Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 28-tsamba 29 ndime 1
  • Mwambo Wotsegulira Ofesi ya Nthambi ku Sri Lanka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwambo Wotsegulira Ofesi ya Nthambi ku Sri Lanka
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Nkhani Yofanana
  • M’bale Watsopano M’Bungwe Lolamulira
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Maphunziro Amene Ndikupitirizabe Mpaka Pano
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017
  • Mwambo Wotsegulira Maofesi a Nthambi
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 28-tsamba 29 ndime 1
Chithunzi patsamba 28

ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Mwambo Wotsegulira Ofesi ya Nthambi ku Sri Lanka

Mapu patsamba 29

ABALE ndi alongo a ku Sri Lanka anavala zovala za kwawoko n’kukalandira alendo 130 ochokera m’mayiko 19. Alendowo anadzakhala nawo pa mwambo wotsegulira nthambi pachilumba chokongolachi. Panali ana amene anaimba nyimbo za Ufumu. Abale ndi alongo ankacheza, kuchita masewero, kudya ndiponso kumvetsera nyimbo zosangalatsa.

Loweruka pa January 11, 2014, anatsegulira ofesi ya nthambiyi komanso kuipereka kwa Yehova. Panali anthu okwana 893 ndipo nkhani zake zinkamasuliridwa m’zilankhulo zitatu. M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe lolamulira anafunsa gululo kuti: “Kodi mukufuna kupereka ofesi yatsopanoyi kwa Yehova Mulungu?” Anthuwo anavomera poomba m’manja kwa nthawi yaitali kwambiri.

Tsiku lotsatira, anthu, 7,701 anamvetsera pulogalamuyi ndipo M’bale Sanderson anakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri. Ena mwa anthuwa anasonkhana m’malo ena ndipo ankachita kuonera pulogalamuyi m’masikirini. Kunena zoona abale ndi alongo m’madera osiyanasiyana a chilumbachi anali ndi mwayi woonera pulogalamuyi ndipo ‘anasangalala kwambiri.’ Iwo anaimba nyimbo za Ufumu komanso ankamva pamene anzawo kumalo enawo ankaimba.—Neh. 12:43.

Chithunzi patsamba 29
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena