MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muzitsatira Ndandanda Yanu Yowerengera Baibulo Tsiku Lililonse
Kodi zimakuvutani kutsatira ndandanda yanu yowerengera Baibulo tsiku ndi tsiku chifukwa chakuti mumakhala otanganidwa? (Yos. 1:8) Ngati ndi choncho, yesani kuchita chimodzi mwa zinthu zotsatirazi:
Muzitchera alamu. Mungatchere alamu pafoni yanu kapena pachipangizo chinachake kuti izikukumbutsani kuwerenga Baibulo.
Muziika Baibulo lanu pamalo oonekera. Ngati mumagwiritsa ntchito Baibulo lochita kupulinta, muziliika pamalo oti muzitha kuliona tsiku lililonse.—Deut. 11:18.
Muzimvetsera Baibulo lochita kujambulidwa. Mukhoza kumamvetsera Baibulo pa nthawi imene mukugwira ntchito zanu za tsiku ndi tsiku. Tara yemwe ndi mpainiya, ali ndi ana komanso amagwira ntchito usiku ananena kuti, “Kumvetsera Baibulo lochita kujambulidwa uku ndikugwira ntchito zapakhomo, kumandithandiza kutsatira ndandanda yanga yowerengera Baibulo tsiku ndi tsiku.”
Musamagwe ulesi. Ngati pachitika zadzidzidzi ndipo mwalephera kuwerenga Baibulo pa nthawi imene mumawerenga, muziwerengabe mavesi ochepa musanagone. Mukhoza kupindulabe ngakhale mutangowerenga mavesi ochepa okha patsiku.—1 Pet. 2:2.