Zimene Zachitika M’chaka Chapitachi
N’zoonekeratu kuti mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova ikupita patsogolo. Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zosangalatsa zomwe zachitika m’miyezi yapitayi.
Kugulitsa Malo N’kugula Atsopano
Malo Atsopano Oti Amangepo Likulu Lathu
Mu July 2009, a Mboni za Yehova anagula malo m’chigawo cha New York, m’dziko la United States. Iwo anagula malowa n’cholinga choti asamutsireko likulu lawo. Malowa ndi okwana maekala 253 ndipo ali pa mtunda wa makilomita 80 kumpoto cha kumadzulo kwa malo awo a ku Brooklyn, m’chigawo cha New York, omwe akhala akugwiritsa ntchito kuyambira mu 1909.
Malo atsopanowa akadzamangidwa, kuzidzakhala atumiki a pa Betheli okwana 800. Pamalowa adzamangapo maofesi ndi nyumba zina zogwiriramo ntchito komanso nyumba zinayi zogona. Akukonzanso zoti kudzakhale malo aang’ono osungirako zinthu zakale zosonyeza mbiri ya Mboni za Yehova.
Nyumba zonsezi zidzafuna malo okwana maekala 45, ndipo malo ena otsalawo adzangowasiya choncho. Sadzakhala ndi malo aakulu odzala kapinga koma adzangosiya mitengo yambiri yachilengedwe imene ili pamalowo. Akatswiri a zomangamanga akonza pulani yoti nyumbazo zisamadzawononge magetsi ambiri. Zimenezi zidzathandiza kuteteza chilengedwe komanso kuti asamadzawononge ndalama zambiri. Mwachitsanzo, padenga la nyumbazi adzadzalapo zomera zosavuta kusamalira. Zomerazi zidzathandiza kuti madzi a mvula asamadzawononge zinthu komanso kuti m’nyumbazi musamadzatenthe kapena kuzizira kwambiri. Maofesi azidzagwiritsa ntchito kwambiri kuwala kochokera kunja, komanso akukonza zoti asamadzawononge madzi ambiri pamalowa.
N’chifukwa chiyani aganiza zosamukira kumeneko? Chifukwa choyamba n’chakuti maofesi ena a nthambi a m’mayiko ena akugwiranso ntchito yosindikiza mabaibulo ndiponso mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo. M’mbuyomu ntchitoyi inkachitika ku Brooklyn kokha. Koma mu 2004, ntchito yosindikiza komanso kutumiza mabuku m’dziko la United States anaisamutsira ku Wallkill, mumzinda wa New York, womwe uli pa mtunda wa makilomita pafupifupi 145 kumpoto cha kumadzulo kwa Brooklyn. Chifukwa china n’choti anaganizira za ndalama zimene zimawonongeka posamalira ndi kukonzanso nyumba zakale zimene zili m’malo osiyanasiyana ku Brooklyn. Kusamukira kumalo amene nyumba zonse zikakhale pamodzi kuthandiza kuti ndalama zimene abale amapereka zigwiritsidwe ntchito mosamala.
Maofesi Ena Anthambi Anaphatikizidwa
Pofika m’mwezi wa September 2012, ntchito zimene maofesi a Mboni za Yehova oposa 20 ankagwira, anazipereka m’manja mwa nthambi zikuluzikulu. Pali zifukwa zikuluzikulu ziwiri zomwe zinachititsa zimenezi:
1. Zipangizo zamakono zathandiza kuti ntchito yambiri izigwiridwa ndi anthu ochepa. M’zaka zaposachedwapa njira zotumizira mauthenga komanso kusindikiza mabuku zapita patsogolo kwambiri. Zimenezi zachititsa kuti tichepetse chiwerengero cha anthu ogwira ntchitozi m’nthambi zikuluzikulu. Popeza kuti tsopano pali anthu ochepa amene akutumikira m’nthambi zikuluzikulu, n’zotheka kusamutsa anthu ena m’nthambi zing’onozing’ono za m’mayiko ena kuti azikatumikira m’nthambi zikuluzikuluzo.
Zimenezi zachititsa kuti abale ndi alongo odziwa bwino ntchito zawo, ochokera m’madera osiyanasiyana, azigwirira limodzi ntchito yothandiza pophunzitsa Baibulo. Mwachitsanzo, tsopano nthambi ya ku Mexico ndi imene ikuyang’anira ntchito yolalikira ku Costa Rica, ku El Salvador, ku Guatemala, ku Honduras, ku Nicaragua ndi ku Panama. Zimenezi zachititsa kuti maofesi a nthambi m’mayiko 6 amenewa atsekedwe. Anthu okwana 40 amene ankatumikira pa Beteli m’mayiko amenewa anawatumiza ku nthambi ya ku Mexico. Ena pafupifupi 95 anatsala m’mayiko awo omwewo, ndipo anayamba utumiki wa nthawi zonse.
Abale ndi alongo enanso anatsala m’mayiko amenewo ndipo akupitiriza kugwira ntchito yomasulira mabuku koma moyang’aniridwa ndi nthambi ya ku Mexico. Mwachitsanzo, ku Panama kuli abale ndi alongo pafupifupi 20 amene akumasulira mabuku m’zinenero zakwawoko. Ku Guatemala kuli abale ndi alongo okwana 16 amene akumasulira mabuku m’zinenero 4 zakwawoko. Ntchito yophatikiza maofesi a nthambi ku Central America, yachepetsa chiwerengero cha anthu ogwira ntchito pa Beteli, kuchoka pa 300 kufika pa 75.
2. Zathandiza kuti atumiki ambiri a nthawi zonse azigwira ntchito yolalikira. Kuphatikiza maofesi a nthambi kumeneku kwachititsa kuti abale ndi alongo amene ankatumikira m’nthambi zing’onozing’ono aike maganizo awo onse pa ntchito yolalikira uthenga wabwino. M’bale wina wa ku Africa, amene anatumizidwa kuti azikagwira ntchito yolalikira, analemba kuti: “Kwa miyezi ingapo yoyambirira, zinali zovuta kusintha zina ndi zina kuti moyo wanga ugwirizane ndi utumiki watsopanowo. Koma kulowa mu utumiki tsiku lililonse kwandipangitsa kukhala wosangalala ndipo ndapeza madalitso osaneneka. Panopa ndikuphunzira Baibulo ndi anthu okwana 20, ndipo ena mwa iwo amafika pa misonkhano ya mpingo.”
Wotchi Imene Yakhala ku Brooklyn kwa Nthawi Yaitali
Kwa zaka zoposa 40 usana ndi usiku, anthu a ku New York City, akhala akuona zilembo zofiira zotalika mamita 4.6 zimene anaziika pamwamba ku likulu la Mboni za Yehova. Zilembo zimenezi n’zothandiza kwambiri kwa anthu a mumzindawu chifukwa zimawathandiza kudziwa nthawi komanso mmene kunja kwachera.
Zilembozi zinaikidwa zaka zoposa 70 zapitazo ndi amene anali mwini wake wa malowo. Koma a Mboni za Yehova atagula nyumbayi mu 1969, anasintha zilembozi kuti zizioneka mmene zikuonekera panopa.
Abale akuika zilembo za chikwangwani cha mawu akuti “Watchtower” mu 1970
Zilembo zimenezi akhala akuzisintha maulendo angapo pofuna kuti zikhale zothandiza kwa anthu ambiri. Mwachitsanzo, chapakati pa zaka za m’ma 1980, anakonza zilembozo kuti zizionetsa mmene kunja kwachera m’ma digiri Seshasi, chifukwa poyamba zinkangoonetsa nthawi ndi mmene kunja kwachera m’ma digiri Farenihaeti.
Eboni, amene amaona zilembozi ali m’nyumba mwake ku Brooklyn, anati: “Zimasangalatsa kusuzumira pawindo kuti ndione nthawi ndi mmene kunja kwachera ndisanapite kuntchito. Zimandithandiza kuti ndisamachedwe kuntchito komanso kuti ndizivala mogwirizana ndi mmene kunja kwachera.”
Kodi zilembozi zipitirirabe kukhala pamenepo kwa zaka zina 40? Popeza kuti a Mboni za Yehova akusamuka pa malo amenewa, zidzadalira amene adzagule malowo.
Kulalikira Uthenga Wabwino
Ku Manhattan Kukuchitika Zatsopano
Mu November 2011, gulu la anthu a Mboni za Yehova linayamba kuuza anthu a ku Manhattan uthenga wa m’Baibulo poika magazini ndi mabuku pa matebulo ndi m’timashelefu tamateyala. Ntchito imeneyi ikuchitikira kum’mwera kwa tauni ya Manhattan, yomwe ndi yakale kwambiri ku New York City. Abale anagawa tauni ya Manhattan m’zigawo zinayi. Chigawo chilichonse chili ndi malo osiyanasiyana pomwe anthu odutsa amatha kupeza tebulo loyalidwa bwino kapena kashelefu pomwe amaikapo mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Anthu odutsawo amatha kuima m’malowa ndipo apainiya amakambirana nawo n’kuwagawira mabuku amene akufuna. Matebulo amenewa amapezeka kwambiri m’malo okwerera mathiransipoti kumene kumadutsa anthu ambiri tsiku lililonse.
Banja lina limene likuchita upainiya likugawira magazini amene awaika patebulo ku Grand Central Station ku New York City
M’malo amenewa anthu amapeza mayankho a mafunso ambiri a m’Baibulo. Anthu amene akufulumira kwambiri amangotenga buku kapena magazini kuti akawerenge nthawi ina. Abalewo amakhala ndi mabuku a zinenero zosiyanasiyana. Koma ngati palibe mabuku a m’chinenero chimene munthu akufuna, angathe kuitanitsa ndipo munthuyo amadzatenga pakapita masiku angapo.
Anthu ambiri, kuphatikizapo akuluakulu ena a m’boma, akusangalala ndi zimenezi. Mwachitsanzo, wapolisi wina anati: “Mumachedwa kuti anthu inu? Muli ndi zinthu zofunika kwambiri kwa anthu.” Bambo wina anaima mwadzidzidzi ataona buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Iye ananena kuti anaona anthu akuwerenga bukuli kumalo okwerera sitima ndipo sankadziwa kuti anthuwo alitenga kuti. Apa tsopano anadziwa kumene analitenga.
Mnyamata wina ankadutsa tebulo lina la mabuku tsiku lililonse kwa milungu 6 akamapita kuntchito. Tsiku lina anaima n’kunena kuti, “Ndikufuna mundithandize.” Abale ndi alongo amene anali patebulopo anasangalala kumuthandiza. Iwo anam’patsa Baibulo ndi kumusonyeza mmene angaliphunzirire. Anthu achidwi omwe amadutsa m’malowa amaima n’kumakambirana ndi abalewo nkhani za m’Baibulo, ndipo pa miyezi 8 yokha, anthu 1,748 anasonyeza kuti akufuna kuphunzira Baibulo. Pofika m’mwezi wa June 2012, ntchito imeneyi yathandiza kuti anthu alandire magazini 27,934 ndi mabuku 61,019.
Magazini Athu Ayamba Kukhala ndi Masamba Ochepa Ndipo Azipezeka M’zinenero Zambiri
Kuyambira mu January 2013, magazini a Galamukani! komanso Nsanja ya Olonda imene timagawira anthu mu utumiki, anayamba kukhala ndi masamba 16 m’malo mwa masamba 32. Popeza kuti magaziniwa azikhala ndi nkhani zochepa, zichititsa kuti amasuliridwe m’zinenero zambiri. Panopa Galamukani! ikumasuliridwa m’zinenero 98 ndipo Nsanja ya Olonda ikumasuliridwa m’zinenero 204. Magazini yophunzirira ya Nsanja ya Olonda ipitiriza kukhala ndi masamba 32.
Nkhani zina zimene kale zinkapezeka m’magaziniwa tsopano zizipezeka pa Webusaiti ya www.pr2711.com pokha. Zina mwa nkhani zimenezi ndi monga yakuti “Zoti Achinyamata Achite,” “Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo” komanso lipoti la mwambo womaliza maphunziro ku sukulu ya Giliyadi zimene zinkapezeka mu Nsanja ya Olonda imene timagawira mu utumiki. Nkhani zinanso zimene zizipezeka pa Webusaiti pokha ndi yakuti “Zoti Banja Likambirane” komanso yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” zimene zinkapezeka m’magazini a Galamukani!
Kuwonjezera pamenepa, pali nkhani zinanso zimene zizipezeka pa Webusaiti pokha, zomwe zikuyankha mafunso okhudza Baibulo ndi Mboni za Yehova momveka bwino komanso mosapita m’mbali. Mabuku ndi magazini amene tinasindikiza akupezekanso pa Webusaiti yathu ndipo munthu akhoza kuwakopera. Munthu amene ali ndi kompyuta kapena foni ya Intaneti angathe kuwerenga mabuku athu mosavuta pa Webusaiti yathu ya www.pr2711.com m’zinenero zoposa 440.
Webusaiti Yathu Yakonzedwanso Ndipo Ikuoneka Bwino
Kwa miyezi ingapo yapitayi, gulu lalikulu la Mboni za Yehova ku likulu lathu ku New York lakhala likugwira ntchito mwakhama pokonza Webusaiti yathu ya www.pr2711.com kuti izioneka bwino komanso kuti ikhale yosavuta kugwiritsa ntchito pa kompyuta, pafoni kapena pa chipangizo chilichonse. Kuwonjezera pamenepo, akonza Webusaitiyi ndi zolinga ziwiri:
1. Kuphatikiza Mawebusaiti atatu kuti ikhale imodzi. Mawebusaiti atatu a Mboni za Yehova aphatikizidwa n’kupanga Webusaiti imodzi yovomerezeka ya www.pr2711.com. Izi zikutanthauza kuti Mawebusaiti anthu awiri, ya www.watchtower.org ndi ya www.jw-media.org, anasiya kugwira ntchito. Kuphatikiza Mawebusaitiwa pamodzi kwathandiza kuti munthu azipeza zonse zimene akufuna zokhudza Mboni za Yehova pamalo amodzi. Mwachitsanzo, mungathe kuwerenga, kumvetsera kapena kusindikiza Baibulo ndi mabuku athu m’zinenero zambiri.
Webusaiti yathu ya www.pr2711.com yokonzedwanso, inayamba kugwira ntchito pa August 28, 2012
2. Kuti awonjezeremo zinthu zina. Pa Webusaiti imene yakonzedwayi pali mayankho a mafunso a m’Baibulo komanso pali nkhani zokhudza ntchito yolalikira, maofesi a nthambi, Nyumba za Ufumu ndi misonkhano ikuluikulu ya Mboni za Yehova. Palinso nkhani zokhudza zimene zikuchitikira abale athu padziko lonse. Komanso pali zina zosangalatsa zimene mabanja, achinyamata ndiponso ana angathe kuzigwiritsa ntchito.
Tsiku lililonse, anthu masauzande ambiri amawerenga mabuku athu pa Intaneti. Iwo amakopera zinthu zomvetsera, ma EPUB, ma PDF kapena mavidiyo a chinenero chamanja, pafupifupi hafu miliyoni. Tsiku lililonse, anthu 100 amapempha kuti akufuna munthu woti aziphunzira nawo Baibulo.
Kuthandiza Anthu a Mitundu Yonse
Baibulo Lalitali la Zilembo za Anthu Akhungu
Baibulo lonse la Dziko Latsopano la zilembo za anthu akhungu likupezeka m’Chingelezi, m’Chisipanishi ndi m’Chitaliyana ndipo lili m’mavoliyumu 20 mpaka 28. Mavoliyumu onsewa amakwana pashelefu yaitali mamita awiri. Koma anthu akhunguwo akamagwiritsa ntchito zipangizo zamakono, samafuna malo ambiri poyerekezera ndi mabaibulo a zilembo za anthu akhungu ochita kusindikiza. Mwachitsanzo, pali chipangizo china chamakono chimene anthu akhungu amagwiritsa ntchito polemba manotsi kapena kuwerenga nkhani zina. Chipangizo chimenechi sichifuna malo ambiri ngati Baibulo losindikiza la zilembo za anthu akhungu. Anthu akhungu angathenso kumvetsera nkhani za m’mabuku ndi m’magazini pogwiritsa ntchito pulogalamu ya pakompyuta imene imawerenga mabukuwo.
Kwa zaka zoposa 100, a Mboni akhala akufalitsa mabuku ndi magazini ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zilembo za anthu akhungu, ndipo panopa mabuku amenewa akupezeka m’zinenero 19. Ngakhale kuti anthu akhungu achidwi angathe kupeza mabukuwa popanda mtengo, ambiri amapereka chopereka mwa kufuna kwawo.
M’bale Anthony Bernard wa ku Sri Lanka akuchititsa kulambira kwa pabanja pogwiritsa ntchito Baibulo lachingelezi la zilembo za anthu akhungu
A Mboni apanga mapulogalamu a pakompyuta amene amasintha nkhani kuti ikhale m’zilembo za anthu akhungu m’zinenero zosiyanasiyana. Pulogalamuyi imakopera nkhaniyo n’kuimasulira kuti ikhale m’zilembo za anthu akhungu. Kenako imakonzanso bwinobwino zilembo za anthu akhunguzo kuti zikhale zosavuta kuwerenga. Pulogalamu imeneyi imathandiza popanga mabuku a zilembo za anthu akhungu, kuphatikizapo Baibulo, m’chinenero chilichonse chimene chili ndi zilembo za anthu akhungu.
M’mbuyomu, buku latsopano likatulutsidwa pa msonkhano wachigawo, ankalengeza kuti mtsogolo abale adzatha kuitanitsa buku la chinenero cha anthu akhungu. Koma chaka chatha, abale ku ofesi ya ku United States anafufuza m’mipingo kuti adziwe msonkhano umene anthu akhungu akapezekeko. Ankafunanso kudziwa kuti anthuwo amakonda kuwerenga zofalitsa za mtundu uti, pakati pa mabuku osindikizidwa ndi zilembo za anthu akhungu, kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono za anthu akhungu kapena pulogalamu ya pakompyuta imene imawerenga mabuku.
Atatero anatumiza mabuku a zilembo za anthu akhungu m’malo amisonkhano kumene kunali anthu akhungu. Zimenezi zinachititsa kuti anthu akhunguwo alandire mabuku atsopano pa nthawi yofanana ndi anthu ena onse. Anthu amene ankafuna kuti aziwerenga mabukuwo pa zipangizo zamakono, anawatumizira patapita mlungu umodzi chichitikireni msonkhanowo.
Mlongo wina wosaona ananena kuti: “Zinali zosangalatsa kwambiri kulandira mabuku atsopano pa nthawi imodzi ndi ena onse. Lemba la Salimo 37:4 limatiuza kuti Yehova adzatipatsa zokhumba za mtima wathu. Iye wachitadi zimenezi mlungu uno.” M’bale wina wosaona anangoyamba kulira, kenako anati, “Tikuthokoza Yehova chifukwa chotisamalira bwino kwambiri.”
Anthu Ambiri Aphunzira Kuwerenga ndi Kulemba
Mu 2011, Mboni za Yehova zinathandiza anthu 5,700 kudziwa kuwerenga ndi kulemba. Tiyeni tione zimene zakhala zikuchitika m’mayiko ena:
Ghana: Zaka 25 zapitazi, tathandiza anthu oposa 9,000 kuphunzira kuwerenga ndi kulemba.
Akuphunzira kuwerenga ndi kulemba ku Zambia
Mozambique: Anthu oposa 19,000 aphunzira kuwerenga m’zaka zoposa 15 zapitazi. Mlongo wina amene anaphunzira kuwerenga, dzina lake Felizarda, ananena kuti: “Ndikusangalala kwambiri chifukwa panopa ndimatha kuwerengera ena Baibulo. Poyamba sindinkatha kuchita zimenezi.”
Solomon Islands: Ofesi ya nthambi inalemba kuti: “M’mbuyomu, anthu ambiri akumidzi analibe mwayi wopita ku sukulu. Komanso atsikana ambiri sanapite patali ndi sukulu. Choncho sukulu imeneyi yathandiza kwambiri anthu kuphunzira kuwerenga ndi kulemba, makamaka azimayi. Anthu ambiri akadziwa kuwerenga ndi kulemba amachita zinthu molimba mtima.”
Zambia: Kuyambira mu 2002, anthu pafupifupi 12,000 aphunzira kuwerenga ndi kulemba mwaluso. Mwachitsanzo, mlongo wina wa zaka 82, dzina lake Agnes, ananena kuti: “Kumpingo atalengeza kuti kukuyambika kalasi yophunzitsa kuwerenga ndi kulemba, ndinasangalala kwambiri ndipo ndinalembetsa. Tsiku loyamba kuphunzira lenilenilo, ndinaphunzira kulemba dzina langa.”
Nyimbo Zotamanda Mulungu Zikupezeka M’zinenero Zosiyanasiyana
Panopa a Mboni za Yehova akumasulira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo m’zinenero 600. Koma kumasulira buku la nyimbo zokwana 135 si ntchito yamasewera. Komabe, m’zaka zitatu zokha buku lonse la nyimbo, lakuti Imbirani Yehova, linamasuliridwa m’zinenero 116. Kuwonjezera pamenepo, pali zinenero zinanso 55 zomwe zili ndi mabuku a nyimbo 55, ndipo panopa abale akumasulira bukuli m’zinenero zina zambirimbiri.
Solomon Islands: Abale ndi alongo akuimba m’Chingelezi cha Chipijini
Amene amamasulira nyimbo amakhala n’cholinga chotulutsa nyimbo zatanthauzo, zosangalatsa ndiponso zosavuta kukumbukira. Komanso amafuna kuti mawu a m’nyimbo zotamanda Mulungu akhale osavuta kuti woimba azitha kumvetsa tanthauzo lake ndi zimene chiganizo chilichonse chikunena. M’chinenero chilichonse, mawu a nyimbo ayenera kugwirizana bwino ndi kamvekedwe ka zipangizo za m’nyimboyo kuti azimveka ngati kuti mawuwo ndi a munthu amene anaimba zipangizozo.
Kodi omasulira amatha bwanji kuchita zimenezi? Iwo samangomasulira liwu ndi liwu potsatira mawu a m’nyimbo ya Chingelezi, koma amalemba mawu awoawo amene akufotokoza mfundo zofunika za m’nyimbo ya Chingelezi ija. Ngakhale kuti omasulirawo amayesetsa kutulutsa mfundo za m’Malemba m’nyimbo iliyonse, iwo amagwiritsa ntchito mawu amene anthu akhoza kuwamva komanso kuwakumbukira mosavuta.
Pogwira ntchito imeneyi, choyamba iwo amamasulira ndendende ziganizo za nyimbo ya Chingelezi. Kenako, m’bale amene amadziwa bwino kalembedwe ka nyimbo amakonza ziganizo za chinenero chakecho kuti zikhale nyimbo yosangalatsa komanso yatanthauzo. Ikachoka kwa m’bale ameneyu, abale amene anamasulira nyimboyo pamodzi ndi anthu ena amaonetsetsa kuti ikugwirizanadi ndi mfundo za m’Malemba komanso kuti palibe zolakwika zina. Ngakhale kuti ntchito yomasulira buku la nyimbo ndi yaikulu kwabasi, Mboni za Yehova padziko lonse zikusangalala kuimba nyimbo zotamanda Mulungu m’zinenero zawo.
Maofesi a Omasulira Mabuku Akusamutsidwa
Buku la Chivumbulutso linalosera kuti odzozedwa m’nthawi yathu ino adzaitana anthu kuti abwere kuti adzamwe “madzi a moyo kwaulere.” (Chiv. 22:17) Amene akuitanidwawo ndi anthu a “mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chiv. 7:9) M’mbuyo monsemu abale ndi alongo omasulira mabuku ankagwirira ntchito yawo pa ofesi yawo ya nthambi, ngakhale kuti chinenero chawo chimalankhulidwa m’madera ena akutali. Zinali zovuta kwambiri kuti omasulirawa azimva mmene anthu a chinenero chawo akulankhulira, ndiyeno n’kumasulira mabukuwo mowafika pamtima. Koma pano omasulira ambiri akusamukira kumadera amene chinenero chawocho chimalankhulidwa. Zimenezi zathandiza kwambiri m’njira zosiyanasiyana monga mmene ndemanga zotsatirazi za omasulira zikusonyezera.
Mlongo wina womasulira m’chinenero cha Chimaya ku Mexico atasamukira kudera limene chinenero chawo chimalankhulidwa, anati: “Ndinkangomva ngati kamtengo kamene kawokedwanso pamene kanali poyamba.” M’bale wina womasulira kum’mwera kwa Russia anati: “Ofesi ya omasulira ikakhala m’dera limene anthu amalankhula chinenerocho, zimakhala ngati omasulirawo ali m’paradaiso. Mmene chinenero chimagwiritsidwira ntchito pa TV, m’mabuku ndi pa Intaneti zimasiyana kwambiri ndi mmene anthu amalankhulira tsiku ndi tsiku. Kwa ife, kumva anthu akulankhula, n’zimene zimatithandiza kuti tizimasulira mmene anthuwo amalankhulira.”
“Ndinkangomva ngati kamtengo kamene kawokedwanso pamene kanali poyamba.”
M’bale winanso amene amamasulira Chishiluba ku Congo ananena kuti: “Timalankhula chinenero chathu tsiku lililonse pa chilichonse chimene tikuchita monga tikapita kokagula zinthu, tikamacheza ndi aneba, polalikira ndiponso tikapita ku misonkhano yachikhristu. Timaphunzira zimene tinamasulirazo, ndipo timagwiritsa ntchito mabuku a Chishiluba mu utumiki. Choncho timatha kuona ngati anthu akumva bwinobwino zimene tinamasulirazo.”
M’bale wina womasulira Chilukonzo ku Uganda anati: “Simungamvetse mmene timasangalalira tikakhala pa misonkhano imene ikuchitika m’chinenero chimene timamasulira. Timasangalalanso kwambiri tikakhala mu utumiki chifukwa chakuti tsopano timalankhula ndi anthu m’chinenero chathu.”
Abale m’mipingo imene omasulirawo amatumizidwa amapindulanso kwambiri. Mwachitsanzo, ponena za omasulira a Chimaya, mlongo wina anati: “Omasulirawa amatilimbikitsa chifukwa cha chitsanzo chawo chabwino komanso chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva. Timangoona ngati tikusonkhana ndi mbali ina ya banja la Beteli, ndipo zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri.”
Abale ndi alongo omasulira mabuku m’Chiluo ku Kisumu, m’dziko la Kenya
Nawonso omasulirawo amalimbikitsidwa. Mwachitsanzo, womasulira wina ku Kenya ananena kuti: “Popeza kuti pali mabuku ochepa kwambiri a chinenero cha Chiluo, anthu kuno sankaganiza kuti angaone mabuku abwino chonchi a m’chinenero chawo. Choncho anthu ambiri amasangalala kwambiri akalandira mabuku athu. Ndikaona zimenezi, ndimalimbikitsidwa kwambiri ndipo zimandipatsa mphamvu kuti ndipitirize utumiki wanga komanso kuti ndizilimbikira.”
Ambiri mwa omasulira amenewa ndi oti atumikira zaka zambiri pa ofesi ya nthambi. Timayamikira kwambiri chitsanzo chawo chabwino komanso mtima wawo wofunitsitsa kuika patsogolo zofuna za nkhosa za Yehova m’malo mwa zofuna zawo, ndipo Mulungu akuwadalitsa chifukwa cha mtima umenewu. Womasulira wina wa Chikhosa ku South Africa anafotokoza mwachidule mmene omasulira ambiri amaonera nkhaniyi. Iye anati: “Bungwe Lolamulira linaganiza bwino kwambiri ponena kuti omasulira asamukire kumadera amene chinenero chawo chimalankhulidwa. Tinkasangalala ku Beteli, koma tikusangalala kwambiri kugwira ntchito kudera limene chinenero chathu chimalankhulidwa.”
Malipoti Apadera Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana
“Abale Anatisamalira Bwino Kwambiri”
Lamlungu pa June 3, 2012, m’dziko la Nigeria munachitika ngozi yoopsa kwambiri ya ndege. Ndege imene inanyamula anthu 153 inagwera m’dera lina lokhala anthu ambiri mumzinda waukulu wa Lagos, ndipo anthu onse amene anali m’ndegemo anafa, kuphatikizapo anthu enanso amene anali pansi.
Lagos, Nigeria: Kutachitika ngozi ya ndenge
Collins Eweh ndi banja lake ankakhala m’chipinda cham’mwamba cha nyumba ya nsanjika zitatu imene inawombedwa ndi ndegeyo. Pamene ngoziyi inkachitika, n’kuti banjali lili ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu.
Cha m’ma 3:35 madzulo, pa nthawi ya Phunziro la Nsanja ya Olonda Collins ndi mkazi wake Chinyere, anaona kuti anthu ambirimbiri akuwaimbira mafoni, koma iwo sanayankhe. Ndiyeno misonkhano itangotha, Chinyere anayankha foni yake ndipo aneba awo anamuuza kuti nyumba yawo ikuyaka. Choncho iwo atanyamuka n’kufika kunyumbako, anaona kuti ndege inagunda nyumba yawo n’kukagwera panyumba ina yapafupi ndipo ndegeyo inayakiratu.
Chinyere ananena kuti: “Tikanakhala kuti tinali panyumba bwenzi titafa ndithu. Ngoziyi itachitika tinangotsala ndi zovala zimene tinavala ku misonkhano basi, koma tikusangalala kuti tili ndi moyo. Izi zitachitika, nthawi yomweyo woyang’anira dera anapanga komiti yopereka chithandizo ndipo tikuyamikira kwambiri chifukwa abale anatisamalira bwino.”
Collins ananena kuti: “Achibale anga amene ankanditsutsa nditakhala Mboni tsopano asintha maganizo awo. Mwachitsanzo, wachibale wanga wina anandiuza kuti: ‘Yehova wako amayankha mapemphero. Usasiye kutumikira Mulungu wako chifukwa amakuthandiza.’ Munthu wina anati: ‘Pitiriza kuchita ndi mtima wonse, chilichonse chimene wakhala ukuchita potumikira Mulungu.’ Tadzionera tokha kuti Yehova amathandizadi anthu ake, ndipo ndikusangalala kwambiri.”
Nyumba ya Malamulo Inavomereza Lamulo Lokhudza Zipembedzo
Budapest, Hungary: Abale athu amalalikira kwa alendo kulikonse kumene angapezeke
Pa February 27, 2012, boma la Hungary linavomereza mbali ina ya Lamulo la Matchalitchi imene inachititsa kuti boma liziona Mboni za Yehova kuti ndi chipembedzo chovomerezeka m’dzikolo. Lamulo limeneli lithandiza kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ipite patsogolo ku Hungary. Komanso lithandiza kuti Mboni za Yehova zisamapereke msonkho pa zinthu zokhudzana ndi kulambira kwathu. Lithandizanso kuti abale azilandira zopereka komanso kuti azikalalikira kundende ndi m’zipatala.
Unali Mwambo Wapadera wa Chikumbutso
Mpainiya wina wapadera wa ku Rundu, m’dziko la Namibia, ananena za mwambo wa Chikumbutso umene unachitikira m’mudzi wina wapafupi. Abale anaona kuti kuderali kuli anthu ambiri achidwi, choncho anaganiza zochita mwambo wa Chikumbutso m’chinenero chawo cha Chirumanyo kwa nthawi yoyamba. Iye analemba kuti: “Malowo ankaoneka bwino kwambiri, chifukwa tinachitira panja mwezi ukuwala, komanso panali nyale za palafini ndi mababu awiri oyendera batire.” Anthuwo ankangoona kuti ali pafupi ndi Yehova. Ngakhale kuti kuderali kuli wofalitsa mmodzi yekha amene anayamba kulalikira m’mwezi wa March, pa Chikumbutsochi panafika anthu 275.
Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi Umalemekeza Yehova
Deti la November 19, 2011, ndi losaiwalika m’mbiri ya gulu la Yehova ku Central African Republic ndi ku Chad. Pa tsiku limeneli abale ndi alongo okwana 269 anasonkhana kutsogolo kwa ofesi yawo ya nthambi yatsopano. Zinali zosangalatsa kwambiri kukhala ndi M’bale Samuel Herd, wa m’Bungwe Lolamulira, amene anakamba nkhani yoperekera nyumba ya Beteli kwa Yehova kuti izigwiritsidwa ntchito pomutumikira. Pulogalamuyi ili mkati, m’bale wina anafotokoza mmene ntchito yolalikira m’mayiko awiriwa inayambira. Ku Central African Republic, ntchitoyi inayamba mu 1947 ndipo ku Chad inayamba mu 1959. Nkhani yotsatira inafotokoza mwatsatanetsatane mmene ntchito yomanga nyumbazi inayendera. Pambuyo pake abale analandira moni wochokera m’mayiko osiyanasiyana, ndipo kenako anasangalala ndi nkhani yotsegulira nyumbazi imene M’bale Herd anakamba. Abale ndi alongo okwana 42 amene akutumikira pa Beteli anasangalala chifukwa tsopano anapeza zimene ankafuna, monga maofesi 8 a abale ndi alongo omasulira mabuku, khitchini, chipinda chodyera ndi malo ochapira zovala. Tsopano zinthu zikuyenda bwino kwambiri ku Beteli, chifukwa panopa kuli zipinda 22 zogona komanso zinthu zina monga, malo ofikira alendo, maofesi ena ndi nyumba yosungira mabuku.
Unali mwambo woyamba wotsegulira ofesi ya nthambi m’dziko la Congo
M’bale Jackson akukamba nkhani yotsegulira ofesi ya nthambi ku Kinshasa, m’dziko la Congo
Loweruka, pa May 26, 2012, linali tsiku lapadera kwambiri kwa Mboni za Yehova za ku Congo (Kinshasa). Abale m’dzikoli atagwira ntchito yomanga ndi kukonzanso ofesi ya nthambi kwa zaka 8, anasangalala kuipereka kwa Mulungu. Mwambo umenewu unali wapadera chifukwa chakuti unali mwambo woyamba wotsegulira ofesi ya nthambi m’dzikoli, ngakhale kuti ofesiyi yakhala ikugwira ntchito m’dzikoli kwa zaka pafupifupi 50. Ku mwambowu kunafika M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira amene anakamba nkhani yotsegulira ofesi ya nthambi. Pa mwambowu panali anthu 2,422, ndipo ambiri a iwo ndi amene anakwanitsa zaka zoposa 40 kuchokera pamene anabatizidwa. Ku mwambowu kunafikanso alendo 117 ochokera m’mayiko 23. Amishonale ena amene anatumikirapo m’dziko la Congo m’mbuyomu anafotokoza zimene ankakumana nazo mu utumiki. Anthu onse pa mwambowu anasangalala kwambiri ndipo analonjeza kuti agwiritsa ntchito nyumbazi pa ntchito yokhudzana ndi kulambira Yehova basi.
Lipoti la Milandu
Pa June 30, 2011, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula kuti boma la France linaphwanya ufulu wa Mboni za Yehova. Bomali linaphwanya ufuluwu pamene linalamula kuti a Mboni za Yehovawo azipereka msonkho wa 60 peresenti pa zopereka zonse zimene anali kulandira kuyambira mu 1993 mpaka mu 1996. Ngakhale kuti khotili linapempha magulu awiriwa kuti athetse nkhaniyi mwamtendere, boma la France linapitirizabe kunena kuti msonkhowo unali wovomerezeka. Choncho sizinatheke kuthetsa nkhaniyi mwamtendere. Ndiyeno pa July 5, 2012, Khotilo linalamula boma la France kuti libweze ndalama zonse zimene a Mboni za Yehova anawononga chifukwa cha msonkhowo. Izi zikutanthauza kuti boma la France likufunika kubweza ndalama zokwana mayuro 4,590,295 (zomwe ndi madola 5,749,440 a ku America) zimene a Mboni anapereka monga msonkho kuchokera pamene anayamba kupereka msonkhowu. Kuwonjezera pamenepa, bomali likufunikanso kupereka chiwongoladzanja cha ndalama zimenezi. Komanso likufunika kupereka ndalama zina zokwana mayuro 55,000 (zomwe ndi madola 68,890 a ku America) pobweza ndalama zimene a Mboni anawononga pa mlanduwu.
Atumiki okhulupirika a Yehova ku Eritrea alandidwa ufulu wawo wokhala nzika za dzikolo chifukwa chosalowerera ndale. (Yes. 2:4) Pa zaka 17 zapitazi, atumiki a Yehova ambiri amangidwa, ndipo panopa abale ndi alongo pafupifupi 50 kuphatikizapo alongo achikulire ndi ana aang’ono ngakhale a zaka ziwiri, ali m’ndende. Chomvetsa chisoni n’chakuti mu July 2011, M’bale Misghina Gebretinsae anakhala munthu woyamba wa Mboni kumwalira m’ndende za ku Eritrea. M’baleyu asanamwalire, anamuika yekhayekha m’chikontena chachitsulo kwa mlungu wathunthu. Koma zikuoneka kuti chimene chinamupha sichikudziwika. Abale athu akuyesetsabe kukumana ndi akuluakulu a boma kuti awathandize kumvetsa kuti tikamachita zinthu mwamtendere komanso kupewa kulowerera ndale, sizitanthauza kuti sitilemekeza boma la Eritrea.
India: M’bale waima panja pa khoti asanamutenge kupita kundende
Magulu a anthu achiwawa amazunza a Mboni za Yehova ku India pamene ali mu utumiki. Mwachitsanzo, abale, alongo, ana, ngakhalenso mlongo wachikulire wazaka 60 komanso mwana wa miyezi 18, aneneredwapo zachipongwe komanso kumenyedwa. Ena avulidwapo zovala komanso kuwopsezedwa kuti awapha. Popeza kuti apolisi amangoyang’ana osachita chilichonse komanso amadana ndi Mboni za Yehova, zachititsa kuti a Mboniwo azingozunzidwabe. M’malo moti apolisi amange anthu amene amazunza Mboniwo, iwo amagwira a Mboniwo n’kuwaimba milandu yabodza. Kawirikawiri omangidwawo amawauza kuti alipire ndalama zambiri kuti awatulutse pa belo. Komanso apolisi amawanenera mawu achipongwe ndi kuwamenya ndiponso amakana kuwapatsa mankhwala, chakudya ndi madzi. Kenako, iwo amakhala m’ndende kwa nthawi yaitali pa mlandu womwe sanapalamule akudikirira chigamulo chosonyeza kuti sanalakwe. Abale athu akhala akupereka madandaulo ku Bungwe Loona za Ufulu Wachibadwidwe m’dzikolo pofuna kuti liwathandize pa mavuto amenewa.
Turkey: M’bale Feti Demirta akupitirizabe kulalikira mwakhama ngakhale kuti anakumana ndi mavuto
Mu November 2011, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, linagwirizana kuti dziko la Turkey linaphwanya ufulu wachibadwidwe wokhudza chikumbumtima cha a Yunus Erçep. A Erçep ndi a Mboni za Yehova ndipo anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali malinga ndi chikumbumtima chawo. Kuyambira mu March 1998, M’bale Erçep wakhala akuitanidwa maulendo okwana 39 kuti akayambe usilikali ndipo wakhala akumangidwa maulendo oposa 30. M’bale Erçep wakhala akulipiritsidwa ndalama, kumangidwa ndi kupititsidwa kuchipatala cha anthu amisala pomuganizira kuti wachita misala.
Mu October 2004, M’bale Erçep anakasuma mlandu wake ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya. Poweruza mlanduwo, Khotilo linanena kuti, “wodandaulayu, amene ndi wa Mboni za Yehova, sakufuna kukalowa usilikali chifukwa cha zimene amakhulupirira ku chipembedzo chake osati kungokana kuti azigwira ntchito zina zofuna kutukula moyo wake.”
M’bale winanso amene anakana kukaphunzira usilikali ataitanidwa ndi boma la Turkey mu 2005 ndi Feti Demirtaş. M’baleyu anamangidwa, kumenyedwa, kuimbidwa mlandu ndi kutsekeredwa m’ndende kwa masiku 554, ndipo anatulutsidwa mu June 2007. Popeza kuti M’bale Demirtaş sanalole kusintha maganizo ake pa zimene amakhulupirira kuchokera m’Baibulo, aboma analemba chikalata chosonyeza kuti m’baleyu akudwala misala. Pogamula mlanduwu, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linapeza kuti boma la Turkey linazunza kwambiri M’bale Demirtaş ndiponso linamuphwanyira ufulu wake wokhudza chikumbumtima.
Zigamulo ziwiri zomwe tafotokoza pamwambazi zinatsatana ndi chigamulo chosaiwalika chimene chinaperekedwa ndi Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya pa July 2011, pa mlandu wapakati pa a Bayatyan ndi dziko la Armenia. Pa mlandu umenewu, akuluakulu a Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya anatsimikizira kuti pangano la mayiko a ku Ulaya limateteza ufulu wa anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Mayiko onse amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya, kuphatikizapo dziko la Turkey, akuyenera kutsatira lamulo limeneli.
Mu January 2012, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamulanso kuti dziko la Armenia linali lolakwa pa mlandu wapakati pa bomalo ndi a Bukharatyan komanso a Tsaturyan. Chigamulo chimenechi chinatsimikizira kuti bomali linkaphwanya ufulu wa kulambira wa anthu awiri a Mboni za Yehova amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Popereka chigamulochi, Khotilo linatchula za chigamulo chimene linapereka pa mlandu wa pakati pa a Bayatyan ndi boma la Armenia.
Ngakhale kuti Khotili linagamula kuti dziko la Armenia linali lolakwa, boma la dzikoli likupitirizabe kumanga ndi kuika m’ndende anthu amene chikumbumtima chawo sichikuwalola kulowa usilikali. Boma la Armenia linavomereza mu March 2012 kuti anthu amene sangagwire ntchito ya usilikali azigwira ntchito zina. Koma nyumba ya malamulo sinakambiranebe lamulo limeneli. Tikuyembekezera kuti boma la Armenia litsatira chigamulo cha Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya ndipo litulutsa m’ndende abale athu amene anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali.
Boma la Azerbaijan likupitirizabe kuzunza Mboni za Yehova. Bomali likumafufuza m’nyumba za abale, kuwamanga chifukwa chochita misonkhano yachikhristu, kufufuza m’mabuku athu kuti aone ngati mulibe zokayikitsa ndiponso akumathamangitsa abale ndi alongo ochokera kumayiko ena. Komanso apolisi akumamenya abale ndi alongo ndi kuwanenera mawu achipongwe ndiponso kuwaopseza kuti afafaniza chipembedzo chawo m’kaundula waboma. Bungwe lina laboma loona za zipembedzo linakana kulembanso m’kaundula Mboni za Yehova, choncho apolisi akupitiriza kusokoneza ulaliki ndi misonkhano imene Mboni zimachita mwamtendere. Komanso aika malamulo okhwima okhudza kuitanitsa mabuku ndi kuwafalitsa m’dzikolo. Makhoti akulamula kuti a Mboni za Yehova azilipira chindapusa chokwera chifukwa chofalitsa mabuku achipembedzo komanso kuchita misonkhano yachikhristu. Mwachitsanzo, mlongo wina anamulamula kuti apereke chindapusa cha ndalama zokwana madola 1,909 a ku America chifukwa chopita ku msonkhano mu mzinda wa Ganja. Popeza kuti zimenezi zimaphwanya ufulu wolambira momasuka womwe uli m’Pangano Lokhudza Ufulu wa Anthu ku Ulaya, tapempha mobwerezabwereza ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya kuti atithandize kuthetsa nkhanza zimene boma la Azerbaijan likuchitira Mboni za Yehova.
Akuluakulu aboma m’madera osiyanasiyana m’dziko la Russia akupitiriza kuzunza Mboni za Yehova. Iwo amakakamiza makhoti kuti apereke chilango kwa Mboni chifukwa chogwiritsa ntchito ufulu wawo wolambira Mulungu. Pogwiritsa ntchito lamulo loletsa kuchita zinthu monyanyira limene anthu ambiri amadana nalo, makhoti a ku Russia anagamula kuti mabuku pafupifupi 64 a Mboni za Yehova ndi olimbikitsa kuchita zinthu monyanyira. Posachedwapa, woweruza wina anapempha khoti kuti ligamule zoti buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, limene timaphunzitsira ana za Yesu Khristu, ndi lophunzitsa anthu kuchita zinthu monyanyira. M’madera ambiri ku Russia, makhoti anatseka Webusaiti ya Mboni za Yehova. Makhotiwo anaperekanso chilolezo kwa akuluakulu aboma kuti azifufuza mwachinsinsi zochita za abale ndi alongo, komanso aziwajambula pavidiyo ndi kuwerenga makalata awo. Choncho apolisi amafunsa anthu ena odana ndi Mboni kuti amve maganizo awo pa nkhani ya Mbonizo, amafufuza m’nyumba za Mbonizo, amawalanda mabuku ndiponso katundu wawo. Nthawi zina a Mboni amagwidwa akungodziyendera mumsewu, akuyendetsa galimoto yawo kapena akamatsika sitima. Apolisi akhala akusokoneza misonkhano yachikhristu komanso kumanga akulu chifukwa chogwira ntchito yoweta nkhosa mu mpingo. M’madera ena anthu odana ndi Mboni akufuna kupempha a khoti kuti athetse mabungwe amene Mboni za Yehova m’maderawo zinalembetsa ku boma.
Mu May 2012, Mboni zokwana 17 mu mzinda wa Taganrog zinaimbidwa mlandu wochita zinthu zophwanya malamulo chifukwa chakuti ankachita zinthu zokhudza chikhulupiriro chawo. Mu mzinda umenewo khoti linalamula kuti bungwe la Mboni za Yehova lithe. Zimenezi zinachitika mu 2009 ndipo Nyumba ya Ufumu inalandidwa ponena kuti m’nyumbayi anthu ankaphunzira kuchita zinthu monyanyira. Chifukwa choti analetsedwa kugwiritsa ntchito Nyumba yawo ya Ufumu, a Mboni anayamba kusonkhana m’nyumba zawo kapena kupeza nyumba za lendi kuti azipangira misonkhano. Koma panopa akuluakulu aboma akufuna kuletsa kuti anthu onse asamakumane pamodzi n’kumapemphera. Mu July 2012, m’bale wina ndi mkazi wake, omwe akuchita upainiya mu mzinda wa Chita ku Siberia, anaimbidwa mlandu wochititsa kuti anthu azidana chifukwa choti ankagawa buku lophunzirira Baibulo lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? limene ena amanena kuti limaphunzitsa anthu kuchita zinthu monyanyira. Aliyense anamulamula kuti akagwire ntchito yakalavulagaga kwa maola 200, koma iwo anachita apilo mlandu umenewu.
Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linagamula milandu iwiri mokomera Mboni za Yehova ku Russia. Mlandu woyamba unali wa pakati pa boma la Russia ndi a Kuznetsov komanso anthu ena mu 2007, ndipo wachiwiri unali wa pakati pa Mboni za Yehova za ku Moscow ndi boma la Russia mu 2010. Ngakhale zili choncho, akuluakulu a boma la Russia akupitiriza kunyalanyaza zigamulo zimene Khoti lalikululi linapereka. Panopa, a Mboni za Yehova anakasuma milandu ina 19 ku khotili ndipo akuyembekezera kuti zigamulo zimene khotili lidzapereke zidzachititsa kuti boma la Russia lisiye kuzunza anthu a Yehova. Komanso akuyembekezera kuti zigamulozo zidzachititsa kuti bomali lilole a Mboniwo ‘kukhala ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti akhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso akhale oganiza bwino.’—1 Tim. 2:2.
Boma la South Korea likupitirizabe kumanga abale achinyamata chifukwa chokana kulowa usilikali. Mwezi uliwonse, abale achinyamata pafupifupi 45 amamangidwa n’kuwalamula kuti akhale m’ndende chaka chimodzi ndi hafu. Zimenezi zachititsa kuti abale pafupifupi 750 akhale m’ndende ku Korea. Chimenechi ndi chiwerengero chachikulu kwambiri cha Mboni za Yehova zomwe zili m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo kuposa dziko lililonse padziko lapansi. Tikawonkhetsa zaka zonse zimene Mboni za Yehova zokwana 17,000 zalamulidwa kukhala m’ndende kuyambira mu 1950, zikuposa zaka 32,000.
Mu 2012, akuluakulu a boma m’dzikoli anawirikiza kuzunza a Mboni amene akukana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Mwachitsanzo, kwa nthawi yoyamba iwo anamanga anthu amene anakana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo anthuwo atakananso kukaphunzira za usilikali kuti aziitanidwa pa nthawi imene afunika. M’mbuyomu anthu amene akana kukaphunzira za usilikali kuti aziitanidwa pa nthawi imene afunika, ankangowalipiritsa chindapusa. Popeza kuti pakufunika anthu ambiri oti akaphunzire za usilikali kuti aziitanidwa pa nthawi imene afunika, anthu amene akukana kupita kumaphunziro amenewa akumaimbidwa mlandu mobwerezabwereza. Mwachitsanzo mu November 2011, Ho-jeong Son anamulamula kuti akakhale m’ndende kwa miyezi 8. Kenako, mu June 2012, anamuimbanso mlandu ndipo pa nthawiyi anamulamula kukakhala m’ndende kwa miyezi 6. Atagamula mlandu umenewu anamumanga nthawi yomweyo ndipo anam’tulutsa pa belo patatha masiku 29. Panopa akuyembekezera kupitanso kukhoti chifukwa anachita apilo mlanduwo. Ngati angamulamule kuti akakhale m’ndende, ndiye kuti miyezi yonse pamodzi idzakwana 14.
Ku South Korea, mwezi uliwonse abale achinyamata pafupifupi 45 amamangidwa ndi kuwalamula kuti akakhale m’ndende kwa chaka chimodzi ndi hafu
Maulendo angapo, Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu inadzudzula boma la South Korea chifukwa chophwanya ufulu wa anthu wochita zinthu motsatira chikumbumtima chawo. Pofuna kuthetsa nkhaniyi, panopa abale anthu m’dzikoli anakatula madandaulo awo ku Komitiyi komanso ku Khoti Loona za Malamulo a Dziko la South Korea.