifukwa cha zimene tinalakwitsazo. (Yes. 43:25) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Mfumu Davide. Nkhani yake ikusonyeza kuti tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ngakhale kuti tinalakwitsapo zinthu zina.

Davide anachitapo zinthu zoipa kwambiri kuphatikizapo chigololo komanso kupha. Koma chifukwa chakuti analapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova anamukhululukira. Davide anavomereza pamene ankamudzudzula, anasintha zochita zake ndipo pambuyo pake sanapatukenso pa kulambira koona.​—2 Sam. 11:1-27; 12:13.

Pofotokoza za moyo wa Davide, Yehova anauza Solomo kuti: ‘Uziyenda mʼnjira zanga ngati mmene bambo ako Davide anachitira, yemwe anali ndi mtima wokhulupirika komanso ankachita zoyenera.’ (1 Maf. 9:4, 5) Yehova sanatchulepo zimene Davide analakwitsa. M’malomwake, anangofotokoza kuti Davide anali munthu wokhulupirika ndiponso ankachita zoyenera. Yehova ‘anamupatsa mphoto yaikulu’ chifukwa cha kukhulupirika kwake.​—Sal. 13:6.

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Yehova akatikhululukira samaganizira zoipa zimene tinachitazo, koma zabwino zimene angatipatse nazo mphoto. (Aheb. 11:6) Choncho sitiyenera kupitiriza kumakumbukira machimo omwe tinachita m’mbuyomu, omwe Yehova anasankha kuwaiwala.

15. Kodi tingatani ngati timadziimbabe mlandu chifukwa cha zimene tinalakwitsa m’mbuyo?

15 Kodi mawu a Davide a mu Salimo 103, angatithandize bwanji kuti tizikhulupirira kuti Yehova amatikhululukira? Ngati timapitirizabe kudziimba mlandu chifukwa cha zimene tinalakwitsa m’mbuyo, tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaiwala zimene Yehova amakumbukira, kapena kuti kodi ndimaiwala kuti iye amakumbukira zoti ndine wochimwa komanso kuti amakhululukira munthu wochimwa yemwe walapa ngati ineyo? Kodi ndimakumbukira zimene Yehova wasankha kuziiwala, mwachitsanzo, machimo omwe anandikhululukira m’mbuyo omwe sangadzandiimbenso nawo mlandu?’ Yehova samangoganizira zimene tinalakwitsa m’mbuyo. Ndiye ifenso tisamachite zimenezi. (Sal. 130:3) Tikamakhulupirira kuti Yehova anatikhululukira, ifenso tidzadzikhululukira ndipo tidzapitirizabe kutumikira Yehova mosangalala.

16. Perekani chitsanzo chosonyeza kuopsa kodziimbabe mlandu chifukwa cha zimene tinalakwitsa. (Onaninso chithunzi.)

16 Taganizirani chitsanzo ichi: Kumangodziimba mlandu chifukwa cha zimene tinalakwitsa m’mbuyo, kuli ngati kuyendetsa galimoto tikumangoyang’ana pagalasi loonera kumbuyo. N’zoona kuti kuyang’ana pagalasili mwa apo ndi apo ndi kwabwino. Chifukwa kungakuthandizeni kupewa zoopsa zimene zikubwera kumbuyo kwanu. Koma kuti muyende bwino muyenera kumayang’ana kwambiri kutsogolo. Mofanana ndi zimenezi, zingakhale zothandiza kumayang’ana mwa apo ndi apo zimene tinalakwitsa m’mbuyo n’cholinga choti tiphunzirepo kanthu komanso tisadzabwerezenso zimene tinalakwitsazo. Koma ngati timaganizira kwambiri zimene tinalakwitsa, tingamadziimbe mlandu ndipo tingamalephere kuchita zambiri potumikira Yehova. M’malomwake tiyenera kumayang’ana kwambiri kutsogolo kumene tikupita. Tili pamsewu wopita kumoyo m’dziko latsopano la Mulungu kumene ‘sitidzakumbukiranso’ zinthu zoipa.​—Yes. 65:17; Miy. 4:25.

Bambo akuyendetsa galimoto ndipo akuyang’ana pagalasi loonera zakumbuyo.

Mofanana ndi dalaivala yemwe amafunika kuyang’ana kwambiri kutsogolo osati pagalasi loonera zakumbuyo, tiyenera kumaganizira kwambiri madalitso a m’tsogolo osati zimene tinalakwitsa m’mbuyo (Onani ndime 16)


PITIRIZANI KUKHULUPIRIRA KUTI YEHOVA AMAKHULULUKA

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kutsimikizira mtima wathu kuti Yehova amatikonda komanso amatikhululukira?

17 Tiyenera kupitiriza kutsimikizira mtima wathu kuti Yehova amatikonda komanso kutikhululukira. (1 Yoh. 3:19) Tikutero chifukwa Satana adzapitiriza kutichititsa kuti tiziona kuti Yehova samatikonda kapenanso sangatikhululukire. Iye amachita zonsezi n’cholinga choti tisiye kutumikira Yehova. Tingayembekezere kuti Satana awonjezera kuchita zimenezi, chifukwa akudziwa kuti watsala ndi kanthawi kochepa. (Chiv. 12:12) Koma tisalole kuti iye apambane.

18. Kodi tingatani kuti tizitsimikizira mtima wathu kuti Yehova amatikonda komanso kutikhululukira?

18 Kuti muzikhulupirira kwambiri zoti Yehova amakukondani, mungagwiritse ntchito mfundo zimene tinakambirana munkhani yapita ija. Kuti muzikhulupirira kwambiri kuti Yehova amakukhululukirani, muziganizira zimene Yehova anafotokoza zokhudza iyeyo. Muziganizira zimene Baibulo limanena zokhudza kukhululuka kwa Yehova. Musamaiwale kuti iye amadziwa bwino kuti ndinu wochimwa ndipo adzachita nanu zinthu mwachifundo. Muzikumbukiranso kuti akakhululuka amachita zimenezo ndi mtima wonse. Choncho mofanana ndi Davide yemwe sankakayikira kuti Yehova anamusonyeza chifundo, mungathe kunena kuti, “Zikomo Yehova chifukwa chondikhululukira ‘zolakwa zanga ndi machimo anga.’”​—Sal. 32:5.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti Yehova amatikhululukira?

  • N’chiyani chingatithandize kuti tizikhulupirira kuti Yehova amatikhululukira?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kutsimikizira mtima wathu kuti Yehova amatikhululukira?

NYIMBO NA. 1 Makhalidwe a Yehova

a Onani nkhani yakuti “Yandikirani Mulungu​—Yehova Anafotokoza Makhalidwe Ake” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2009.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena