Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w25 October tsamba 30-31
  • Abale Awiri Atsopano a M’Bungwe Lolamulira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Abale Awiri Atsopano a M’Bungwe Lolamulira
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Nkhani Yofanana
  • Abale Awiri Atsopano M’Bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Bungwe Lolamulira ndi Chiyani?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Mamembala Atsopano a Bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25 October tsamba 30-31

Abale Awiri Atsopano a M’Bungwe Lolamulira

PAMSONKHANO wapachaka umene unachitika pa 5 October 2024, panaperekedwa chilengezo chapadera chakuti M’bale Jody Jedele ndi M’bale Jacob Rumph, aikidwa kuti azitumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Abale awiriwa atumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri.

Jody Jedele ndi mkazi wake, Damaris

M’bale Jedele anabadwira mumzinda wa Missouri, ku U.S.A. ndipo analeredwa m’banja la Mboni. Banja lawo linkakhala kufupi ndi dera limene kunali a Mboni ochepa. Izi zinachititsa kuti azikumana ndi abale ndi alongo ochokera m’madera osiyanasiyana a m’dzikoli amene ankabwera kudzalalikira uthenga wabwino m’derali. Iye ankalimbikitsidwa kwambiri akaona chikondi komanso mgwirizano wawo moti anabatizidwa pa 15 October 1983, ali ndi zaka zapakati pa 13 ndi 14. Iye ankasangalala kwambiri ndi ntchito yolalikira moti atamaliza maphunziro akusekondale, anayamba upainiya wokhazikika mu September 1989.

M’bale Jedele ali mnyamata, makolo ake ankakonda kumutenga limodzi ndi mchemwali wake, kukaona malo ku Beteli. Zimenezi zinachititsa kuti akhale ndi cholinga chodzatumikira pa Beteli ndipo zinatheka. M’bale Jedele anayamba kutumikira kubeteli ya ku Wallkill mu September 1990. Poyamba ankatumikira mu Dipatimenti Yoyeretsa ndipo kenako anadzayamba kutumikira mu Dipatimenti ya Zachipatala.

Pa nthawiyo, mipingo yapafupi ya Chisipanishi inkakula ndipo kunkafunika abale oti azikathandiza. Ndiyeno M’bale Jedele anayamba kusonkhana mumpingo wa Chisipanishi n’kuyamba kuphunzira chilankhulochi. Pasanapite nthawi, M’bale Jedele anakumana ndi Mlongo Damaris yemwe ankachita upainiya m’derali. Kenako anakwatirana ndipo mlongoyu nayenso anayamba kutumikira pa Beteli.

Mu 2005, anachoka pa Beteli kuti azikasamalira makolo awo omwe ankatumikira Yehova mokhulupirika. Pa nthawiyi, M’bale ndi Mlongo Jedele ankachita upainiya wokhazikika. M’bale Jedele ankatumikira monga mlangizi wa Sukulu ya Utumiki wa Upainiya. Ankatumikiranso m’Komiti Yolankhulana ndi Achipatala komanso m’Komiti ya Zomangamanga.

Mu 2013, M’bale ndi Mlongo Jedele anaitanidwanso ku Beteli ya ku Warwick kuti azikagwira ntchito ya zomangamanga. Kuchokera nthawi imeneyo atumikiraponso ku Patterson ndi ku Wallkill. M’bale Jedele anatumikirapo mu Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga komanso mu Dipatimenti Yoyang’anira Zachipatala. Mu March 2023, M’bale Jedele anaikidwa kukhala wothandiza m’Komiti ya Utumiki. Poganizira za ma utumiki amene wachita, iye ananena kuti: “Ukalandira utumiki watsopano, umaona ngati sungaukwanitse. Koma pamenepo m’pamene umafunika kudalira kwambiri Yehova chifukwa ndi iyeyo amene amatithandiza kuti tikwanitse utumiki uliwonse umene watipatsa.”

Jacob Rumph ndi mkazi wake, Inga

M’bale Rumph anabadwira mumzinda wa California, ku U.S.A. Ali mwana, mayi awo anafooka mwauzimu koma ankayesetsa kuphunzitsa m’baleyu choonadi cha m’Baibulo. Komanso chaka ndi chaka, ankapita kukacheza ndi agogo awo aakazi omwe anali Mboni yokhulupirika. Iwo anathandiza kwambiri m’baleyu kuti azikonda choonadi ndipo atafika zaka 13 anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Pasanapite nthawi yaitali, pa 27 September 1992 anabatizidwa. Zinali zosangalatsa kuona kuti mayi ake anayambiranso kulalikira komanso kusonkhana mokhazikika. Bambo akenso ndi achibale ena, anayamba kupita patsogolo n’kubatizidwa.

Ali wachinyamata, M’bale Rumph ankaona mmene apainiya ankasangalalira. Ndiye atamaliza maphunziro akusekondale, anayamba upainiya mu September 1995. Mu 2000, anasamukira ku Ecuador komwe kunkafunikira olalikira ambiri. Kumeneko anakumana ndi Mlongo Inga wa ku Canada yemwe anali mpainiya ndipo kenako anakwatirana. Pambuyo pake anayamba kutumikira mtauni ina ya ku Ecuador komwe kunali kagulu kochepa ka ofalitsa. Panopa kaguluka kanakula n’kukhala mpingo wamphamvu.

Patapita nthawi, banjali linaikidwa kukhala apainiya apadera ndipo kenako linayamba utumiki woyang’anira dera. Mu 2011 analowa kalasi nambala 132 ya sukulu ya Giliyadi. Atamaliza maphunzirowa, anatumikira m’mayiko ambiri komanso anachita ma utumiki osiyanasiyana monga kutumikira pa Beteli, umishonale komanso ntchito yoyang’anira dera. M’bale Rumph anatumikiraponso monga mlangizi wa Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.

Chifukwa cha mliri wa COVID-19, M’bale ndi Mlongo Rumph anabwerera ku United States. Iwo anaitanidwa kuti azikatumikira ku Beteli ya ku Wallkill ndipo M’bale Rumph anaphunzitsidwa ntchito m’Dipatimenti ya Utumiki. Patapita nthawi, anatumizidwanso ku nthambi ya Ecuador, komwe M’bale Rumph amatumikira m’Komiti ya Nthambi. Mu 2023, anatumizidwa ku Warwick. Mu January 2024, M’bale Rumph anayamba kutumikira monga wothandiza m’Komiti ya Utumiki. Poganizira za mayiko amene wakhala akutumikira, iye ananena kuti: “Chimene chimachititsa kuti utumiki ukhale wapadera, si malo amene ukutumikirako, koma anthu amene ukutumikira nawo limodzi.”

Timayamikira khama la abale amenewa ndipo ‘timawalemekezeka kwambiri.’—Afi 2:29.

Panopa m’Bungwe Lolamulira muli abale odzozedwa okwana 11: Kenneth Cook, Jr.; Gage Fleegle; Samuel Herd; Geoffrey Jackson; Jody Jedele; Stephen Lett; Gerrit Lösch; Jacob Rumph, Mark Sanderson; David Splane ndi Jeffrey Winder.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena