Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 September tsamba 26-30
  • Yehova Anatithandiza ‘Kukula Paliponse Pomwe Tinkadzalidwa’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Anatithandiza ‘Kukula Paliponse Pomwe Tinkadzalidwa’
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Wandidalitsa Kuposa Mmene Ndinkaganizira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Yehova Wakhala ‘Akuwongola Njira Zanga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Yehova Ndiye Pothaŵirapo Panga ndi Mphamvu Yanga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Utumiki Wathu Ukasintha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 September tsamba 26-30
A Mats ndi Ann-Catrin aima pafupi ndi galimoto yawo m’dera lakumudzi.

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Anatithandiza ‘Kukula Paliponse Pomwe Tinkadzalidwa’

YOFOTOKOZEDWA NDI MATS NDI ANN-CATRIN KASSHOLM

MALANGIZO akuti “muzikula paliponse pomwe mwadzalidwa,” angaoneke ngati achilendo. Koma a Mats ndi a Ann-Catrin omwe kwawo ndi ku Sweden, anakhala “akudzalidwa” maulendo ambiri. Kodi zimenezi zinachitika bwanji, nanga malangizo amene analandira anawathandiza bwanji?

Banja la a Kassholm linalowa Sukulu ya Giliyadi mu 1979, ndipo pa zaka zapitazi iwo akhala “akudzalidwa,” kapena kuti kutumizidwa kukatumikira m’mayiko ena monga Iran, Mauritius, Myanmar, Tanzania, Uganda ndi Zaire. Iwo ali ku Giliyadi, M’bale Jack Redford yemwe anali mlangizi wawo anapereka malangizo omwe akhala akuwathandiza pa nthawi yonse imene akhala “akudzalidwa,” “kuzulidwa” ndi “kudzalidwanso” kambirimbiri. Tiyeni tiwalole kuti afotokoze okha zimene zinachitika.

A Mats, choyamba tiuzeni mmene munaphunzirira choonadi.

Mats: Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri, bambo anga ankakhala ku Poland ndipo anaona zachinyengo zambiri zomwe Tchalitchi cha Katolika chinkachita. Koma ankanena kuti, “Choonadi chiyenera kuti chilipo ndithu.” Patapita nthawi ndinatsimikizira kuti choonadi chilipodi. Ndinagula mabuku ambiri akale ndipo lina linali lachikuto chabuluu, la mutu wakuti Choonadi Chimene Chimatsogolera ku Moyo Wamuyaya. Mutuwu unandisangalatsa moti ndinaliwerenga usiku wonse. Pofika m’mawa ndinazindikira kuti ndapeza choonadi.

Kuyambira mu April 1972, ndinawerenga mabuku ambiri a Mboni za Yehova ndipo ndinapeza mayankho a mafunso amene ndinali nawo. Ndinamva ngati wamalonda wa m’fanizo la Yesu yemwe atapeza ngale, anagulitsa chilichonse kuti akagule ngaleyo. Inenso ndinasiya mapulani anga onse opita kuyunivesite kuti ndikachite maphunziro a udokotala. Ndinachita zimenezi n’cholinga choti ndikagule “ngale” yomwe ndi choonadi chomwe ndinapeza. (Mat. 13:​45, 46) Choncho ndinabatizidwa pa 10 December, 1972.

M’chaka chomwecho, makolo anga ndi mng’ono wanga anaphunzira choonadi ndipo anabatizidwa. Mu July 1973, ndinayamba utumiki wanthawi zonse. Ann-Catrin anali mmodzi wa apainiya akhama mumpingo wathu. Iye anali wokongola ndipo ankakonda Yehova. Tinayamba kukondana ndipo tinakwatirana mu 1975. Pa zaka 4 zotsatira tinkakhala m’tauni yokongola ya Strömsund ku Sweden komwe anthu ake ankachita chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo.

Ann-Catrin: Bambo anga anaphunzira choonadi atatsala pang’ono kumaliza maphunziro awo a kuyunivesite ku Stockholm. Pa nthawiyi ndinali ndi miyezi itatu koma ankanditenga kumisonkhano ndiponso kolalikira. Mayi anga sankasangalala ndi zimenezi ndipo anayesetsa kuti apeze zimene a Mboni amalakwitsa, koma sanazipeze. Choncho patapita nthawi nawonso anabatizidwa. Ineyo ndinabatizidwa ndili ndi zaka 13 ndipo ndinayamba upainiya ndili ndi zaka 16. Ndinapita ku Umeå komwe kunkafunika olalikira ambiri kenako ndinadzakhala mpainiya wapadera.

Titakwatirana ndi a Mats, tinathandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi kuphatikizapo mtsikana wina dzina lake Maivor, yemwe anali katswiri wochita masewera enaake. Iye analolera kusiya kuchita masewerawo kuti azichita zambiri potumikira Yehova ndipo ankachita upainiya limodzi ndi mng’ono wanga. Iwo analowa Sukulu ya Giliyadi mu 1984 ndipo ndi amishonale ku Ecuador.

M’mayiko onse omwe mwakhala mukutumikira, kodi munkatsatira bwanji malangizo akuti “muzikula pamene mwadzalidwa”?

Mats: Utumiki wathu wakhala ukusinthasintha. Koma tinkayesetsa ‘kuzika mizu’ mwa Khristu pomutsanzira pa nkhani ya kudzichepetsa. (Akol. 2:​6, 7) Mwachitsanzo, m’malo moyembekezera kuti abale ndi alongo asinthe, tinkayesetsa kudziwa chifukwa chake amachita zinthu m’njira inayake. Tinkafunitsitsa kumvetsa kaganizidwe ndi chikhalidwe chawo. Pamene tinkayesetsa kutsanzira Yesu, tinkaona kuti ‘tadzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi,’ kuti tikule bwino kulikonse kumene atitumiza.—Sal. 1:​2, 3.

A Mats ndi Ann-Catrin anyamula chikwama ndi zakudya.

Tinkayenda kwambiri kuchezera mipingo

Ann-Catrin: Mtengo ukawokeredwa umafunikanso dzuwa kuti ukule bwino, ndipo Yehova anali ngati ‘dzuwa’ kwa ife. (Sal. 84:11) Iye anatipatsa abale ndi alongo achikondi. Mwachitsanzo, tili mumpingo wina waung’ono ku Tehran ku Iran, iwo ankatilandira bwino komanso kutipatsa zinthu. Izi zinkatikumbutsa mmene anthu ankalandirira alendo m’nthawi za m’Baibulo. Tikanakonda kukhalabe ku Iran, koma mu July 1980, boma linaletsa ntchito yathu m’dzikoli ndipo tinauzidwa kuti tichoke pasanathe maola 48. Choncho tinatumizidwa ku Zaire (panopa ndi ku Congo) ku Africa.

Nyumba zimene zili m’dera lakumudzi ku Zaire.

Zinthu zosangalatsa zomwe timakumbukira tikutumikira ku Zaire, mu 1982

Nditamva kuti tikutumizidwa ku Africa, ndinalira. Zomwe ndinamva zoti ku Africa kuli njoka komanso matenda zinandichititsa mantha. Koma anzathu ena omwe anatumikirako kwa nthawi yaitali anatiuza kuti: “Musachite mantha, simunapitepo ku Africa. Koma tikudziwa kuti mukapita mukasangalala.” Ndipo ankanenadi zoona. Abale ndi alongo kumeneko ndi ansangala ndiponso achikondi. Ndipo pambuyo pa zaka 6, ntchito yathu italetsedwa n’kuuzidwa kuti tichoke Zaire, ndinaseka chifukwa pa nthawiyo ndinali nditayamba kukukonda ndipo ndinkapempha Yehova kuti, “Chonde, tithandizeni tisachoke ku Africa.”

Ndi zinthu ziti zomwe mwasangalala nazo pa zaka zimenezi?

Ann-Catrin wakhala pampando pafupi ndi galimoto yawo.

“Chipinda” chathu ku Tanzania, mu 1988

Mats: Tinayamba kugwirizana ndi amishonale ochokera m’mayiko osiyanasiyana. M’mayiko ena tinkaphunzira ndi anthu ambiri moti munthu mmodzi ankatha kukhala ndi maphunziro 20. Abale a ku Africa ndi achikondi komanso amalandira bwino alendo moti sindidzaiwala. Tikamayendera mipingo ku Tanzania, anzathu ankatipatsa ‘zinthu zambiri,’ ngakhale kuti ankakhala ndi zochepa. Ankatibweretsera zinthu pa galimoto yathu yomwe tinkangoiimika pambali pa nyumba zawo. Galimotoyo inali ngati “chipinda” chathu. (2 Akor. 8:3) Nthawi ina yosangalatsa inkakhala pamene ine ndi Ann-Catrin tinkauzana zimene zachitika tsiku lililonse ndipo tinkathokoza Yehova chifukwa chokhala nafe.

Ann-Catrin: Kwa ine, chimene chimandisangalatsa ndi kudziwana ndi abale ndi alongo a m’mayiko osiyanasiyana. Tinaphunzira zikhalidwe zosiyanasiyana komanso zilankhulo monga Chifasi, Chifulenchi, Chiluganda ndi Chiswahili. Tinkaphunzira ndi anthu atsopano, kukhala ndi anzathu atsopano komanso kugwira ntchito mogwirizana potumikira Yehova.—Zef. 3:9.

Takhala tikuonanso zinthu zokongola zimene Yehova analenga. Utumiki wathu ukasintha, tinkangomva ngati tili pa ulendo woona malo ndipo Yehova ndi amene akutitsogolera. Tingati Yehova wationetsa zinthu zimene sitikanatha kuziona patokha.

Zithunzi: 1. A Mats ndi Ann-Catrin akulalikira kwa mayi ndi ana ake. 2. Ann-Catrin akulalikira kwa mnyamata wa Chimaasai.

Tinkalalikira m’madera osiyanasiyana ku Tanzania

Kodi mwakumana ndi mavuto otani, nanga n’chiyani chinakuthandizani kupirira?

Mats: Nthawi zina tinkadwala matenda osiyanasiyana kuphatikizapo malungo ndipo Ann-Catrin anachitidwa opaleshoni maulendo angapo. Tinkaderanso nkhawa makolo athu okalamba, koma timayamikira achibale omwe ankawasamalira. Iwo ankawasamalira mwachikondi komanso moleza mtima. (1 Tim. 5:4) Komabe nthawi zina tinkavutika ndi maganizo oona kuti tikanatha kuchita zambiri powathandiza m’malo mongowatumizira thandizo.

Ann-Catrin: Mu 1983, tikutumikira ku Zaire, ndinadwala kolera. Dokotala anauza a Mats kuti, “Muyesetse kuchoka nawo lero lomwe.” Tsiku lotsatira tinanyamuka kupita ku Sweden pa ndege yonyamula katundu chifukwa ndi yokhayo yomwe inalipo.

Mats: Tinkaona ngati utumiki wathu wathera pomwepo choncho tinalira kwambiri. Mosiyana ndi zimene dokotala uja ananena, Ann-Catrin anachira moti chaka chotsatira tinabwerera ku Zaire. Pa nthawiyi tinatumizidwa mumpingo wina waung’ono wa Chiswahili ku Lubumbashi.

Ann-Catrin: Tikutumikira ku Lubumbashi ndinakhala woyembekezera koma kenako ndinapita padera. Ngakhale kuti sitinkayembekezera kukhala ndi ana, zimenezi zinali zowawa kwambiri kwa ife. Koma pa nthawi yovuta kwambiriyi, Yehova anatipatsa mphatso ina imene sitinkaiyembekezera. Tinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri. Pasanathe chaka, ofalitsa anachoka pa 35 kufika pa 70 komanso osonkhana anachoka pa 40 kufika pa 220. Tinkatanganidwa mu utumiki ndipo Yehova anadalitsa khama lathu, zomwe zinachititsa kuti tizisangalala. Komabe nthawi ndi nthawi timaganizira komanso kukambirana zokhudza mwana wathu ndipo tikuyembekezera kudzaona mmene Yehova adzathetseretu chisoni chathu.

Mats: Pa nthawi ina, Ann-Catrin ankavutika ndi nkhawa ndipo ine anandipeza ndi khansa moti ndinkafunika kuchitidwa opaleshoni yaikulu. Panopa ndili bwino ndipo nayenso Ann-Catrin akuchita zomwe angathe potumikira Yehova.

Panopa tazindikira kuti si ife tokha amene tikukumana ndi mavuto. Pambuyo pa nkhondo yapachiweniweni ya mu 1994 ku Rwanda, tinapita kukayendera abale ndi alongo omwe anali ku malo osungirako anthu othawa nkhondo. Titaona chikhulupiriro, kupirira komanso mtima wawo wofuna kuthandiza ena, tinaona kuti Yehova amasamalira anthu ake pa mavuto alionse.—Sal. 55:22.

