NKHANI YOPHUNZIRA 35
NYIMBO NA. 121 Timafunika Kukhala Odziletsa
Zimene Zingatithandize Kulimbana ndi Zilakolako Zoipa
“Musalole kuti uchimo uzilamulirabe ngati mfumu mʼmatupi anu oti akhoza kufawo kuti muzitsatira zilakolako zawo.”—AROMA 6:12.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Nkhaniyi itithandiza (1) kuona zimene tingachite tikafooka komanso (2) kudziwa zimene tingachite tikamayesedwa.
1. Popeza kuti anthu onse si angwiro, kodi amalimbana ndi chiyani?
KODI munayamba mwalakalakapo kwambiri kuchita zimene Yehova sasangalala nazo? Ngati ndi choncho, musamaganize kuti munakumana ndi mayesero aakulu kuposa wina aliyense. Baibulo limati: “Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene anthu ena amakumana nawo.” (1 Akor. 10:13) Zimenezi zikutanthauza kuti zilakolako zoipa zilizonse zimene mungakhale nazo, pali enanso omwe akulimbana ndi zomwezo. Dziwani kuti Yehova adzakuthandizani kuti mupambane pankhondoyi.
2. Kodi Akhristu ena komanso anthu amene akuphunzira Baibulo angamalimbane ndi mayesero ati? (Onaninso zithunzi.)
2 Baibulo limanenanso kuti: “Munthu aliyense amayesedwa ndi chilakolako chake chimene chimamukopa ndi kumukola.” (Yak. 1:14) Chimene chingakope munthu wina, chingakhale chosiyana ndi chimene chingakope wina. Mwachitsanzo, Akhristu ena angakopedwe kuti achite chiwerewere ndi anthu omwe si amuna kapena akazi anzawo, pomwe ena angakopedwe kuti achite zimenezo ndi munthu yemwe ndi mwamuna kapena mkazi mnzawo. Ena omwe anasiya kuonera zolaula angayambirenso kukhala ndi chilakolako champhamvu chofuna kuchita zimenezo. Ambiri omwe anasiya kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kumwa mowa amakumananso ndi vuto limeneli. Izi ndi zilakolako zochepa chabe zimene Akhristu ena komanso anthu amene timaphunzira nawo Baibulo akulimbana nazo. Pa nthawi ina tonsefe tinamvapo ngati mtumwi Paulo, yemwe analemba kuti: “Pamene ndikufuna kuchita zinthu zabwino, zoipa zimakhala mkati mwangamu.”—Aroma 7:21.
Tingakumane ndi mayesero nthawi iliyonse komanso kulikonse (Onani ndime 2)c
3. Ngati munthu akulimbanabe ndi zilakolako zoipa, kodi angakhale ndi maganizo ati?
3 Ngati mukulimbanabe ndi zilakolako zoipa, mukhoza kumaona kuti mulibiretu mphamvu zomwe zingakuthandizeni kulimbana ndi mayesero. Mwinanso mungataye mtima n’kumaona kuti Yehova angakuweruzeni kuti ndinu munthu woipa chifukwa chokhala ndi zilakolako zoipazo. Koma dziwani kuti maganizo onsewa si oona. Kuti tidziwe chifukwa chake tikutero, munkhaniyi tipeza mayankho a mafunso awiri awa: (1) Kodi maganizo odziona kuti tilibiretu mphamvu komanso otichititsa kutaya mtima amachokera kwa ndani? (2) Kodi tingatani kuti tizilimbana ndi zilakolako zoipa?
MAGANIZO OMWE “WOIPAYO” AMAFUNA KUTI TIZIKHALA NAWO
4. (a) N’chifukwa chiyani Satana amafuna tizikhala ndi maganizo odziona kuti tilibe mphamvu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti tili ndi mphamvu zolimbana ndi mayesero?
4 Tikamayesedwa, Satana amafuna tizidzimva kuti tilibe mphamvu zolimbana ndi mayeserowo. Yesu anavomereza mfundo imeneyi pomwe anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa, koma mutiteteze kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Satana amakayikira kuti tingapitirize kumvera Yehova tikamayesedwa. (Yobu 2:4, 5) N’chifukwa chiyani Satana amaganiza chonchi? Iye anakopedwa ndi zilakolako zake ndipo analephera kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Choncho amaganiza kuti ife tili ngati iyeyo ndipo tikhoza kusiya kutumikira Yehova tikamayesedwa. Satana anafika pomaganiza kuti ngakhale Mwana wa Mulungu yemwe ndi wangwiro angasiye kumvera Yehova atayesedwa. (Mat. 4:8, 9) Koma kodi n’zoona kuti tilibe mphamvu zotha kulimbana ndi zilakolako zoipa? Ayi ndithu. Timagwirizana ndi zimene mtumwi Paulo analemba, kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa Mulungu amene amandipatsa mphamvu zimene ndikufunikira.”—Afil. 4:13.
5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amakhulupirira kuti tingapambane pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa?
5 Mosiyana ndi Satana, Yehova samakayikira kuti tingathe kulimbana ndi zilakolako zoipa. Tikudziwa bwanji zimenezi? Chifukwa Yehova ananeneratu kuti gulu lalikulu la atumiki ake okhulupirika lidzapulumuka pa chisautso chachikulu. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Yehova, yemwe sanganame, ananena kuti anthu ambiri, osati ochepa chabe, adzalowa m’dziko latsopano ali oyera ‘atachapa mikanjo yawo nʼkuiyeretsa mʼmagazi a Mwanawankhosa.’ (Chiv. 7:9, 13, 14) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova samaona kuti tilibe mphamvu zoti n’kulimbana ndi zilakolako zoipa.
6-7. N’chifukwa chiyani Satana amafuna kuti tizitaya mtima tikamalimbana ndi mayesero?
6 Satana samangofuna kuti tizidzimva kuti tilibe mphamvu, koma amafunanso kuti tizitaya mtima n’kumaona kuti Yehova sangatikonde chifukwa chokhala ndi zilakolako zoipa. Pamenepanso n’chifukwa chiyani Satana amafuna tiziganiza chonchi? Iye alibe chiyembekezo chifukwa anaweruzidwa ndi Yehova kuti si woyenera kudzakhala ndi moyo wosatha. (Gen. 3:15; Chiv. 20:10) Popeza kuti ifeyo tili ndi chiyembekezo chodzalandira madalitso amene Satana anawalephera, iye amafuna kuti ifenso tizitaya mtima. Koma ifeyo sitili ngati iyeyo ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova amafuna kutithandiza kuti tidzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Iye “sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.”—2 Pet. 3:9.
7 Zoona n’zakuti, tikamaganiza kuti tilibe mphamvu kapenanso tikamataya mtima kuti sitingathe kulimbana ndi zilakolako zoipa, timakhala tikuganiza mmene Satana amafunira. Kuzindikira zimenezi kungatithandize kuti titsimikize mtima kulimbana naye.—1 Pet. 5:8, 9.
MAGANIZO OMWE TIMAKHALA NAWO CHIFUKWA CHAKUTI NDIFE OCHIMWA
8. Kuwonjezera pa kuchita zoipa, kodi nthawi zina Baibulo limati uchimo umaimira chiyani? (Salimo 51:5) (Onaninso Tanthauzo la Mawu Ena.)
8 Kuwonjezera pa Satana, palinso chinthu china chomwe chimatichititsa kuti tizidziona kuti tilibe mphamvu komanso tizitaya mtima tikamalimbana ndi zilakolako zoipa. Kodi chinthu chimenechi n’chiyani? Ndi uchimo umene tinatengera kwa makolo athu oyamba.a—Yobu 14:4; werengani Salimo 51:5.
9-10. (a) Kodi Adamu ndi Hava anamva bwanji atazindikira kuti achimwa? (Onaninso chithunzi.) (b) Kodi timamva bwanji chifukwa chakuti ndife ochimwa?
9 Taganizirani mmene Adamu ndi Hava anamvera atachimwa. Iwo atangodziwa kuti sanamvere Yehova anabisala ndipo anavala masamba. Pofotokoza zimene zinachitikazi, buku la Insight on the Scriptures, limati: “Uchimo unawachititsa kuti azidziimba mlandu, azikhala ndi nkhawa, azidziona kuti ndi osatetezeka komanso azichita manyazi.” Zinali ngati Adamu ndi Hava atsekeredwa m’nyumba yomwe inali ndi zipinda 4 zimenezi. Iwo akanatha kutuluka chipinda china n’kulowa china, koma sakanatha kutuluka m’nyumbayi. Zinali zosatheka kuti apulumutsidwe ku uchimo.
10 Kwa ifeyo zinthu n’zosiyana ndi mmene zinalili kwa Adamu ndi Hava. Dipo, lomwe silimathandiza makolo athu oyambawa, limatiyeretsa ku uchimo komanso kutipatsa chikumbumtima choyera. (1 Akor. 6:11) Ngakhale zili choncho, tinatengera uchimowo. Choncho n’zosadabwitsa kuti nafenso timadziimba mlandu, kukhala ndi nkhawa, kudziona kuti ndife osatetezeka komanso kuchita manyazi. Ndipotu Baibulo limanena kuti anthu adakali mu ukapolo wa uchimo. Uchimowo ukulamulira “ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe ngati mmene anachimwira Adamu.” (Aroma 5:14) Ngakhale kuti zimenezi zingaoneke zofooketsa sitiyenera kutaya mtima kapenanso kudziona kuti tilibe mphamvu. Tingathe kupewa maganizo ofooketsawo. Kodi tingachite bwanji zimenezi?
Uchimo unachititsa Adamu ndi Hava kuti azidziimba mlandu, akhale ndi nkhawa, azidzimva kuti ndi osatetezeka komanso azichita manyazi (Onani ndime 9)
11. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikudzimva kuti tilibe mphamvu, nanga n’chifukwa chiyani? (Aroma 6:12)
11 Tikayamba kudziona kuti tilibe mphamvu moti sitingathe kulimbana ndi zilakolako zoipa, tiziona kuti uchimo ndi umene ukutiuza zimenezo ndipo tisamaumvere. Chifukwa chiyani? Chifukwa Baibulo limatiphunzitsa kuti sitiyenera kulola kuti uchimo ‘uzitilamulirabe ngati mfumu.’ (Werengani Aroma 6:12.) Zimenezi zikutanthauza kuti tingasankhe kuti tisamachite zoipa zimene timalakalaka. (Agal. 5:16) Yehova amakhulupirira kuti tingathe kulimbana ndi mayesero. Zikanakhala zosatheka si bwenzi akutiuza kuti tizichita zimenezo. (Deut. 30:11-14; Aroma 6:6; 1 Ates. 4:3) Apa n’zoonekeratu kuti tili ndi mphamvu zotha kulimbana ndi zilakolako zoipa.
12. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tayamba kutaya mtima, nanga n’chifukwa chiyani?
12 Mofanana ndi zimenezi, tikayamba kutaya mtima n’kumaona kuti Yehova sangatikonde chifukwa chakuti tili ndi zilakolako zoipa, tiziona kuti uchimo ndi umene ukutiuza zimenezo ndipo tisamaumvere. Chifukwa chiyani? Chifukwa Baibulo limatiphunzitsa kuti Yehova amamvetsa kuti ndife ochimwa. (Sal. 103:13, 14) Iye “amadziwa zonse” kuphatikizapo zimene zimachititsa kuti tichite zinthu zoipa chifukwa chakuti ndife ochimwa. (1 Yoh. 3:19, 20) Tikamapitiriza kulimbana ndi uchimo popewa zilakolako zoipa, Yehova angamatione kuti ndife oyera pamaso pake. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zimenezi?
13-14. Kodi kukhala ndi zilakolako zoipa kukutanthauza kuti ndife olephera? Fotokozani.
13 Baibulo limasonyeza kuti pali kusiyana pakati pa kuchita zoipa, komwe tingathe kudziletsa, ndi kulakalaka zoipa, komwe kumangobwera kokha. Mwachitsanzo, Akhristu ena a ku Korinto poyamba ankagonana amuna kapena akazi okhaokha. Paulo analemba kuti: “Ena a inu munali otero.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iwo atakhala Akhristu sankalakalakanso kuchita khalidwe loipali? Zingakhale zosamveka kuganiza choncho chifukwa nthawi zambiri khalidwe ngati limeneli limakhala lovuta kuti munthu asiye. Koma Akhristu amene ankadziletsa n’kumapewa kuchita zimene ankalakalaka ankakhala ovomerezeka kwa Yehova. Iye ankawaona kuti ‘asambitsidwa n’kukhala oyera.’ (1 Akor. 6:9-11) Izi ndi zimene zingachitikirenso inuyo.
14 Kaya mukulimbana ndi zilakolako zotani, mungathe kupambana. Ngakhale kuti simungathetseretu zilakolako zoipa, mungathe kudziletsa n’kumapewa “kuchita zofuna za thupi ndi maganizo [anu].” (Aef. 2:3) Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupambana pankhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa?
ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TIPAMBANE
15. Kuti tipambane pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa, n’chifukwa chiyani tiyenera kudzifufuza moona mtima?
15 Kuti tipambane polimbana ndi zilakolako zoipa, tiyenera kudziwa bwino zofooka zathu. Muzisamala kuti musamadzipusitse ndi “maganizo abodza.” (Yak. 1:22) Musamachepetse vuto pokhala ndi maganizo ngati akuti, ‘Pali anthu ena omwe amamwa kwambiri mowa kuposa ineyo.’ Musamaimbenso mlandu ena pa zimene mwalakwitsa pokhala ndi maganizo ngati akuti, ‘Si bwenzi ndikuonera zolaula zikanakhala kuti mkazi wanga amandikonda kwambiri.’ Kukhala ndi maganizo ngati amenewa kungachititse kuti zikhale zosavuta kugwera m’mayesero. Choncho musamayese kuchititsa zoipa kuoneka ngati zoyenera, ngakhale m’maganizo mwanu. Muzikhala okonzeka kukumana ndi zotsatirapo za zochita zanu.—Agal. 6:7.
16. Kodi tingatani kuti titsimikize mtima kuchita zoyenera?
16 Kuwonjezera pa kuzindikira zofooka zanu, muyenera kutsimikiza mtima kuti zofookazo zisakugonjetseni. (1 Akor. 9:26, 27; 1 Ates. 4:4; 1 Pet. 1:15, 16) Muziganizira zimene zimakukopani kuti mugwere m’mayesero enaake komanso nthawi imene zingakhale zovuta kwa inu kupirira mayeserowo. Mwachitsanzo, kodi mumaona kuti zikumakuvutani kulimbana ndi mayesero mukakhala kuti mwatopa kapena zikakhala kuti ndi usiku? Muzidzikonzekeretsa n’kudziwiratu zimene mungachite. Nthawi yabwino kuchita zimenezi ndi pamene mayeserowo asanafike.—Miy. 22:3.
17. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yosefe? (Genesis 39:7-9) (Onaninso zithunzi.)
17 Taganizirani zimene Yosefe anachita pamene mkazi wa Potifara ankamunyengerera kuti agone naye. Iye anachita zinthu motsimikiza ndipo anakana nthawi yomweyo. (Werengani Genesis 39:7-9.) Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Yosefe ankadziwa kale kuipa kotenga mkazi wamwini, mkazi wa Potifarayo asanayambe n’komwe kumunyengerera. Mofanana ndi zimenezi, inunso mungatsimikize mtima kuchita zoyenera musanakumane ndi mayesero enaake. Choncho mayeserowo akafika zidzakhala zosavuta kuti mungotsatira zimene munasankha kale.
Muzikana mayesero mwachangu ngati mmene Yosefe anachitira (Onani ndime 17)
“PITIRIZANI KUDZIYESA”
18. Kodi n’chiyaninso chingakuthandizeni kuti mupambane pa nkhondo yolimbana ndi zilakolako zoipa? (2 Akorinto 13:5)
18 Kuti mupambane polimbana ndi zilakolako zoipa, muyenera ‘kupitiriza kudziyesa,’ kapena kuti kudzifufuza nthawi zonse kuti mudziwe mmene mukuchitira. (Werengani 2 Akorinto 13:5.) Nthawi ndi nthawi, muziona mmene mumaganizira komanso mmene mumachitira zinthu n’kusintha ngati pakufunika kutero. Mwachitsanzo, ngakhale pamene mwapambana mayesero enaake muzidzifunsa kuti, ‘Kodi panatenga nthawi yaitali bwanji kuti ndikane mayeserowa?’ Ngati mutaona kuti munachedwa kuchitapo kanthu, musadziimbe mlandu. M’malomwake, ganizirani zimene mungadzachite ulendo wina kuti mudzachite zinthu mwachangu. Mungadzifunse mafunso ngati awa: ‘Ndikayamba kuganizira zinthu zolakwika, kodi ndimazichotsa mwamsanga m’maganizo mwanga? Kodi zosangalatsa zimene ndimasankha zimachititsa kuti zizindivuta kukana mayesero? Kodi ndimasiya mwamsanga kuyang’ana zithunzi zoipa? Kodi ndimamvetsa kuti nthawi zonse mfundo za Yehova ndi zabwino, ngakhale kuti ndimafunika kukhala wodziletsa kuti ndikwanitse kuzitsatira?’—Sal. 101:3
19. Kodi kulephera kusankha mwanzeru pa nkhani zooneka ngati zazing’ono, kungatilepheretse bwanji kulimbana ndi zilakolako zoipa?
19 Muzipewa kudziikira kumbuyo kapena kudzikhululukira. Baibulo limati: “Mtima ndi wopusitsa kwambiri kuposa chinthu chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.” (Yer. 17:9) Yesu anati mumtima mumachokera “maganizo oipa.” (Mat. 15:19) Mwachitsanzo, munthu yemwe anasiya kuonera zolaula, pakapita nthawi akhoza kuyamba kuganiza kuti palibe vuto kuona zithunzi zina zomwe sizikuonetsa anthu amene ali maliseche koma zingachititse kuti akhale ndi chilakolako chogonana. Kapenanso angamaganize kuti, ‘Palibe vuto kuganizira zinthu zolakwika bola ngati sindikuzichita.’ Apa tingati mtima wa munthu ameneyu umakhala ‘ukukonzekera kuchita zimene thupi limalakalaka.’ (Aroma 13:14) Ndiye kodi mungatani kuti mupewe zimenezi? Muzikhala osamala kuti musamasankhe mopanda nzeru pa nkhani zing’onozing’ono zomwe zingadzachititse kuti musasankhe mwanzeru pa nkhani zikuluzikulu n’kuchita tchimo.b Muzipewanso “maganizo oipa” alionse omwe angachititse kuti muziona kuti palibe vuto kuchita khalidwe linalake loipa.
20. Kodi tikuyembekezera chiyani m’tsogolo, nanga n’chiyani chingatithandize panopa?
20 Monga mmene taonera munkhaniyi, Yehova amatipatsa mphamvu zotithandiza kulimbana ndi mayesero. Komanso chifukwa cha chifundo chake, watipatsa chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kutumikira Yehova popanda kulimbana ndi zilakolako zoipa. Pamene tikuyembekezera zimenezo, tiyenera kukhala otsimikiza kuti tisamadzione ngati tilibe mphamvu kapenanso kumataya mtima pamene tikulimbana ndi zilakolako zoipa. Yehova angadalitse khama lathu, ndipo tidzapambana.
NYIMBO NA. 122 Khalani Olimba Komanso Osasunthika
a TANTHAUZO LA MAWU ENA: M’Baibulo, mawu akuti “tchimo” amanena za makhalidwe monga kuba, chiwerewere kapena kupha. (Eks. 20:13-15; 1 Akor. 6:18) M’malemba ena, mawu akuti “tchimo” anganene za uchimo umene tinatengera pobadwa ngakhale kuti timakhala tisanachite choipa chilichonse.
b Onani kuti wachinyamata wotchulidwa pa Miyambo 7:7-23 anasankha mopanda nzeru pa zinthu zing’onozing’ono zomwe zinachititsa kuti asasankhe mwanzeru pa zinthu zazikulu, ndipo anachita chiwerewere.
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Kumanzere: Pamene ali kumalo omwera khofi, m’bale wachinyamata akuona amuna awiri akusonyezana chikondi. Kumanja: Mlongo akuona anthu awiri akusuta fodya.