Ann-Catrin: Tinakumananso ndi vuto lina lalikulu mu 2007 tikuchokera kumwambo wopereka kwa Yehova ofesi ya nthambi ya ku Uganda. Tinkabwerera ku Nairobi, m’dziko la Kenya ndipo tinalipo amishonale ndi abale a pa Beteli pafupifupi 25. Tisanafike m’malire a dziko la Kenya, lole ina inadzaomba basi yathu. Dalaivala ndi anzathu ena 5 anafera pomwepo ndipo mlongo mmodzi anakamwalirira kuchipatala. Tikulakalaka kwambiri kudzaonananso ndi anzathuwa.—Yobu 14:​13-15.

Pang’ono ndi pang’ono mabala anga anayamba kupola. Koma ine ndi Mats ndi amodzi mwa anthu amene tinavutika kwambiri chifukwa cha ngoziyo. Ineyo ndinkavutika ndi nkhawa makamaka usiku. Ndinkalephera kugona moti ndinkamva zizindikiro ngati za mtima. Zinali zoopsa kwambiri. Koma kupemphera mochokera pansi pa mtima komanso kuwerenga mavesi ena amene tinkawakonda, kunatithandiza kumvako bwino. Tinalandiranso thandizo kwa madokotala odziwa bwino za matenda a nkhawa. Panopa sitikukhalanso ndi nkhawa kwambiri ndipo tikupitirizabe kupempha Yehova kuti azithandiza komanso kulimbikitsa anzathu omwe akuvutikabe ndi nkhawa.

Pofotokoza mmene munapiririra, munanena kuti Yehova anakunyamulani “ngati mazira.” Kodi mumatanthauza chiyani?

Mats: Pali mawu a Chiswahili omwe amati, “Tumebebwa kama mayai mabichi,” kapena kuti “Tinanyamulidwa ngati mazira.” Mofanana ndi mmene munthu amanyamulira mazira mosamala, Yehova wakhala akutithandiza mokoma mtima pa utumiki wathu uliwonse. Nthawi zonse sitinasowepo chilichonse. Yehova wakhalanso akutisonyeza chikondi ndi kutithandiza kudzera mwa abale a m’Bungwe Lolamulira omwe akhala akuchita nafe zinthu mokoma mtima.

Ann-Catrin: Ndikufuna kutchula chitsanzo chimodzi chosonyeza mmene Yehova wakhala akutithandizira. Tsiku lina ndinalandira foni yoti bambo anga akudwala ndipo ali m’chipatala ku Sweden. A Mats anali atangochira kumene malungo komanso tinalibe ndalama zogulira tikiti ya ndege. Choncho tinaganiza zoti tigulitse galimoto yathu. Kenako tinalandira mafoni awiri. Ina inali yochokera kwa banja lina lomwe litadziwa za vuto lathuli, linatigulira tikiti yopitira ku Sweden. Pomwe ina inali yochokera kwa mlongo wachikulire yemwe ankasunga ndalama m’kabokosi komwe anakalemba kuti “Kwa amene akufunika thandizo.” M’maminitsi ochepa, Yehova anatithandiza kuti ulendo wathu utheke.—Aheb. 13:6.

Kodi mwaphunzira chiyani pa zaka 50 zimene mwakhala mukuchita utumiki wanthawi zonse?

A Mats ndi Ann-Catrin aima limodzi ndipo akuoneka osangalala.

Panopa tikutumikira ku Myanmar

Ann-Catrin: Ndaphunzira kuti timakhala amphamvu ‘tikakhala odekha komanso tikamasonyeza kuti timadalira’ Yehova. Tikamamudalira iye amatimenyera nkhondo. (Yes. 30:15; 2 Mbiri 20:​15, 17) Chifukwa chotumikira modzipereka pa utumiki uliwonse, tapeza madalitso ambiri omwe sitikanawapeza kulikonse.

Mats: Mfundo yaikulu imene ndaphunzira ndi kudalira Yehova pa chilichonse n’kumaona mmene akundithandizira. (Sal. 37:5) Iye sanalepherepo kukwaniritsa malonjezo ake. Timaonabe izi pamene tikuchita utumiki wathu pa Beteli ku Myanmar.

Tikukhulupirira kuti Yehova adzadalitsanso achinyamata ambiri omwe akufuna kuchita zambiri pomutumikira. Sitikukayikira kuti zimenezi zidzatheka ngati iwo atalola kuti Yehova awathandize kukula pamalo alionse omwe adzalidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena